Olengeza Ufumu Akusimba
Ntchito Zabwino Zimene Zimalemekeza Yehova
MU ULALIKI wake wa pa Phiri, Yesu anati kwa ophunzira ake: “Muwalitse kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Matthew 5:16) Moteronso, Akristu oona lerolino amachita “ntchito zabwino” zimene zimalemekeza Yehova.
Kodi ntchito zabwino zimenezi ndi ziti? Zimaphatikizapo kulalikira uthenga wabwino, koma khalidwe lathu labwino lilinso mbali yofunika kwambiri. Kaŵirikaŵiri ndi khalidwe lathu labwino limene poyamba limakokera anthu kumpingo wachikristu. Zokumana nazo zotsatira zikusonyeza mmene Mboni za Yehova ku Martinique ‘zikuwalitsira kuunika kwawo pamaso pa anthu.’
◻ Pochita ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba, mmodzi wa Mboni za Yehova anapita pa nyumba ya mkazi wachikatolika. Mkazi ameneyu anakhala ndi mwamuna amene sanakwatirane naye kwa zaka 25. Ankadziŵa ziphunzitso za Mboni za Yehova, popeza iyeyo, pafupifupi zaka zisanu ndi ziŵiri pachiyambi, analandira buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.a Mkaziyo anauza Mboniyo kuti: “Pali zipembedzo zochuluka kwambiri. Sindikudziŵa amene ndiyenera kukhulupirira pakati pa msokonezo wonsewu.” Mboniyo inafotokoza kuti choonadi chimapezeka m’Baibulo mokha ndi kuti ngati akufuna kuchipeza, ayenera kuphunzira Malemba mosamala ndi kupemphera kwa Mulungu kaamba ka mzimu wake ndi chitsogozo.
Kwa nthaŵi yaitali, ngakhale kuti anali wokondweretsedwa kuphunzira Baibulo, mkaziyo anakana kangapo chiitano cha kukapezeka pa misonkhano yachikristu pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Chifukwa ninji? Ankachita manyazi kwambiri. Komabe, atalandira chiitano cha kukapezeka pa Chikumbutso cha Imfa ya Kristu, anagonjetsa manyazi ake ndi kupezekapo.
Chimene chinamkondweretsa kwambiri pamsonkhanowo chinali mkhalidwe wachikondi mu Nyumba ya Ufumu. Sanaonepo ubwenzi weniweni wotero kutchalitchi chake! Pambuyo pa msonkhanowo anayamba kupezeka pamisonkhano yonse yochitidwa ndi Mboni zakumaloko, ndipo posapita nthaŵi anakwatirana ndi mwamuna amene ankakhala nayeyo. Tsopano ndi mmodzi wa obatizidwa a mumpingo.
◻ Ntchito zabwino za Mboni ina zinatulutsa zipatso zabwino. Iyo inali ndi thayo lalikulu mu ofesi inayake. Pamene mwamuna wina wa ku Réunion analembedwa ntchito, antchito ena anayamba kumnyodola chifukwa cha kufupika kwake. Anakhala choseketsa. Mosiyana ndi zimenezo, Mboniyo inali yokoma mtima nthaŵi zonse ndi yaulemu kwa mwamunayo. Posapita nthaŵi mwamunayo anayamba kufunsa chifukwa chake mkaziyo anali wosiyana kwambiri ndi ena.
Mboniyo inafotokoza kuti inali ndi khalidwe laulemu chifukwa cha mapulinsipulo a Baibulo amene inaphunzira kuchokera kwa Mboni za Yehova. Inamsonyezanso zimene Malemba amanena ponena za zifuno za Mulungu ndi chiyembekezo cha dziko latsopano. Mwamunayo analandira phunziro la Baibulo, nayamba kupezeka pamisonkhano yachikristu, ndi kukwatira mkazi amene ankakhala naye.
M’kupita kwa nthaŵi anabwerera ku Réunion. Kale, anakhalapo ndi vuto ndi achibale ake, makamaka ndi banja la mkazi wake. Koma tsopano iwo anakondwera kwambiri ndi khalidwe lake labwino lachikristu. Mwamunayo anabatizidwa ndipo tsopano ndi mtumiki wotumikira. Am’banjalo angapo, kuphatikizapo mkazi wake ndi ana ake aakazi aŵiri, nawonso akutumikira mumpingo wachikristu monga ofalitsa a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.