Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/97 tsamba 3-6
  • Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1998

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1998
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Timitu
  • Malangizo
  • NDANDANDA
  • Jan. 12 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 9-10
  • Jan. 19 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 11-13
  • Jan. 26 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 14-16
  • May 4 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 7-9
  • Sept. 7 Kuŵerenga Baibulo: 2 Timoteo 1-4
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 10/97 tsamba 3-6

Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1998

Malangizo

Mu 1998, otsatiraŵa ndiwo adzakhala makonzedwe pochititsa Sukulu Yautumiki Wateokratiki.

MABUKU OPHUNZIRA: Revised Nyanja (Union) Version [bi53], Nsanja ya Olonda [w-CN], Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN], Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha [kl-CN], Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja [fy-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN], adzakhala magwero a nkhani zimene zidzagaŵiridwa.

Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno kupitiriza motere:

NKHANI NA. 1: Mphindi 15. Imeneyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira, ndipo idzatengedwa mu Nsanja ya Olonda kapena buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN]. Ngati yatengedwa mu Nsanja ya Olonda, iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 15 yopanda mafunso openda. Ngati yatengedwa m’buku la Munthu Wamkulu, ikambidwe ngati nkhani yachilangizo ya mphindi 10 mpaka 12, kenako mphindi 3 mpaka 5 za mafunso openda, kugwiritsira ntchito mafunso osindikizidwa m’bukulo. Cholinga chake sichiyenera kukhala cha kungokamba nkhaniyo koma kusamalira kwambiri za phindu lenileni la chidziŵitso chimene chikufotokozedwa, mukumagogomezera mfundo zomwe zidzakhala zothandiza kwambiri mpingowo. Gwiritsirani ntchito mutu wosonyezedwa.

Abale opatsidwa nkhani imeneyi ayenera kukhala osamala kusunga nthaŵi. Uphungu wamseri ungaperekedwe ngati uli wofunikira kapena ngati wapemphedwa ndi mlankhuliyo.

MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 6. Nkhaniyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira amene adzagwiritsira ntchito mfundozo pa zofunika za kumaloko. Siyenera kukhala chidule wamba cha kuŵerenga kwa mlunguwo. Choyamba perekani chithunzi chachidule cha machaputala onse a mlunguwo pa masekondi 30 mpaka 60. Komabe, cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvetsera kuzindikira chifukwa chake ndi mmene chidziŵitsocho chilili chaphindu kwa ife. Ndiyeno woyang’anira sukulu adzauza ophunzirawo kupita kumakalasi awo osiyanasiyana.

NKHANI NA. 2: Mphindi 5. Iyi ndi nkhani ya kuŵerenga Baibulo kwa mbali yogaŵiridwa kochitidwa ndi mbale. Nkhaniyi idzakambidwa m’sukulu yaikulu limodzinso ndi m’timagulu tinato. Kaŵirikaŵiri mbali zoŵerenga zimakhala zazifupi mololeza wophunzira kukamba mawu oyamba ndi omaliza achidule opereka chidziŵitso pankhaniyo. Zingaphatikizepo mbiri yakale, tanthauzo la ulosi kapena la chiphunzitso, ndi mmene mapulinsipulo angagwirire ntchito. Mavesi onse ogaŵiridwa ayenera kuŵerengedwa mosalekeza. Ndithudi, pamene mavesi owaŵerenga saali ondondozana, wophunzira angatchule vesi lopitirizira kuŵerengako.

NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhaniyi idzapatsidwa kwa mlongo. Idzatengedwa m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, kapena Kukambitsirana za m’Malemba. Chochitikacho chingakhale umboni wamwamwaŵi, ulendo wobwereza, kapena phunziro la Baibulo la panyumba, ndipo okambawo angakhale pansi kapena kuimirira. Woyang’anira sukulu adzafuna makamaka kuona mmene wophunzirayo adzathandizira mwini nyumba kusinkhasinkha ndi kumvetsetsa nkhaniyo ndi mmene adzagwiritsira ntchito malemba. Wophunzira wopatsidwa nkhani imeneyi ayenera kudziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi, koma mukhoza kugwiritsira ntchito wothandiza winanso. Wophunzirayo ndiye angasankhe kuti kaya amlole mwini nyumba kuŵerenga ndime zina kapena ayi pamene akuphunzira buku la Chidziŵitso kapena la Chinsinsi. Chimene chiyenera kusamalidwa kwambiri, si mkhalidwe wa chochitikacho, koma kugwiritsira ntchito mfundo kogwira mtima.

NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Ngati nkhani imeneyi yatengedwa m’buku la ‘Kukambitsirana za m’Malemba,’ idzakhala ya mbale kapena mlongo. Ngati yatengedwa m’buku la Chinsinsi, idzakhala ya mbale. Nkhani iliyonse mutu wake ulimo kale pandandanda. Pamene ipatsidwa kwa mbale, iyenera kukhala nkhani yokambidwa kwa omvetsera onse. Kaŵirikaŵiri kudzakhala bwino kuti mbaleyo akonzekere nkhani yake akumalingalira za omvetsera ake m’Nyumba ya Ufumu kotero kuti idzakhaledi yopatsa chidziŵitso ndi yopindulitsa omvetsera. Pamene ipatsidwa kwa mlongo, iyenera kuperekedwa mofanana ndi Nkhani Na. 3.

*NDANDANDA YOWONJEZERA YA KUŴERENGA BAIBULO: Imeneyo taiika m’mabulaketi, pambuyo pa nambala ya nyimbo ya mlungu uliwonse. Mwa kutsatira ndandanda imeneyi, mukumaŵerenga masamba ngati khumi pamlungu, mungaŵerenge Baibulo lonse m’zaka zitatu. Ndandanda ya kuŵerenga yowonjezera imeneyi siili maziko a nkhani za programu ya sukulu kapena kupenda kolemba.

CHIDZIŴITSO: Za chidziŵitso china ndi malangizo onena za uphungu, kusunga nthaŵi, kupenda kolemba, ndi kukonzekera nkhani, chonde onani patsamba 3 la Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996.

NDANDANDA

Jan. 5 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 7-8

Nyimbo Na. 196 [*Genesis 1-9]

Na. 1: “Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Choonadi” (w96-CN 1/1 mas. 29-31)

Na. 2: Machitidwe 7:44-60

Na. 3: Nthaŵi Zonse Mverani Wolamulira Wamkulu pa Onse (kl-CN mas. 130-1 ndime 1-6)

Na. 4: Mboni za Yehova Si Chipembedzo cha ku Amereka, Sizili Kagulu ka Mpatuko (rs-CN tsa. 272 ndime 4-6, mpaka tsa. 273 ndime 4-6)

Jan. 12 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 9-10

Nyimbo Na. 53 [*Genesis 10-18]

Na. 1: Khalani Wolengeza Mawu a Mulungu Wolimba Mtima (w96-CN 1/15 mas. 24-5)

Na. 2: Machitidwe 9:1-16

Na. 3: Gonjerani Maulamuliro Aakulu (kl-CN mas. 131-3 ndime 7-10)

Na. 4: Mboni za Yehova Si Chipembedzo Chatsopano (rs-CN tsa. 274 ndime 1-4)

Jan. 19 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 11-13

Nyimbo Na. 162 [*Genesis 19-24]

Na. 1: Yang’anani Kupyola pa Zimene Mukuona! (w96-CN 2/15 mas. 27-9)

Na. 2: Machitidwe 13:1-12

Na. 3: Zindikirani Makonzedwe a Mulungu a Ulamuliro m’Banja (kl-CN mas. 134-6 ndime 11-18)

Na. 4: Chifukwa Chake Timakhulupirira kuti Chipembedzo Chathu Ndicho Choka Cholondola (rs-CN tsa. 275 ndime 1, 2)

Jan. 26 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 14-16

Nyimbo Na. 180 [*Genesis 25-30]

Na. 1: Kuchita Mogwirizana ndi Lumbiro Lanu la Ukwati (w96-CN 3/1 mas. 19-22)

Na. 2: Machitidwe 16:1-15

Na. 3: Ulamuliro Mumpingo—Makonzedwe Achikondi a Yehova (kl-CN mas. 137-9 ndime 19-25)

Na. 4: Maziko Odziŵira Chipembedzo Choona (rs-CN tsa. 275 ndime 3)

Feb. 2 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 17-19

Nyimbo Na. 111 [*Genesis 31-36]

Na. 1: Yehova—Wokonda Chilungamo ndi Chiweruzo (w96-CN 3/15 mas. 21-3)

Na. 2: Machitidwe 18:1-11

Na. 3: Mmene Kukhulupirika Kumamangira Banja Lachimwemwe (kl-CN mas. 140-1 ndime 1-6)

Na. 4: Njira za Kulimvetsetsa Baibulo (rs-CN tsa. 276 ndime 1-4)

Feb. 9 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 20-21

Nyimbo Na. 38 [*Genesis 37-42]

Na. 1: Senzani Yehova Nkhaŵa Yanu Nthaŵi Zonse (w96-CN 4/1 mas. 27-30)

Na. 2: Machitidwe 21:1-14

Na. 3: Kufunika Kwake kwa Kulankhulana Muukwati (kl-CN mas. 142-3 ndime 7-9)

Na. 4: Chifukwa Chake Pali Masinthidwe m’Ziphunzitso za Mboni za Yehova (rs-CN tsa. 277 ndime 1)

Feb. 16 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 22-24

Nyimbo Na. 8 [*Genesis 43-49]

Na. 1: “Mphindi Yakutonthola ndi Mphindi Yakulankhula” (w96-CN 5/15 mas. 21-3)

Na. 2: Machitidwe 22:1-16

Na. 3: Chitirani Ulemu Mnzanu wa Muukwati (kl-CN mas. 143-5 ndime 10-14)

Na. 4: Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba Nkwam’malemba Ndipo Kumagwira Mtima (rs-CN tsa. 277 ndime 2-5)

Feb. 23 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 25-26

Nyimbo Na. 179 [*Genesis 50-Eksodo 7]

Na. 1: Kodi Kukonda Mulungu Kumatanthauzanji? (w96-CN 6/15 mas. 4-7)

Na. 2: Machitidwe 25:1-12

Na. 3: Khalani Chitsanzo Chabwino ndipo Sonyezani Ana Anu Chikondi (kl-CN mas. 145-6 ndime 15-18)

Na. 4: Kodi Nchifukwa Ninji Mboni za Yehova Zimazunzidwa? (rs-CN tsa. 278 ndime 2, 3)

Mar. 2 Kuŵerenga Baibulo: Machitidwe 27-28

Nyimbo Na. 92 [*Eksodo 8-13]

Na. 1: Chifukwa Chake Yesu Anatchedwa “Munthuyu” (gt-CN mutu 123)

Na. 2: Machitidwe 27:33-44

Na. 3: Zimene Chilango Chachikondi ndi Chitsogozo Chaluso Zingachite (kl-CN mas. 148-9 ndime 19-23)

Na. 4: Yesu Kristu Anali Munthu wa m’Mbiri (rs-CN tsa. 423 ndime 1 mpaka tsa. 424 ndime 1)

Mar. 9 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 1-3

Nyimbo Na. 79 [*Eksodo 14-20]

Na. 1: Chifukwa Chake Pilato Anaopa Yesu (gt-CN mutu 124)

Na. 2: Aroma 1:18-32

Na. 3: Chifukwa Chake Timafuna Kuyandikira kwa Mulungu (kl-CN mas. 150-2 ndime 1-5)

Na. 4: Yesu Sanali Kokha Munthu Wabwino (rs-CN tsa. 424 ndime 2)

Mar. 16 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 4-6

Nyimbo Na. 174 [*Eksodo 21-27]

Na. 1: “Muzindikire Otere” (w96-CN 6/15 mas. 28-30)

Na. 2: Aroma 4:1-15

Na. 3: Zofunika Kuti Tiyandikire kwa Mulungu (kl-CN mas. 152-3 ndime 6-9)

Na. 4: Yesu Sanali Mneneri Wongodzipanga Yekha (rs-CN tsa. 424 ndime 3)

Mar. 23 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 7-9

Nyimbo Na. 27 [*Eksodo 28-33]

Na. 1: Zimene Zolengedwa “Zanzeru Mwachibadwa” Zingatiphunzitse (w96-CN 7/15 mas. 21-3)

Na. 2: Aroma 9:1-18

Na. 3: Lankhulani ndi Mulungu Ndipo Akumveni

(kl-CN mas. 153-5 ndime 10-14)

Na. 4: Chifukwa Chake Ayuda Ambiri Sanavomereza Yesu Monga Mesiya Wawo (rs-CN tsa. 425 ndime 1, 2)

Mar. 30 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 10-12

Nyimbo Na. 70 [*Eksodo 34-39]

Na. 1: Maphunziro Othandiza Otengedwa ku Dziko Lolonjezedwa (w96-CN 8/15 mas. 4-8)

Na. 2: Aroma 10:1-15

Na. 3: Limbikirani Kupemphera Ndipo Mvetserani (kl-CN mas. 156-9 ndime 15-20)

Na. 4: Mmene Tikudziŵira kuti Yesu Kwenikweni Saali Mulungu (rs-CN tsa. 426 ndime 1, 2)

Apr. 6 Kuŵerenga Baibulo: Aroma 13-16

Nyimbo Na. 175 [*Eksodo 40-Levitiko 7]

Na. 1: Maumboni Akuti Yesu Amakonda Anthu (gt-CN mutu 125)

Na. 2: Aroma 13:1-10

Na. 3: Pezani Chisungiko Chenicheni Pakati pa Anthu a Mulungu (kl-CN mas. 160-1 ndime 1-4)

Na. 4: Zimene Yohane 1:1 Amanena ndi Zimene Samanena (rs-CN tsa. 426 ndime 4 mpaka tsa. 427 ndime 1)

Apr. 13 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 1-3

Nyimbo Na. 173 [*Levitiko 8-13]

Na. 1: Mmene Yesu Anasonyezera Chitsanzo Mpaka Mapeto (gt-CN mutu 126)

Na. 2: 1 Akorinto 1:10-25

Na. 3: Mmene Yehova Amaperekera Chakudya Chauzimu (kl-CN mas. 162-3 ndime 5-8)

Na. 4: Yohane 20:28 Samatsimikizira kuti Yesu Anali Mulungu (rs-CN tsa. 427 ndime 2-4)

Apr. 20 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 4-6

Nyimbo Na. 56 [*Levitiko 14-19]

Na. 1: Kodi Baibulo Limaphunzitsa za Kukhulupirira Choikidwiratu? (w96-CN 9/1 mas. 4-7)

Na. 2: 1 Akorinto 4:1-13

Na. 3: Zimene Kukhala ndi Chikondi Kumatanthauza (kl-CN mas. 163-6 ndime 9-14)

Na. 4: Chifukwa Chake Mateyu 1:23 Samatsimikizira kuti Yesu Anali Mulungu (rs-CN tsa. 428 ndime 1-3)

Apr. 27 Kupenda Kolemba. Malizani Machitidwe 7-1 Akorinto 6

Nyimbo Na. 91 [*Levitiko 20-25]

May 4 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 7-9

Nyimbo Na. 29 [*Levitiko 26-Numeri]

Na. 1: Kodi Mufunikiradi Kupepesa? (w96-CN 9/15 mas. 22-4)

Na. 2: 1 Akorinto 7:10-24

Na. 3: Mpingo—Malo Achisungiko (kl-CN mas. 167-9 ndime 15-20)

Na. 4: Chifukwa Chake Yohane 5:18 Samatsimikizira kuti Yesu Ndiye Yehova (rs-CN tsa. 428 ndime 4, 5)

May 11 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 10-12

Nyimbo Na. 103 [*Numeri 4-9]

Na. 1: Kubwerera Kufumbi—Motani? (w96-CN 9/15 mas. 29-31)

Na. 2: 1 Akorinto 11:1-16

Na. 3: Tsanzirani Yesu—Tumikirani Mulungu Kosatha (kl-CN mas. 170-3 ndime 1-6)

Na. 4: Chifukwa Chake Yesu Sindiye Woyenera Kulambiridwa (rs-CN tsa. 429 ndime 1-3)

May 18 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 13-14

Nyimbo Na. 160 [*Numeri 10-15]

Na. 1: Ntchito Yosamalira Banja Lanu (w96-CN 10/1 mas. 29-31)

Na. 2: 1 Akorinto 14:1-12

Na. 3: Njira Zofunika Zotsogolera ku Moyo (kl-CN mas. 173-5 ndime 7-9)

Na. 4: Zozizwitsa Zimene Yesu Anachita Sizimatsimikizira kuti Anali Mulungu (rs-CN tsa. 429 ndime 1 mpaka 430 ndime 2)

May 25 Kuŵerenga Baibulo: 1 Akorinto 15-16

Nyimbo Na. 158 [*Numeri 16-22]

Na. 1: Chifukwa Chake Tiyenera Kudziŵa za Kuikidwa kwa Yesu ndi Manda Apululu (gt-CN mutu 127)

Na. 2: 1 Akorinto 16:1-13

Na. 3: Chifukwa Chake Ubatizo Uli Wofunika (kl-CN mas. 175-6 ndime 10-12)

Na. 4: Chipulumutso Chimafuna Zambiri Osati Kungokhulupirira Yesu Basi (rs-CN tsa. 430 ndime 4)

June 1 Kuŵerenga Baibulo: 2 Akorinto 1-4

Nyimbo Na. 58 [*Numeri 23-29]

Na. 1: Chisangalalo pa Kuuka kwa Yesu (gt-CN mutu 128)

Na. 2: 2 Akorinto 4:1-12

Na. 3: Ubatizo—Chinthu Chofunika Kwambiri m’Moyo Wanu (kl-CN tsa. 177, ndime 13-16)

Na. 4: Yesu Analiko Asanakhale Munthu (rs-CN tsa. 431 ndime 1, 2)

June 8 Kuŵerenga Baibulo: 2 Akorinto 5-8

Nyimbo Na. 193 [*Numeri 30-35]

Na. 1: Moyo Pambuyo pa Imfa—Motani, Kuti, Liti? (w96-CN 10/15 mas. 4-7)

Na. 2: 2 Akorinto 7:1-13

Na. 3: Zimene Kukhala ndi Moyo Monga mwa Kudzipatulira Kwathu Zimatanthauza (kl-CN mas. 178-80 ndime 17-22)

Na. 4: Yesu Sanapite ndi Thupi Lake Lanyama Kumwamba (rs-CN tsa. 431 ndime 3-6)

June 15 Kuŵerenga Baibulo: 2 Akorinto 9-13

Nyimbo Na. 43 [*Numeri 36-Deuteronomo 4]

Na. 1: Mmene Chikhulupiriro m’Chiukiriro Chimalimbira (gt-CN mutu 129)

Na. 2: 2 Akorinto 10:1-12

Na. 3: Kukonzekera Tsopano “Moyo Weniweniwo” (kl-CN mas. 181-2 ndime 1-5)

Na. 4: Yesu ndi Mikaeli Ali Munthu Mmodzimodziyo (rs-CN tsa. 432 ndime 1-3)

June 22 Kuŵerenga Baibulo: Agalatiya 1-3

Nyimbo Na. 127 [*Deuteronomo 5-11]

Na. 1: Yesu Akufotokoza Mmene Tingasonyezere Chikondi (gt-CN mutu 130)

Na. 2: Agalatiya 1:1-12

Na. 3: Pambuyo pa Armagedo—Dziko Lapansi Laparadaiso (kl-CN mas. 182-4 ndime 6-11)

Na. 4: Mboni za Yehova Zimakhulupirira Yesu (rs-CN tsa. 433 ndime 1-3)

June 29 Kuŵerenga Baibulo: Agalatiya 4-6

Nyimbo Na. 98 [*Deuteronomo 12-19]

Na. 1: Mmene Yesu Alimbikitsira Ophunzira Ake (gt-CN mutu 131)

Na. 2: Agalatiya 6:1-18

Na. 3: Mtendere Konsekonse ndi Kuuka kwa Akufa (kl-CN mas. 184-6 ndime 12-18)

Na. 4: Mboni za Yehova Zimalandira Yesu Monga Mpulumutsi (rs-CN tsa. 433 ndime 4 mpaka tsa. 434 ndime 2)

July 6 Kuŵerenga Baibulo: Aefeso 1-3

Nyimbo Na. 71 [*Deuteronomo 20-27]

Na. 1: Zimene Yesu Akuchita ku Dzanja Lamanja la Mulungu (gt-CN mutu 132)

Na. 2: Aefeso 1:1-14

Na. 3: Chimene Ungwiro Udzatanthauza, ndi Mmene Tingasangalalire Nawo (kl-CN mas. 187-91 ndime 19-25)

Na. 4: Lero Ayuda Salinso Anthu Osankhidwa a Mulungu (rs-CN tsa. 42 ndime 2 mpaka tsa. 43 ndime 3)

July 13 Kuŵerenga Baibulo: Aefeso 4-6

Nyimbo Na. 214 [*Deuteronomo 28-32]

Na. 1: Chifukwa Chake Yesu Anali Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako (gt-CN mutu 133)

Na. 2: Aefeso 6:1-13

Na. 3: Si Ayuda Onse Amene Adzatembenukira kwa Kristu (rs-CN tsa. 44 ndime 1, 2)

Na. 4: Banja Lili Pavuto (fy-CN mas. 5-9 ndime 1-14)

July 20 Kuŵerenga Baibulo: Afilipi 1-4

Nyimbo Na. 123 [*Deuteronomo 33-Yoswa 6]

Na. 1: Chifukwa Chake Aliyense Ayenera Kuŵerenga Buku la Munthu Wamkulu (gt-CN Gwiritsirani ntchito mawu oyamba kukonza nkhaniyo.)

Na. 2: Afilipi 1:1-14

Na. 3: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja (fy-CN mas. 9-12 ndime 15-23)

Na. 4: Ayuda Nawonso Ayenera Kukhulupirira Yesu Kristu Kuti Apulumuke (rs-CN tsa. 44 ndime 3, 4)

July 27 Kuŵerenga Baibulo: Akolose 1-4

Nyimbo Na. 64 [*Yoswa 7-12]

Na. 1: Gabrieli Afikira Zakariya ndi Mariya (gt-CN mutu 1)

Na. 2: Akolose 4:1-13

Na. 3: Israyeli Lero Sakukwaniritsa Maulosi a Baibulo (rs-CN tsa. 45 ndime 1-3)

Na. 4: Kodi Muli Wokonzeka Kuloŵa Ukwati? (fy-CN mas. 13-15 ndime 1-6)

Aug. 3 Kuŵerenga Baibulo: 1 Atesalonika 1-5

Nyimbo Na. 35 [*Yoswa 13-19]

Na. 1: Yesu Alemekezedwa Asanabadwe (gt-CN mutu 2)

Na. 2: 1 Atesalonika 2:1-12

Na. 3: Chifukwa Chake Muyenera Kudzidziŵa Nokha ndi Kukhala Woona Mtima (fy-CN mas. 16-18 ndime 7-10)

Na. 4: Maulosi Onena za Kubwezeretsa Akukwaniritsidwa pa Israyeli Wauzimu (rs-CN tsa. 46 ndime 3 mpaka 47 ndime 2)

Aug. 10 Kuŵerenga Baibulo: 2 Atesalonika 1-3

Nyimbo Na. 10 [*Yoswa 20-Oweruza 1]

Na. 1: Kubadwa kwa Yohane (gt-CN mutu 3)

Na. 2: 2 Atesalonika 1:1-12

Na. 3: Ufumu wa Mulungu ndi Boma Lenileni (rs-CN tsa. 375 ndime 1, 2)

Na. 4: Zimene Muyenera Kufuna mwa Wokwatirana Naye (fy-CN mas. 20-22 ndime 11-15)

Aug. 17 Kuŵerenga Baibulo: 1 Timoteo 1-3

Nyimbo Na. 221 [*Oweruza 2-7]

Na. 1: Yosefe Akwatira Mariya Ali Wapakati (gt-CN mutu 4)

Na. 2: 1 Timoteo 1:3-16

Na. 3: Zinthu Zofuna Kulingalira Musanawinde kwa Moyo Wonse (fy-CN mas. 22-24 ndime 16-19)

Na. 4: Kodi Ndani Amene Ali Olamulira mu Ufumu wa Mulungu? (rs-CN tsa. 375 ndime 3-5)

Aug. 24 Kuŵerenga Baibulo: 1 Timoteo 4-6

Nyimbo Na. 30 [*Oweruza 8-13]

Na. 1: Kubadwa kwa Yesu—Kuti Ndipo Liti? (gt-CN mutu 5)

Na. 2: 1 Timoteo 4:1-16

Na. 3: Chiyambukiro Chimene Ufumu wa Mulungu Udzakhala Nacho pa Maboma a Anthu (rs-CN tsa. 376 ndime 1, 2)

No. 4: Khalani ndi Chibwenzi Cholemekezeka, Ndipo Onani ndi Zapambuyo pa Phwando la Ukwati (fy-CN mas. 24-6 ndime 20-3)

Aug. 31 Kupenda Kolemba. Malizani 1 Akorinto 7-1 Timoteo 6

Nyimbo Na. 59 [*Oweruza 14-19]

Sept. 7 Kuŵerenga Baibulo: 2 Timoteo 1-4

Nyimbo Na. 46 [*Oweruza 20-Rute 4]

Na. 1: Mwana wa Lonjezo (gt-CN mutu 6)

Na. 2: 2 Timoteo 3:1-13

Na. 3: Mapulinsipulo a Baibulo Amene Angakuthandizeni Kukonzekera Ukwati Wachipambano

(fy-CN tsa. 26 bokosi la kupenda)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzachirikiza Uchifumu wa Mulungu ndi Kuthetsa Ulamuliro wa Satana (rs-CN tsa. 376 ndime 3-5)

Sept. 14 Kuŵerenga Baibulo: Tito 1-Filemoni

Nyimbo Na. 155 [1 Samueli 1-8]

Na. 1: Yesu ndi Openda Nyenyezi (gt-CN mutu 7)

Na. 2: Tito 3:1-14

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzagwirizanitsa Anthu pa Kulambira Koyera (rs-CN tsa. 377 ndime 1, 2)

Na. 4: Kiyi Yoyamba ya Ukwati Wokhalitsa (fy-CN mas. 27-9 ndime 1-6)

Sept. 21 Kuŵerenga Baibulo: Ahebri 1-3

Nyimbo Na. 149 [*1 Samueli 9-14]

Na. 1: Kuthaŵa Wolamulira Wankhalwe (gt-CN mutu 8)

Na. 2: Ahebri 3:1-15

Na. 3: Kiyi Yachiŵiri ya Ukwati Wokhalitsa (fy-CN mas. 30-1 ndime 7-10)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzamasula Anthu ku Nkhondo ndi Chitsenderezo (rs-CN tsa. 377 ndime 3, mpaka tsa. 378 ndime 2)

Sept. 28 Kuŵerenga Baibulo: Ahebri 4-7

Nyimbo Na. 3 [*1 Samueli 15-19]

Na. 1: Nkumpatsiranji Yehova? (w96-CN 11/1 mas. 28-30)

Na. 2: Ahebri 6:1-12

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzagaŵira Chakudya Chochuluka ndi Kuthetsa Matenda (rs-CN tsa. 378 ndime 3-5)

Na. 4: Umutu wa Mwamuna Uyenera Kufanana ndi wa Kristu (fy-CN mas. 31-3 ndime 11-15)

Oct. 5 Kuŵerenga Baibulo: Ahebri 8-10

Nyimbo Na. 209 [*1 Samueli 20-25]

Na. 1: Tsanzirani Kupanda Tsankhu kwa Yehova (w96-CN 11/15 mas. 25-7)

Na. 2: Ahebri 8:1-12

Na. 3: Mmene Mkazi Angathangatire Mwamuna Wake (fy-CN mas. 34-5 ndime 16-19)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzagaŵira Nyumba ndi Ntchito Zokhutiritsa Onse (rs-CN tsa. 378 ndime 6, 7)

Oct. 12 Kuŵerenga Baibulo: Ahebri 11-13

Nyimbo Na. 108 [*1 Samueli 26-2 Samueli 2]

Na. 1: Moyo Wabanja Woyambirira wa Yesu (gt-CN mutu 9)

Na. 2: Ahebri 11:1-10

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Ukulonjeza Chisungiko ndi Chilungamo (rs-CN tsa. 379 ndime 1-4)

Na. 4: Zomwe Kulankhulana Kwabwino Kumatanthauza (fy-CN mas. 35-8 ndime 20-6)

Oct. 19 Kuŵerenga Baibulo: Yakobo 1-5

Nyimbo Na. 144 [*2 Samueli 3-10]

Na. 1: Ku Yerusalemu Pamene Anali Wazaka 12 (gt-CN mutu 10)

Na. 2: Yakobo 5:1-12

Na. 3: Mapulinsipulo a Baibulo Amene Angakuthandizeni Kukhala ndi Ukwati Wachimwemwe ndi Wokhalitsa (fy-CN tsa. 38 bokosi la kupenda)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Udzaukitsa Akufa ndi Kuthetsa Imfa ya Adamu (rs-CN tsa. 379 ndime 6, mpaka tsa. 380 ndime 2)

Oct. 26 Kuŵerenga Baibulo: 1 Petro 1-5

Nyimbo Na. 54 [*2 Samueli 11-15]

Na. 1: Yohane Akonzera Yesu Njira (gt-CN mutu 11)

Na. 2: 1 Petro 4:1-11

Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzasandutsa Dziko Kukhala Paradaiso (rs-CN tsa. 380 ndime 3, mpaka tsa. 381 ndime 1)

Na. 4: Khalirani Moyo Zimene Muli Nazo (fy-CN tsa. 39-41 ndime 1-6)

Nov. 2 Kuŵerenga Baibulo: 2 Petro 1-3

Nyimbo Na.177 [*2 Samueli 16-20]

Na. 1: Zimene Zikuchitika Yesu Atabatizidwa (gt-CN mutu 12)

Na. 2: 2 Petro 3:1-13

Na. 3: Kusamalira Banja ndi Ntchito ya Banja Lonse (fy-CN mas. 42-4 ndime 7-11)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Sunakhazikitsidwe m’Zaka za Zana Loyamba (rs-CN tsa. 381 ndime 2-4)

Nov. 9 Kuŵerenga Baibulo: 1 Yohane 1-5

Nyimbo Na. 114 [*2 Samueli 21-1 Mafumu 1]

Na. 1: Kuphunzirapo Kanthu pa Ziyeso za Yesu (gt-CN mutu 13)

Na. 2: 1 Yohane 5:1-12

Na. 3: Kodi Nchiyani Chimene Chimasonyeza Kuti Tikukhala m’Masiku Otsiriza? (rs-CN tsa. 261 ndime 3)

Na. 4: Chifukwa Chake Yehova Amafuna Kuti Tizikhala Aukhondo (fy-CN mas. 45-9 ndime 12-20)

Nov. 16 Kuŵerenga Baibulo: 2 Yohane-Yuda

Nyimbo Na. 22 [*1 Mafumu 2-6]

Na. 1: Ophunzira Oyambirira a Yesu (gt-CN mutu 14)

Na. 2: 2 Yohane 1:1-13

Na. 3: Mmene Kutamanda ndi Kuyamikira Koona Mtima Kumalimbikitsira Banja (fy-CN mas. 49-50 ndime 21-2)

Na. 4: Nkhondo Zazikulu, Chizindikiro cha Masiku Otsiriza (rs-CN tsa. 262 ndime 1-3)

Nov. 23 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 1-3

Nyimbo Na. 195 [*1 Mafumu 7-10]

Na. 1: Chozizwitsa Choyamba cha Yesu (gt-CN mutu 15)

Na. 2: Chivumbulutso 3:1-11

Na. 3: Masiku Otsiriza Akudziŵika ndi Njala ndi Zivomezi (rs-CN tsa. 262 ndime 4, mpaka tsa. 263 ndime 1)

Na. 4: Lingaliro la Baibulo pa Ana ndi Udindo wa m’Banja (fy-CN mas. 51-2 ndime 1-5)

Nov. 30 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 4-6

Nyimbo Na. 203 [*1 Mafumu 11-15]

Na. 1: Kodi Mukanamzindikira Mesiya? (w96-CN 11/15 mas. 28-31)

Na. 2: Chivumbulutso 5:1-12

Na. 3: Zimene Kukwaniritsa Zofunika za Mwana Kumatanthauza (fy-CN mas. 53-5 ndime 6-9)

Na. 4: Miliri ndi Kusayeruzika, Zizindikiro za Masiku Otsiriza (rs-CN tsa. 263 ndime 2, mpaka tsa. 264 ndime 3)

Dec. 7 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 7-9

Nyimbo Na. 200 [*1 Mafumu 16-20]

Na. 1: ‘Nkukumbukiriranji Masiku Apitawo?’ (w96-CN 12/1 mas. 29-31)

Na. 2: Chivumbulutso 8:1-13

Na. 3: Zizindikiro za Masiku Otsiriza: Ntchito Yolalikira ndi Kuzunzidwa kwa Akristu (rs-CN tsa. 265 ndime 2, 3)

Na. 4: Khomerezani Choonadi mwa Mwana Wanu (fy-CN mas. 55-7 ndime 10-15)

Dec. 14 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 10-12

Nyimbo Na. 137 [*1 Mafumu 21-2 Mafumu 3]

Na. 1: Lingaliro Laumulungu pa Moŵa (w96-CN 12/15 mas. 25-9)

Na. 2: Chivumbulutso 10:1-11

Na. 3: Phunzitsani Mwana Wanu Njira za Yehova (fy-CN mas. 58-9 ndime 16-19)

Na. 4: Kodi Masiku Otsiriza Akusonya ku Chiyani, Ndipo Kodi ndi Motani Mmene Olemba Mbiri Amaonera Masiku Otsiriza? (rs-CN tsa. 266 ndime 1-3 mpaka tsa. 267 ndime 1)

Dec. 21 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 13-15

Nyimbo Na. 60 [*2 Mafumu 4-9]

Na. 1: Changu cha Kulambira Yehova (gt-CN mutu 16)

Na. 2: Chivumbulutso 13:1-15

Na. 3: Ena Adzapulumuka Mapeto a Dziko (rs-CN tsa. 267 ndime 2, mpaka tsa. 268 ndime 1)

Na. 4: Kufunika kwa Chilango m’Njira Zake Zosiyanasiyana (fy-CN mas. 59-61 ndime 20-3)

Dec. 28 Kupenda Kolemba. Malizani 2 Timoteo 1-Chivumbulutso 15

Nyimbo Na. 212 [*2 Mafumu 10-15]

S-38b-CN MOZ & ZAM 10/97

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena