Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu July ndi August: Mungagwiritsire ntchito lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabrosha akuti Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Prolems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? mungawagaŵire pamene kuli koyenera. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kumene tapeza anthu ochita chidwi, tingagaŵire masabusikripishoni paulendo wobwereza.
◼ Poti m’mwezi wa August muli mapeto a milungu asanu, ndi nthaŵi yabwino yoti ambiri angachite upainiya wothandiza.
◼ Kuyambira m’September, oyang’anira madera azidzakamba nkhani yamutu wakuti “Kodi Mukuyenda ndi Mulungu?”
◼ Mu Utumiki Wathu Waufumu wa March 1998, tinalengeza kuti ku Chilumba kudzakhala Msonkhano Wachigawo, komwe mipingo yonse ya m’Dera la M-1 inasankhidwa kukakhala nawo kumeneko. Komabe, chifukwa cha vuto lina limene sitikanatha kuchitira mwina, msonkhano umenewo sudzachitika. Mipingo yonse imene ikanakakhala nawo kumeneko taiuza za msonkhano umene tsopano taisankhirako.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? —Chingelezi
Mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 1997 —Chingelezi
◼ Makompakiti Disiki Amene Alipo
Kingdom Melodies No. 7