Tonse Tingathandize Nawo Kupanga Ophunzira Atsopano
1 Kuti munthu akhale wophunzira watsopano, sizidalira khama la munthu mmodzi yekha ayi. Yehova amagwiritsa ntchito “antchito anzake” onse kuti athandize ophunzira Baibulo kukula mwauzimu. (1 Akor. 3:6-9) Aliyense wa ife amathandiza atsopano osati chabe ndi ndemanga zathu zogwira mtima pamisonkhano yachikhristu, komanso ndi khalidwe lathu labwino. Khalidwe labwino ndi umboni wakuti mzimu wa Mulungu uli pa ife. (Yoh. 13:35; Agal. 5:22, 23; Aef. 4:22, 23) N’chiyaninso china chimene tingachite kuti tithandize atsopano?
2 Zimene Mpingo Ungachite: Tonsefe tingasonyeze chidwi kwa anthu amene angoyamba kumene kubwera ku misonkhano mwa kuwapatsa moni mosangalala ndi kucheza nawo misonkhano isanayambe ndiponso itatha. Pokumbukira tsiku loyamba limene anapita ku mpingo, mwamuna wina anati: “Tsiku limenelo ndinakumana ndi anthu osawadziwa koma achikondi kuposa aliyense amene ndinakumanapo naye kutchalitchi kumene ndakulirako. Zinali zoonekeratu kuti ndapeza choonadi.” Munthuyu anabatizidwa patangodutsa miyezi 7 yokha kuchokera pamene anapita ku msonkhano woyamba.
3 Wophunzira Baibulo akamapita patsogolo mwauzimu, muyamikireni ndi mtima wonse. Kodi iye wakhala akupirira anthu akamamutsutsa? Kodi amabwera ku misokhano nthawi zonse? Kodi analimba mtima kuyankha? Kodi walembetsa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kapena wayamba kupita nawo muutumiki? Muyamikireni. Zimenezi zidzamusangalatsa ndi kumulimbikitsa.—Miy. 25:11.
4 Zimene Mwini Wake wa Phunziro Angachite: Ofalitsa ena athandiza ophunzira Baibulo awo kudziwana ndi anthu a mumpingo mwawo mwa kupita ku phunzirolo ndi ofalitsa osiyanasiyana achitsanzo chabwino. Itanirani munthuyo kumisonkhano ya mpingo mwamsanga atangoyamba kuphunzira. Akayamba kufika pa misonkhano, onetsetsani kuti adziwane ndi ena. Kodi akuvutika kusiya chizolowezi choipa, monga kusuta fodya? Kodi kapena pali winawake kunyumba kwawo amene akumuletsa kuphunzira? Angathandizidwe ngati atalankhulana ndi wofalitsa amene anakumanapo ndi vuto ngati lakelo.—1 Pet. 5:9.
5 Atsopano amafunikira kuthandizidwa ndi mpingo kuti achite bwino mwauzimu. Tonsefe tingawathandize kupita patsogolo mwa kuwasonyeza kuti tili ndi chidwi chofuna kuwathandiza.