Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/98 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya April

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya April
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira April 6
  • Mlungu Woyambira April 13
  • Mlungu Woyambira April 20
  • Mlungu Woyambira April 27
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 4/98 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya April

Mlungu Woyambira April 6

Nyimbo Na. 27

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kumbutsani onse za malo ndi nthaŵi ya Chikumbutso Loŵeruka, April 11. Mbiri Yateokrase.

Mph. 15: “Utumiki Wathu—Umboni wa Chikondi Choona.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zachidule zochokera mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1987, masamba 26-7, ndime 3-7.

Mph. 20: “Magazini Amalengeza Ufumu.” Mkulu apenda nkhaniyo ndi ofalitsa atatu kapena anayi amene amatha bwino kugaŵira magazini. Kambitsiranani mbali zokopa za magazini atsopano, mukumatchula njira zimene mfundozo zingaphatikizidwire m’maulaliki athu. Lingalirani mmene mungawonjezere kugaŵira magazini m’gawo lanu. Mukumagwiritsira ntchito makope atsopano, sonyezani nkhani zomwe zimadzutsa chidwi, monga zija zonena za mavuto a kakhalidwe, banja, kapena mavuto akumaloko. Khalani ndi zitsanzo zachidule ziŵiri kapena zitatu za maulalikiwo. Tchulani chopereka cha masiku onse cha magaziniwo.

Nyimbo Na. 205 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 13

Nyimbo Na. 90

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Pezekani pa Misonkhano ‘Koposa.’” Mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilola, fotokozani mfundo zazikulu zopezeka m’buku la Uminisitala Wathu, masamba 64-5. Ayamikireni kwambiri onse amene amapezeka pamisonkhano nthaŵi zonse.

Nyimbo Na. 119 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 20

Nyimbo Na. 5

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Fotokozani kuti sikuchedwa kwambiri ngati mufuna kufunsira upainiya wothandiza m’May.

Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani ya mkulu amene mokoma mtima atchula njira zotsimikizika za mmene angawongolere zinthu pampingopo.

Mph. 25: “Kulemba Lipoti la Nthaŵi ya Utumiki Wathu Wakumunda Molondola.” Nkhani ya mlembi ya mafunso ndi mayankho. Limbikitsani onse kupereka lipoti nthaŵi zonse ndiponso lolondola.

Nyimbo Na. 109 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 27

Nyimbo Na. 100

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lengezani maina a amene adzachita upainiya wothandiza m’May. Fotokozani makonzedwe enanso amene mukupanga pampingo panu a kukumana kwa utumiki. Tchulani njira zothandiza zokonzekera maulaliki ogaŵira magazini atsopano.—Onani Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996, tsamba 8.

Mph. 15: Mmene Abusa Achikristu Amakutumikirirani. Nkhani ya mkulu, yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya March 15, 1996, masamba 24-7.

Mph. 18: Khalani ndi Maganizo Abwino Polalikira m’Gawo Logwiridwamo Ntchito Kaŵirikaŵiri. Mkulu akukambitsirana zimenezi ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu amene alefuka chifukwa chakuti anthu ambiri sakuwalandira m’gawo limene lagwiridwamo ntchito mobwerezabwereza. Apenda nawo Nsanja ya Olonda ya July 15, 1988, masamba 16-19, ndime 4-14. Akambitsirana motsimikiza za njira zogwiritsira ntchito malingalirowo kwawoko.

Nyimbo Na. 191 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena