Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/98 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya July

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya July
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira July 6
  • Mlungu Woyambira July 13
  • Mlungu Woyambira July 20
  • Mlungu Woyambira July 27
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 7/98 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya July

Mlungu Woyambira July 6

Nyimbo Na. 110

Mph. 10: Zilengezo zapampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani za lipoti la utumiki wakumunda la April, la dziko ndi la mpingo wanu. Mbiri Yateokrase.

Mph. 15: “Nkwabwinotu Kwambiri Kupezekapo Nthaŵi Zonse!” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zochokera mu Galamukani! yachingelezi ya June 8, 1988, masamba 19-21, kuti mulimbikitse achinyamata kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse.

Mph. 20: “Anansi Athu Afunikira Kumva Uthenga Wabwino.” Konzani kuti ofalitsa aŵiri kapena atatu aluso apende njira zakugaŵira mabrosha angapo amene mpingo uli nawo m’sitoko. Fotokozani chifukwa chake mabroshawo angalandiridwe m’dera lanu. Gogomezerani kufikira cholinga chakuyamba phunziro la Baibulo ndi brosha lakuti Mulungu Amafunanji kapena ndi buku la Chidziŵitso. Chitirani chitsanzo ulaliki woyamba kenako ulendo wobwereza ndi mmene tingampemphere munthu kuyamba naye phunziro. Ligaŵireni pachopereka chanthaŵi zonse.

Nyimbo Na. 73 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 13

Nyimbo Na. 116

Mph. 10: Zilengezo zapampingo. Lipoti la maakaunti. Limbikitsani onse kuganiza mwamphamvu zakulembetsa upainiya wothandiza m’August, poti mudzakhala mapeto a milungu asanu.

Mph. 15: Zosoŵa zapampingo.

Mph. 20: Kodi Mzimu wa Dziko Ukukuipitsani? Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1997, masamba 25-9.

Nyimbo Na. 182 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 20

Nyimbo Na. 18

Mph. 10: Zilengezo zapampingo. Pendani Bokosi la Mafunso.

Mph. 12: “Kucheza Kumene Kungakhale Dalitso.” Akulu aŵiri akukambitsirana. Fotokozani zolinga za ntchito yaubusa zimene zalongosoledwa mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, masamba 20-3. Limbikitsani mpingo mowasonkhezera kuti aziyembekezera akulu kuwachezera.

Mph. 23: “Utumiki  Waupainiya—Kodi Ngwoyenera Inu?” (Ndime 1-11) Woyang’anira utumiki akuyamba mwa kulankhulapo mwachidule, namalimbikitsa onse kuganiza mwamphamvu za upainiya wokhazikika. Kenaka akulongosola za funso 1, kuphatikizapo ndemanga yoneza za nkhani yakuti “Mzimu Wachimwemwe Waupainiya,” mu 1998 Yearbook, patsamba 104-5. Ofalitsa aŵiri kapena atatu a mumpingowo akumpeza papulatifomu nkuyamba kukambitsirana funso 2. Akuuzana njira zabwino, zotheka, za mmene munthu angachitire upainiya popanda kuvutika mwakuthupi. Ndiyeno makolo aŵiri afikaponso pakaguluko nkuyamba kukambitsirana funso 3. Akupereka zifukwa zabwino zimene achinyamata ayenera kulingalira mwamphamvu ntchito ya utumiki wanthaŵi zonse. Limbikitsani onse kudzakhalapo pa Msonkhano Wautumiki mlungu wamaŵa, kudzakambitsirana mafunso otsalawo.

Nyimbo Na. 80 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 27

Nyimbo Na. 155

Mph. 10: Zilengezo zapampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda a July. Lengezani makonzedwe a utumiki a mapeto a mlungu oyamba m’August, ndiyeno limbikitsani onse kuti adzatengemo nawo mbali. Pendani “Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.”

Mph. 15: “Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wakuti ‘Njira ya Moyo ya Mulungu.’” Mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mlembi.

Mph. 20: “Utumiki Waupainiya—Kodi Ngwoyenera Inu? (Ndime 12-21) Nkhani ndi kukambitsirana yokambidwa ndi mkulu. Konzekerani pasadakhale kuti apainiya ndi ena amene anachitapo upainiya kale adzasimbe nkhani zochokera mumtima poyankha mafunso 4-5. Agogomezere kuti nkofunika kukhala ndi ndandanda yabwino nkumaitsatira, namapereka zitsanzo za ndandanda yotsatirika ya utumiki yamlungu uliwonse imene imathandizadi. Mkuluyo akumaliza ndi nkhani yosonkhezera imene ikuyankha funso 6. Chiyambi cha chaka chautumiki pa September 1 ndiyo nthaŵi yabwino yoti apainiya atsopano ayambe utumiki wawo wanthaŵi zonse. Angapeze mafomu kwa wina aliyense wa Komiti Yautumiki Yampingo.

Nyimbo Na. 51 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena