Ambirimbiri Akuwonjezedwa
1 Monga zinalili m’zaka za zana loyamba, chiwonjezeko chimene mpingo wachikristu ukuona lerolino nchodabwitsa. (Mac. 2:41; 4:4) Chaka chatha, ophunzira atsopano 366,579 anabatizidwa, oposa 1,000 tsiku lililonse pa avareji! Oposa miliyoni imodzi anabatizidwa pazaka zitatu zapitazi. Ndithudi, Yehova wapitirizabe kuwonjeza okhulupirira ambirimbiri.—Mac. 5:14.
2 Atsopano ambirimbiriwo amene alibe chidziŵitso pamakhalidwe achikristu afunikira kuthandizidwa ndi kuphunzitsidwa ndi awo olimba m’chikhulupiriro. (Aroma 15:1) Pakati pa Akristu oyambirira, panali ena amene analephera “kutsata ukulu msinkhu” ngakhale zaka zambiri pambuyo pa kubatizidwa. (Aheb. 5:12; 6:1) Ndiye chifukwa chake, m’kalata yake kwa Ahebri, Paulo anatchula mbali zimene Akristu ayenera kukulitsa mwauzimu. Kodi zimenezo ndi ziti, ndipo thandizo lofunikira lingaperekedwe motani?
3 Kukhala ndi Kaphunziridwe Kabwino: Mogwirizana ndi malangizo a Paulo, kukhala wophunzira wabwino kumaphatikizapo kuphunzira mwakhama, kubwerezera, ndi kugwiritsira ntchito “chakudya chotafuna” choperekedwa ndi gulu la Yehova. (Aheb. 5:13, 14; onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1993, masamba 12-17.) Mwa kuloŵetsa okhulupirira atsopano m’nkhani zauzimu ndi kugaŵana nawo ngale za choonadi zimene mwafukula pakufufuza kwanu, mungawasonkhezere kukhala ndi kaphunziridwe kabwino. Mwinamwake nthaŵi zina mungapemphe watsopano kukhala nanu paphunziro lanu laumwini kapena paphunziro la banja.
4 Kupezeka Pamisonkhano Nthaŵi Zonse: Chitsanzo chanu chokhulupirika ndi mawu achikondi olimbikitsa zidzathandiza atsopano mumpingo kupeŵa mbali ina yodetsa nkhaŵa yotchulidwa ndi Paulo imene ena “amachita”—kuphonya misonkhano yachikristu. (Aheb. 10:24, 25) Athandizeni kuzindikira kuti misonkhano ndiyo idzawathandiza kukhala ndi moyo wauzimu mumpingo. Yambani ndinu kuwamasula kuti adzimve kuti alimo mu ubale wathu.
5 Kufikira Yehova Mwachidaliro: Kuti tigonjetse zofooka zathupi ndi za maumunthu, tiyenera kupita kwa Yehova m’pemphero, kumfotokozera zolingalira zathu zazikulu ndi nkhaŵa zathu zazikulu koposa. Atsopano ayenera kuphunzira kuti sayenera kuchita mphwayi popempherera thandizo kwa Yehova, monga anatilimbikitsira Paulo. (Aheb. 4:15, 16; 10:22) Kusimba zokumana nazo zanu pamenepa kudzalimbitsa chidaliro cha watsopano chakuti Yehova amamva mapemphero ochokera pansi pa mtima.
6 Kupatula Nthaŵi Yopita mu Utumiki: Paulo anasonyezanso kuti timalimbitsidwa mwauzimu pamene ‘tipereka chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu.’ (Aheb. 13:15) Kodi simungapemphe wofalitsa watsopano kuti agwirizane nanu pamakonzedwe anu a mlungu ndi mlungu a utumiki wakumunda? Kapena aŵirinu mungakonzekere ulaliki kapena kuyesa mbali ina ya utumiki imene watsopanoyo sanaiyesepo.
7 Ambirimbiriwa amene akuwonjezedwa akutipatsa chimwemwe chachikulu. Kudzipereka kwathu pa kuphunzitsa ndi kulangiza atsopano mumpingo kudzawathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chofunikira kuti ‘apulumutse moyo wawo.’—Aheb. 3:12, 13; 10:39.