Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa January 6 kufikira April 21, 1996. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Kunyada kungatichititse kusavomereza zolakwa zathu ndi kukana uphungu. [rs-CN tsa. 325 ndime 1]
2. Palibe aliyense padziko lapansi amene anali ndi mphamvu ya kukhululukira machimo mpaka pamene Yesu anafa ndi kupereka dipo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 4/15 tsa. 29]
3. Kubatizidwa m’dzina la Atate kumatanthauza kuti tikuzindikira kuti Yehova ndiye Mulungu woona, Mlengi ndi Mfumu yachilengedwe chonse. [uw-CN tsa. 98 ndime 9]
4. Ubatizo uli chitsimikizo cha chipulumutso. [uw-CN tsa. 100 ndime 12]
5. Sitiyenera kuimba Mulungu mlandu wa “masoka achilengedwe” amene ananenedweratu kuti adzachitika m’tsiku lathu monga momwe opima machedwe sakhala ndi mlandu wa machedwe amene amaneneratu. [rs-CN tsa. 227 ndime 1-3]
6. Machimo onse a anthu opanda ungwiro amafafanizidwa ndi dipo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 12/15 tsa. 29]
7. Pakati pa “mbuzi” zotchulidwa pa Mateyu 25:31-46, zimene zidzadulidwa kwamuyaya, padzakhala anthu okangalika a m’Babulo Wamkulu ndi atsogoleri awo achipembedzo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 10/15 tsa. 26 ndime 13-15]
8. Mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 23:33 amasonyeza kuti alembi ndi Afarisi, monga gulu, anali mbali ya mbewu ya Njoka. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 6/1 tsa. 11 ndime 11]
9. Kukhululukira ena kumatheketsa machimo athu kukhululukidwa ndi Mulungu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 9/15 tsa. 7]
10. Ubatizo wa Yesu mu imfa unayamba mu 29 C.E. ndipo sunatsirizidwe kufikira atafadi ndi kuukitsidwa. [uw-CN tsa. 97 ndime 6]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Kodi Ufumu wa Yesu sudzawonongeka m’lingaliro lotani? (Dan. 7:14) [uw-CN tsa. 86 ndime 15]
12. Kodi anthu akupindula m’njira zotani ndi nsembe ya Yesu panthaŵi ino? [kl-CN tsa. 68-9 ndime 17-19]
13. M’malo mosuliza awo amene tingaganizire kuti angachite zambiri mu utumiki wa Ufumu, kodi tiyenera kuchitanji aliyense payekha? (Agal. 6:4) [uw-CN tsa. 93 ndime 13]
14. Kodi kudula ndodo yotchedwa Chisomo kumene Zekariya anachita kunatanthauzanji? (Zek. 11:7-11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 6/15 tsa. 31]
15. Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanakhululukire Adamu ndi kungoiŵala tchimo lake? [rs-CN tsa. 225 ndime 5]
16. Kodi uchimo unafalikira motani kwa anthu onse? [kl-CN tsa. 58 ndime 13]
17. Kodi munthu angalande motani Mulungu? (Mal. 3:8) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 4/15 tsa. 18 ndime 15]
18. Kodi ndi kuti m’buku la Mateyu kumene timapeza uphungu wabwino kwambiri umene Yesu anapereka wonena za kuthetsa mavuto aakulu? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 7/15 tsa. 22]
19. Kodi “rupiya la theka” lotchulidwa m’fanizo la Yesu lolembedwa pa Mateyu 20:1-16 ndilo chiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani gt-CN 97 ndime 6]
20. Kodi nchifukwa ninji sitinganene kuti Mdyerekezi ndi ziŵanda zake mwachindunji ndiwo amachititsa kuvutika konse kwa anthu? (Miy. 1:30-33; Agal. 6:7) [rs-CN tsa. 222 ndime 4]
Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Monga momwe kwasonyezedwera m’nkhani ya Yobu, Satana amanena kuti ife tili okondweretsedwa kwakukulukulu ndi ․․․․․․․․, kupeza bwino kwathu ndi thanzi lathu la ife eni, ndi kuti cholinga chathu m’kutumikira Mulungu chili ․․․․․․․․. [uw-CN tsa. 93 ndime 13]
22. Ngati munthu amene amati ali ndi mzimu wa Mulungu sabala ․․․․․․․․ za mzimu m’moyo wake ndipo sadzisiyanitsa ndi ․․․․․․․․ ndi machitachita ake, zonena zake zilibe maziko. [rs-CN tsa. 286 ndime 5-8]
23. Akufa otchulidwa pa Chivumbulutso 20:12 adzaweruzidwa malinga ndi zochita zawo za ․․․․․․․․ kuuka kwawo. Zimenezi zikutithandiza kuzindikira kuti kuuka kwawo sikudzangokhala kuuka kwa ․․․․․․․․. (Yoh. 5:28, 29) [uw-CN tsa. 75 ndime 12]
24. Ngakhale kuti Yesu sanampatsedi dzina laumwini la ․․․․․․․․, ntchito yake monga munthu inakwaniritsa ․․․․․․․․ la dzinalo. (Yes. 7:14; Mat. 1:22, 23) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 1/15 tsa. 22]
25. Chifukwa cha kulingalira ․․․․․․․․ amene amamtumikira mokhulupirika, Mulungu amaona ․․․․․․․․ awo aang’ono monga ․․․․․․․․. (1 Akor. 7:14) [rs-CN tsa. 226 ndime 4]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Yesu anakhala Mesiya pa (kubadwa kwake, kubatizidwa kwake, kuuka kwake), kumene kunachitika m’chaka cha (2 B.C.E.; 29 C.E.; 33 C.E.). [kl-CN tsa. 65 ndime 12]
27. Ochuluka a (otsalira; a 144,000) ali kumwamba, ndipo (otsalira; a 144,000), amene akali padziko lapansi, amapanga (Bungwe Lolamulira; kapolo wokhulupirika ndi wanzeru). [uw-CN tsa. 80 ndime 7]
28. Mlaliki 9:11 amatithandiza kudziŵa kuti kaŵirikaŵiri anthu amavulala ndi kuvutika chifukwa cha (Mdyerekezi; anthu oipa; ngozi, kukhala pamalo osayenera nthaŵi yolakwika). [rs-CN tsa. 223 ndime 3]
29. Ubatizo “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera” unayamba mu (29 C.E.; 33 C.E.; 36 C.E.). (Mat. 28:19) [uw-CN tsa. 98 ndime 9]
30. Mphotho imene Yesu analonjeza kwa awo olandira ophunzira ake monga aneneri, malinga ndi Mateyu 10:41, ndiyo (moyo wosatha; chitetezo cha Mulungu; kumva uthenga wa Ufumu). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 1/1 tsa. 24]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Zek. 4:6; Mat. 4:8-10; Mat. 16:19; Afil. 1:9-11; Aheb. 13:5, 6
31. Tiyenera kugwiritsira ntchito moyo wathu m’njira imene imasonyeza kuti timadziŵadi zimene zili zinthu zofunika koposa. [uw-CN tsa. 91 ndime 9]
32. Otsatira oona a Yesu amakana kuloŵa m’nkhani zandale za dzikoli. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 5/1 tsa. 12 ndime 9]
33. Chidziŵitso cha Ufumu wa Mulungu chinali kudzatsegulira Ayuda, Asamariya, ndi Akunja njira yakumwamba. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 3/15 tsa. 5]
34. Chitsutso cha padziko lonse cha ntchito yathu ya kulalikira chagonjetsedwa ndi chitsogozo cha Yehova ndi chitetezo chake, osati ndi zoyesayesa za anthu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 8/15 tsa. 17 ndime 4]
35. Mosasamala kanthu za kukwera kwa mitengo ndi kufala kwa ulova, Yehova adzatsimikizira kuti tili ndi zimene tifunikiradi. [uw-CN tsa. 89 ndime 6]
S-97-CN Zam, Mal & Moz #291b 4/97