Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi brosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? June: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Sumikani maganizo pa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Lililonse la mabrosha a masamba 32 otsatirawa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha!
◼ Aja amene amagwirizana ndi mpingo uliwonse ayenera kutumiza masabusikripishoni onse atsopano ndi olembetsanso a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ngakhale masabusikripishoni aumwini, kudzera mu mpingo.
◼ Sosaite siisamalira kufunsira mabuku kwa wofalitsa aliyense payekha. Woyang’anira wotsogoza ayenera kulinganiza kuti chilengezo chiziperekedwa mwezi uliwonse oda ya mabuku ya mpingo ya mwezi ndi mwezi isanatumizidwe ku Sosaite kotero kuti onse omwe angafune mabuku aumwini auze mbale wosamalira mabuku. Chonde kumbukirani kuti ndi mabuku ati a oda yapadera.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:
Watch Tower Publications Index 1986-1995 (K8,250.00 ofalitsa ndi K6,000.00 apainiya)—Chingelezi