Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/97 tsamba 5-6
  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 8/97 tsamba 5-6

Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa May 8 kufikira August 18, 1997. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Chifundo cha Yesu, chosonyezedwa pa Marko 1:41, chimapereka chithunzi chogwira mtima chakuti Yehova amasamala anthu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 3/1 tsa. 5.]

2. Chivumbulutso 7:16 chimasonyeza kuti a khamu lalikulu sadzakumana ndi chizunzo m’dzikoli. [uw-CN tsa. 108 ndime 11]

3. Funso la Yohane Mbatizi pa Luka 7:19 limasonyeza kuti iye analibe chikhulupiriro. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 7/15 tsa. 8.]

4. Pa Paskha womaliza wa Yesu ndi ophunzira ake, Petro ndiye yekha yemwe anati kwa iye: “Sindidzakukanani Inu iyayi.” [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu]

5. Palibe umboni uliwonse wa m’Baibulo wosonyeza kuti mtumwi Petro anali wokwatira. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu]

6. Kulibe m’Malemba pamene mzimu woyera umatchulidwa ndi dzina. [rs-CN tsa. 393 ndime 2]

7. Zochitika za masiku otsiriza zili chabe pa Mateyu 24, Marko 13, ndi Luka 21. [kl-CN tsa. 102 bokosi]

8. Malinga ndi Yohane 20:17, Yesu anatcha Yehova “Mulungu wanga,” koma palibe m’Malemba pamene Yehova anatcha Yesu kapena mzimu woyera kuti “Mulungu wanga,” ndiponso Yehova ndi Yesu sanautchepo mzimu woyera kuti “Mulungu wanga.” [rs-CN tsa. 398 ndime 2]

9. Ufumu umene Yesu analalikira unali wochepa, kapena wachiŵiri kwa ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Mulungu. [kl-CN tsa. 91 ndime 4]

10. Palibe malemba m’Baibulo amene amatchula mikhalidwe imene a khamu lalikulu ayenera kusonyeza kuti adzapulumuke pa Armagedo. [uw-CN tsa. 105 ndime 5]

Yankhani mafunso otsatirawa:

11. Nthaŵi zonse pamene ndime ya m’Baibulo itembenuzidwa m’mawu osiyanasiyana, kodi ndi mfundo iti imene wotembenuza ayenera kutsatira? [rs-CN tsa. 402 ndime 5]

12. Kodi nchiyani chimalepheretsa anthu ena kulandira uphungu? [uw-CN tsa. 127 ndime 4]

13. Kodi kukhulupirira Utatu kumaika okuchirikiza m’mkhalidwe wotani? [rs-CN tsa. 411 ndime 3]

14. Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati: “Khalani nawo mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake”? (Marko 9:50) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w85-CN 11/1 tsa. 24 ndime 12.]

15. Kodi ndi phunziro lotani la phindu limene tingatengepo pakachitidwe ka Yesu pachopereka cha mkazi wamasiye wosauka? (Marko 12:42-44) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 12/1 tsa. 29 ndime 7-tsa. 30 ndime 1.]

16. Pamene Yesu anauza Afarisi kuti Ufumu wa Mulungu unali mkati mwawo, anali kunena za iye yekha kukhala Mfumu yamtsogolo. (Luka 17:21) [kl-CN tsa. 91 ndime 6]

17. Poyerekezera Mateyu 6:9, 10 ndi Luka 11:2-4, kodi nchifukwa ninji tinganene kuti sitifunikira kutsanzira pemphero la chitsanzo mwa liwu ndi liwu? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 5/15 tsa. 16 ndime 6.]

18. Kodi ndi malemba ati m’Masalmo ndi Ahebri amene amasonyeza kuti Yesu sanayambe kulamulira atangokwera kumwamba? [kl-CN tsa. 96 ndime 15]

19. Malinga ndi Chivumbulutso 7:14, kodi chimachitika nchiyani ngati munthu watsuka zovala zake m’mwazi wa Mwana wa Nkhosa? [uw-CN tsa. 106 ndime 6-7]

20. Pakuti timadziŵa kuti Yesu sanasoŵepo chikhulupiriro mwa Mulungu, nchifukwa ninji anafuula kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?” (Marko 15:34) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 6/15 tsa. 31.]

Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Mkate ndi vinyo wogwiritsira ntchito pa Chikumbutso ndi ․․․․․․․․ chabe, mkate kuphiphiritsira ․․․․․․․․ ndi vinyo kuphiphiritsira ․․․․․․․․ wake ․․․․․․․․ [uw-CN tsa. 115 ndime 13]

22. Poona zimene zachitika, zimaonekeratu kuti maitanidwe akumwamba a onse anamalizidwa cha m’ma ․․․․․․․․, pamene chiyembekezo cha moyo padziko lapansi cha ․․․․․․․․ chinaonekera bwino lomwe. [uw-CN tsa. 111 ndime 6]

23. Pamene Yohane Mbatizi anayamba kulalikira, kazembe wa ku Yudeya anali ․․․․․․․․ ndipo wolamulira chigawo cha Galileya anali ․․․․․․․․. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani Luka 3:1.]

24. Mzimu womwe umachitira umboni limodzi ndi maganizo ndi mtima kwa aja omwe alidi ana a Mulungu ndiwo ․․․․․․․․. [uw-CN tsa. 113 ndime 9]

25. Malinga ndi zimene akusonyeza pa Luka 10:16, pamene tilandira ndi chiyamikiro chakudya chauzimu chochokera kwa ․․․․․․․․ ndi Bungwe lake Lolamulira, timaonetsa ulemu kwa ․․․․․․․․. [uw-CN tsa. 123 ndime 13]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Oyera mtima otchulidwa pa Mateyu 27:52 (anaukitsidwa mwakanthaŵi m’thupi; anali mitembo ya akufa imene chivomezi chinaponyera kunja; anaukitsidwa ndi kukwera kumwamba Yesu asanapite). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 9/1 ndime 7.]

27. Pa Akolose 1:15, Yesu akutchedwa “woyamba wobadwa wa chilengedwe chonse,” kutanthauza kuti (ali ngati Mulungu wopanda chiyambi; ali mwana woyamba pa ana ake apadziko lapansi; ali wamkulu pa ana aamuna onse a Yehova). [rs-CN tsa. 394 ndime 4]

28. Kuikidwa kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kunatsimikiziridwa ndi mzimu woyera m’chaka cha (33 C.E.; 1918; 1919). (Mat. 24:45) [uw-CN tsa. 119 ndime 6]

29. Chilangizo chimene Akristu onse ayenera kutsatira, makamaka aja okhala m’malo auyang’aniro m’gulu la Mulungu, nchakuti: “Iye wakukhala (wonyada; wolemekezeka; wamng’onong’ono) wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.” (Luka 9:48) [uw-CN tsa. 122 ndime 12]

30. Kutsuka zovala zathu ndi kuziyeretsa m’mwazi wa Mwana wa Nkhosa kumatanthauza (kuleka kuchita machimo; kuzindikira kuti tifunikira nsembe ya Yesu yotetezera machimo; kupatulira moyo wathu kwa Mulungu ndi kubatizidwa). [uw-CN tsa. 106 ndime 7]

Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:

Miy. 4:13; Dan. 7:9, 10, 13, 14; Marko 7:20-23; 13:10; Luka 8:31

31. Tiyenera kukhala maso kuti tizindikire malingaliro aliwonse oipa kapena oipitsa makhalidwe omwe angafike m’maganizo ndi mumtima wathu ndipo tiyenera kuwachotsa mwamsanga asanazikike. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 11/1 tsa. 14 ndime 16.]

32. Ziŵanda zidzakhala pamodzi ndi Satana m’mkhalidwe wosachita kanthu wonga imfa mkati mwa “zaka chikwi.” (Chiv. 20:3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu]

33. Mzimu wachangu ngwofunika kuti ntchito yopereka umboni padziko lonse ichitike panthaŵi yaifupi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 10/1 tsa. 27.]

34. Kulandira uphungu kungaletse wina kunena kapena kuchita zinthu zomwe zingamchititse chisoni. [uw-CN tsa. 128 ndime 6]

35. Ngakhale kuti sitingazione zolengedwa zauzimu, Mawu a Yehova amatipatsa chithunzi cha gulu lake losaoneka lakumwamba ndi cha ntchito zake zina zimene zimakhudza alambiri ake padziko lapansi. [uw-CN tsa. 117 ndime 1]

S-97-CN Zam, Mal & Moz #292b 8/97

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena