Tinapindula ndi Misonkhano Yachigawo ya “Njira ya Moyo ya Mulungu”
1 Miyezi yochepa yapitayo, tinali kukonzekera kupita ku Misonkhano Yachigawo ndi Yamitundu Yonse ya 1998 yakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu.” Tsopano misonkhano imeneyo ndi zochitika zosaiwalika m’mbiri yateokrase ya gululi. Tinasangalala kwambiri ndi chakudya chauzimu chokwana bwino chimene tinalandira pamisonkhano yabwino imene ija.
2 Kunalidi kosangalatsa kuti misonkhano ya chaka chino inaphatikizapo zochitika za m’maiko ena. Kaya amishonale ndi nthumwi za maiko ena zinaliko ku msonkhano umene ife tinapita kapena kunalibe, tonsefe tinamva zokumana nazo zabwino pa Lachisanu masana m’nkhani yakuti “Kutumikira m’Munda wa Amishonale.” “Malipoti Akupita Patsogolo kwa Ntchito Yotuta” omwe anali kuperekedwa tsiku lililonse anali olimbikitsa kwambiri.
3 Zotulutsidwa Zatsopano Zabwino: Nkhani yomalizira pa Lachisanu inayankha funso limene anthu ochuluka amene sadziŵa choonadi afunsapo: “Kodi Kuli Moyo Pambuyo pa Imfa?” Nkhani yosangalatsa kwambiri imene ija inatha mwa kutulutsa brosha latsopano lakuti, What Happens to Us When We Die? Sitikayika kuti mwaliŵerenga pofika tsopano, ndipo mukuona mmene lidzakhalira lopindulitsa m’kuthandiza anthu kuzindikira choonadi ponena za mkhalidwe wa akufa ndi kutonthoza ofedwa ndi chiyembekezo cha chiukiriro.
4 Programu ya Loŵeruka masana inatha ndi nkhani yakuti “Mlengi—Umunthu Wake ndi Njira Zake.” Inatisonyeza bwino kwambiri mfundo yakuti payenera kukhala Mlengi. Pofuna kutithandiza kuti tithandize ena kuzindikira mfundo imeneyi, buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? linatulutsidwa. Pamene kuli kwakuti likulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi kuyamikira kwathu umunthu wake ndi njira zake, bukuli linakonzedwa makamaka kaamba ka aja amene, ngakhale kuti ndi ophunzira kwambiri mwa kudziko, sakhulupirira Mulungu.
5 Chosankha Chogwira Mtima: Nkhani yothera ya msonkhano uja inagogomezera kuti nkofunika kuti tonsefe ‘Tipitirize Kuyenda m’Njira ya Yehova.’ Pachosankha chija, kunalidi koyenera chotani nanga kulengeza nawo kutsimikiza mtima kwa aliyense payekha kuti adzakhalabe, adzasonyezabe, ndipo adzachirikizabe njira ya moyo ya Mulungu monga njira yopambana! (Yes. 30:21) Tsopano tiyenera kukhala otsimikizira kuchita mogwirizana ndi zosankha zimenezi. Tinalimbikitsidwadi mwauzimu mwa kufika pa Msonkhano wa “Njira ya Moyo ya Mulungu”!