Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu August: Lililonse la mabrosha a masamba 32 otsatirawa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. October: Makope a Galamukani! ndi a Nsanja ya Olonda. Mutapeza ochita chidwi pamaulendo obwereza, mungagaŵire masabusikripishoni. Kuyambira chakumapeto kwa mweziwu, tidzagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35. November: Tidzapitiriza kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35. Mipingo imene iti itsirize kufola gawo lawo mwa kufikira eni nyumba panyumba iliyonse ingagaŵire buku la Chidziŵitso.
◼ M’dera lililonse panthaŵi zosiyanasiyana pachaka, pamakhala maholide adziko amene amapatsa ana mpata wopuma kusukulu ndi nthaŵi yopuma pantchito yadziko. Maholide ameneŵa amapatsa mipingo mipata yabwino yoti awonjezere kugwira ntchito mu utumiki wakumunda. Akulu ayenera kudziŵa kuti zochitika zimenezi zidzakhalako liti ndi kudziŵitsa mpingo pasadakhale ndi kukonza zoti adzachitire umboni monga gulu pamaholide ameneŵa.
◼ Mafomu okwanira ogwiritsira ntchito m’chaka cha utumiki cha 1998 akutumizidwa kumpingo uliwonse. Chonde agwiritsireni ntchito mafomu ameneŵa mosamala. Muwagwiritsire ntchito pantchito yake yokhayo.
◼ Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Mlembi wa mpingo akumane ndi mtumiki wamabuku kuchiyambi kwa August ndipo asankhe deti pamene adzawerengera sitoko ya mabuku a mpingo kumapeto kwa mwezi. Mabuku onse amene ali m’sitoko aŵerengedwe ndithu, ndipo ziŵerengero zimene awonkhetsazo azilembe pafomu ya Kuŵerengera Mabuku. Magazini onse amene alipo angapezeke kwa mtumiki wamagazini. Chonde tumizani ku Sosaite kope loyambalo September 6 asanafike. Sungani kope lakaboni m’faelo mwanu. Kope lachitatu mungaligwiritsire ntchito monga poŵerengera. Mlembi ayenera kuyang’anira kuŵerengerako, ndipo woyang’anira wotsogoza aipende fomu yodzazidwayo. Mlembi ndi woyang’anira wotsogoza ndiwo adzasaina fomuyo.
◼ Mipingo ingayambe kuoda Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1998 pafomu yawo yoodera mabuku m’September. Makalendawo adzakhalako m’Chicheŵa ndi Chingelezi.