Misonkhano Yautumiki ya October
Mlungu Woyambira October 6
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.
Mph. 15: “Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?” Mafunso ndi mayankho. Bwerezani mfundo zazikulu za Uthenga wa Ufumu Na. 35. Tchulani zifukwa zimene anthu a m’dera lanu adzapindulira nawo uthenga umenewu. Gogomezerani kufunika kwa kukonzekera tsopano kutengamo mbali mokwanira pakuugaŵira ndi kuchita khama lobwerera kumene anapeza anthu okondwerera.
Mph. 20: “Gaŵirani Uthenga wa Ufumu Na. 35 Kulikonse.” Nkhani yotsegulira ya woyang’anira utumiki. Bwerezani makonzedwe a kwanuko owonjezera ntchito. Kambitsiranani njira zotsimikizira kuti gawo lonse lafoledwa. Ofalitsa angagaŵire Uthenga wa Ufumu Na. 35 pochitira umboni kwa anthu pasiteshoni yabasi, m’masitolo ang’onoang’ono, poimika magalimoto, ndi kwina kulikonse. Perekani malingaliro a mmene mungathandizire achatsopano omwe akufuna kuyamba ntchito yolalikira. Phatikizanipo chidziŵitso cha m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa April 1995, ndime 11. Chitani zitsanzo zachidule ziŵiri kapena zitatu.
Nyimbo Na. 126 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 13
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Pendani mfundo zokambitsirana za m’makope atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Akumbutseni onse kuti pantchito ya pakutha kwa mlungu tizigaŵira magazini pamodzi ndi Uthenga wa Ufumu Na. 35. Tiyenera kubwerera kwa onse omwe anachita chidwi.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 18: “Kodi Amphwayi Mumachita Nawo Bwanji?” Kukambitsirana kwa akulu aŵiri. Phatikizanipo mawu a nkhani yomwe ili pa kamutu kakuti ‘Mmene Mungalakire Mphwayi’ mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 15, 1974, masamba 445-6.
Nyimbo Na. 130 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 20
Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Bwerezani zina mwa zokumana nazo za mu 1996 Yearbook, masamba 6-8 za “Kufalitsa Uthenga wa Ufumu Padziko Lonse.” Sonyezani mmene wofalitsa aliyense anachitira khama pogaŵira Uthenga wa Ufumu ulendo wathawu. Alimbikitseni onse kutengamo mbali mokwanira pofalitsa Uthenga wa Ufumu Na. 35.
Mph. 15: Mfundo zazikulu za Brosha Latsopano lakuti, Buku la Anthu Onse. Kukambitsirana ndi omvetsera zifukwa zimene tiyenera kuphunzirira Baibulo. Brosha limeneli analilembera anthu omwe angakhale ophunzira bwino koma omwe sadziŵa zambiri za m’Baibulo. M’malo moyesa kuwakhutiritsa kuti Mulungu ndiye anauzira Baibulo, broshalo limangolola maumboni kulankhula okha. Tiyenera kumaliŵerenga ndi kumalifotokozera ena, kuphatikizapo amene tikuphunzira nawo.
Mph. 15: “Kodi Ndinu Mboni Yanthaŵi Zonse?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 27
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Pendani mmene Uthenga wa Ufumu Na. 35 ukuyendera. Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zolimbikitsa. Lengezani ukulu wa gawo limene lafoledwa kale, ndi zimene zikufunika kuti litsirizidwe pomadzafika November 16. Titangomaliza kufola gawolo, tidzagaŵira buku la Chidziŵitso pamasiku otsala a mweziwo. Gogomezerani za kukhala ndi cholinga chokayamba maphunziro pa maulendo obwereza kumene anthu anachita chidwi ndi Uthenga wa Ufumu.
Mph. 15: “Mmene Mungakhalire ndi Chiyembekezo Mutataya Mtima”. Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1997, masamba 22-5.
Mph. 18: Lolani Kuunika Kwanu Kuwale. Nkhani ndi kukambitsirana za m’buku la Uminisitala Wathu, masamba 84-8. Uzani ofalitsa isanafike nthaŵiyo kuti akonzekere kudzayankha mwachindunji mafunso otsatirawa: (1) Kodi nchifukwa chiyani Mboni za Yehova zimalalikira kunyumba ndi nyumba? (2) Kodi njira imeneyi anaigwiritsira ntchito mpaka pati m’zaka za zana loyamba? (3) Chifukwa nchiyani tifunikira kuchita changu polalikira kunyumba ndi nyumba lero? (4) Ndi mikhalidwe yotani yomwe ingatilepheretse kutengamo mbali nthaŵi zonse? (5) Kodi tingathandizidwe bwanji kuti tipitirizebe? (6) Kodi timadalitsidwa bwanji tikamalola kuunika kwathu kuwala? (7) Kodi tingatani kuti tizitha kupangitsa anthu kumvetsera polankhula nawo? Chitirani chitsanzo ndi ofalitsa atatu kapena anayi omasimba zokumana nazo zolimbikitsa zomwe anaona pogwira ntchito kusitolo ndi sitolo kapena pochitira umboni pakhwalala.
Nyimbo Na. 136 ndi pemphero lomaliza.