Bokosi la Mafunso
◼ Kodi njira yoyenera yoonera malonda mumpingo ndi yotani?
Ngati tikudziŵa bwino cholinga cha misonkhano yathu ndi cha kuyanjana ndi abale athu, funso limeneli silovuta kuyankha. Timafika pamisonkhano ndi kuyanjana ndi abale athu kuti tilimbikitsane mwauzimu. (Aheb. 10:23-25) Choncho, kungakhale kosayenera kuyambitsa chilichonse, kuphatikizapo malonda, omwe angasemphane ndi zifukwa za m’Malemba za kusonkhana kwathu.
Mtumwi Paulo, atatha zaka zitatu ali mumpingo wa ku Efeso, ananena ndi chikumbumtima chabwino kuti: “Sindinasirira siliva, kapena golidi, kapena chovala cha munthu aliyense.” (Mac. 20:33) Si kokha kuti Paulo anakana kukhumbira zinthu za wina koma sanafunenso kugwiritsira ntchito choonadi kumpindulira ndalama.
Nyumba za Ufumu kapena phunziro la Baibulo la pagulu kapena pamisonkhano ya Mboni za Yehova sindiwo malo oti munthu achitirepo malonda ake iyayi, kapena malo ofunirapo anthu owalemba ntchito, koma ali malo okambitsiranapo zinthu zauzimu ndi kuyanjana misonkhano isanayambike, ili mkati ndi pambuyo pa misonkhano. Chotero, kuipitsa ukoma wauzimu wa mayanjano achikristu mwa kuchitapo malonda kungasonyeze kusayamikira zinthu zauzimu ngakhale pang’ono.
Ena, poona kuti abale ena amalephera kugula kamera, amachita bizinesi yojambula zithunzi pamisonkhano yachigawo ndi pamisonkhano ina ya anthu a Yehova. Sikuti abale akamajambulana pamisonkhano yapadera imeneyi akulakwa iyayi. Ngati mbale watijambula nkutipempha kupereka ndalama za filimu ndi zotsukitsira, imeneyo si bizinesi iyayi. Komabe, ambiri amene amajambula zithunzi amapindula nazo, ndiye kuti akuchita malonda. Asamaipitse ukoma wauzimu wa mayanjano achikristu mwa kuchitapo malonda ndipo ifenso tisamawapemphe kuti atijambule. Nchimodzimodzinso ndi malonda ena alionse. Cholinga cha misonkhano yathu nchakulambira Yehova basi, kudya pathebulo yake yauzimu ndi kulimbikitsana.—Aroma 1:11, 12.