Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/97 tsamba 1
  • Lankhulani za Yehova Masiku Onse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lankhulani za Yehova Masiku Onse
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Lemekezani Yehova Tsiku Lililonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Tamandani Yehova Nthaŵi Zonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Timakonda Kwambiri Atate Wathu Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 12/97 tsamba 1

Lankhulani za Yehova Masiku Onse

1 Anthu amakonda kulankhula za chilichonse chimene mtima wawo umakonda, pakuti m’kamwa mwake mwa munthu mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake. (Luka 6:45b) Kodi mtima wathu umakondanji? Wamasalmo analemba kuti: “Lilime langa lilalikire chilungamo chanu, ndi lemekezo lanu tsiku lonse.” (Sal. 35:28) Ankamkonda kwambiri Yehova ndipo ankaona kuti unali mwaŵi waukulu kumalankhula za Mulungu ndi kumtamanda panthaŵi iliyonse. Poti anali atazoloŵerana kwambiri ndi Yehova, wamasalmoyo anali ndi zinthu zabwino zambiri zosangalalira. (Sal. 35:9) Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo chake chabwinocho?

2 Lankhulani za Yehova Muli Panyumba Panu: Masiku onse Yehova ayenera kukhala mutu wa nkhani pocheza ndi am’banja lathu. Makolo amene amakondadi Yehova amalankhula za iye mwaufulu pogwira ntchito zawo zonse. (Deut. 6:5-7) Akamatero, ana amaona kuti atate ndi mayi wawo amachita zinthu mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo ndi kutinso amakonda chilamulo cha Mulungu. Ndiye anawo aziona phunziro la Baibulo labanja kuti ndiyo njira imene makolo awo amasonyezera kudzipereka kwaumulungu kochokera mumtima.—2 Pet. 3:11.

3 Lankhulani za Yehova ndi Abale Anu: Mlungu uliwonse pochita ntchito zathu zateokrase, timapeza mipata yambiri yodyetsa maganizo athu ndi mitima yathu chakudya chauzimu. Sitimasoŵa zinthu zabwino zonena. (Luka 6:45a) Kodi pali mfundo ina yomwe munatola paphunziro laumwini kapena pakuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu imene inakusangalatsani kwenikweni? Kambitsiranani yomweyo ndi abale anu, choncho mukumawathandiza kukonda Yehova kwambiri.—Sal. 35:18; Aheb. 10:24.

4 Uzani Ena za Yehova: Masiku onse pochita ndi anthu—kuntchito, kusukulu, ndi apabanja osakhulupirira—ayenera kumaoneratu kuti cholinga chathu m’moyo ndicho kuchitira umboni za Yehova. M’malo moti mawu athu aziipitsidwa ndi mawu oipa ndi opanda ulemu a kudziko, zonena zathu zizikhala zotamanda Mulungu. Masiku onse, pampata uliwonse, zilankhulani za uthenga wabwino umene iye watituma kuti tiulalike.—Mac. 5:42; Akol. 4:6.

5 Monga olambira Yehova oona, tiyeni tizigwiritsira ntchito mpata uliwonse kulankhula za Mulungu wathu wosayerekezerekayo, Yehova.—Sal. 106:47.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena