Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 1/15 tsamba 14-19
  • Madalitso Olemerera pa Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Madalitso Olemerera pa Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mukulandiridwa, Inu Nonse Onyamula Kuunika!”
  • Onyamula Kuunika Achichepere
  • Lolani kuunika kuŵale
  • Kukhalapo kwa Kristu ndi Vumbulutso
  • Mabanja Achikristu
  • Sande Masana
  • Bwerani ku Msonkhano Wachigawo wa “Onyamula Kuunika”
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Misonkhano Yosangalatsa Ichirikiza Chiphunzitso Chaumulungu
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Ndani Amene Akutsatira Kuunika kwa Dziko?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Onyamula Kuunika—Kaamba ka Chifuno Chotani?
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 1/15 tsamba 14-19

Madalitso Olemerera pa Misonkhano Yachigawo ya “Onyamula Kuunika”

PAFUPIFUPI zaka 2,700 zapitazo, mneneri Yesaya analemba kuti: “Tawona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu.” (Yesaya 60:2) Mawu amenewo atsimikizira kukhala owona chotani nanga! Komabe, pali chiyembekezo, pakuti Yehova wachititsa kuunika kuti kuŵale. Chaka chathachi, okonda kuunika kwa Mulungu anaitanidwa mwaubwenzi kukafika pa Msonkhano Wachigawo wa “Onyamula Kuunika”.

Programu yamsonkhanowo inaperekedwa choyamba m’June Kumpoto kwa Amereka. M’miyezi yotsatira, inaperekedwanso Kummaŵa ndi Kummadzulo kwa Yuropu, Pakati ndi Kumwera kwa Amereka, Afirika, Asiya, ndi m’zisumbu za nyanja. Awo amene anafikapo chiŵerengero chawo chinafikira mamiliyoni angapo. Ndipo ndiphwando lauzimu lolemerera chotani nanga limene iwo anasangalala nalo!

“Mukulandiridwa, Inu Nonse Onyamula Kuunika!”

M’malo ochuluka msonkhanowo unayamba pa Lachisanu ndipo unatha pa Sande madzulo. Pamene ofika pamsonkhanopo anakhala pamipando yawo pa Lachisanu mmawa, anali ndi chisangalalo cha kumva mbiri yachidule ya njira mu imene kuunika kwa Yehova kwaunikirira moŵala mowonjezereka mkati mwa masiku otsiriza ano. Pambuyo pake wapampando analankhula. Iye anagogomezera kuti Akristu owona ayenera kukhala onyamula kuunika ndipo mwaubwenzi anati: “Mukulandiridwa, inu nonse onyamula kuunika!” Programu yamsonkhano inali kudzathandiza nthumwi kupitirizabe kuŵalitsira kuunika kwa Yehova.

Nkhani yapadera inasonyeza chifuno chamsonkhano wonsewo. Wokamba nkhani ameneyo anakumbutsa ofika pamsonkhano kuti kuunika kunazimitsidwa kwa anthu kalelo m’munda wa Edene. Kuyambira pamenepo, Satana wachititsa khungu anthu, kuti asawone kuunika kwa chowonadi. (2 Akorinto 4:4) Komabe, Yesu anadza monga “kuunika kwa amitundu.” (Yesaya 42:1-6) Iye anavumbula mabodza a chipembedzo, anasonyeza ntchito zolakwa zamdima, nachirikiza uchifumu wa Yehova, ndipo analalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Otsatira a Yesu anachita chomwecho​—ndipo iwo adakachitabe! (Mateyu 28:19, 20) Wokamba nkhaniyo motenthedwa maganizo anati: ‘Ife, mofanana ndi Yesu, tingathe kukhala onyamula kuunika. Palibe ntchito imene iri yofunika kwambiri m’tsiku lathu kuposa imeneyi. Ndipo palibe mwaŵi waukulu kwambiri kuposa umenewu.’

Mwamsanga pamene mbali yoyamba ya programu inali pafupi kutha, panali chosayembekezereka. Tcheyamani wamsonkhano anabwerera papulatifomu nalengeza kutulutsidwa kwa yoyamba ya mpambo wa matrakiti atsopano anayi. Kuwomba m’manja waa waa waa kotenthedwa maganizo kunatsagana ndi chochitika chimenechi, ndipo kope limodzi la trakiti limeneli linachititsidwa kukhala lopezeka kwa nthumwi iriyonse imene inalipo.

Pa Lachisanu masana, programu yamsonkhano inapereka uphungu waukulu kwa Akristu onyamula kuunika. Nkhani ziŵiri zoyambirira zinapereka uphungu wabwino kwambiri ponena za mmene kuipitsidwa ndi mdima wa dziko kungapeŵedwere. Popeza kuti Satana angawonekere kukhala mngelo wa kuunika, kuli kofunika kusunga lingaliro lauzimu kotero kuti zinthu zonyansa za dzikoli sizikutinyenga. (2 Akorinto 11:14) Paulo anapereka uphungu wakuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Nthumwi zamsonkhano zinamva kuti kusandulizidwa kwa Mkristu ndiko mchitidwe wosalekeza. Maganizo athu amayeretsedwa mosalekeza ndipo amaumbidwa pamene tiphunzira Mawu a Mulungu ndi kugwiritsira ntchito zimene tiphunzira. Chotero, timafikira kukhala ofanana ndi Yesu mowonjezereka, amene anali “wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.”​—Yohane 1:14.

Onyamula Kuunika Achichepere

Theka lachiŵiri la madzulo a Lachisanu linalunjikitsidwa kwa achichepere. Nkhani yoyamba yakuti (“Achichepere​—Kodi Mukulondola Chiyani?”) inayamikira Akristu achichepere amene ali chitsanzo chabwino cha kukhulupirika. Koma inawakumbutsa kuti iwo ali chandamale chenicheni cha Satana. Ngakhale katswiri wothamanga wophunzitsidwa bwino lomwe afunikira mphunzitsi. Mofananamo, achichepere afunikira chithandizo cha makolo awo ndi cha mpingo kuti apitirizebe kuyenda m’kuunika.

Izi zinagogomezeredwa ndi drama labwino kwambiri lakuti Kuchita Chimene Chiri Chabwino Pamaso pa Yehova, limene linamaliza programu ya Lachisanu. Chogogomezeredwa chinali chitsanzo cha Mfumu Yosiya. Ngakhale monga mnyamata wachichepere, iye anali wotsimikiza kutumikira Yehova. Zisonkhezero zoipa zinalipo momzinga, koma chitsogozo cha mkulu wa ansembe Hilikiya ndi chifukwa cha kukonda kwake Chilamulo cha Mulungu, Yosiya anachita chimene chinali cholungama m’maso mwa Yehova. Achichepere Achikristu lerolino achitetu chomwecho.

Lolani kuunika kuŵale

Pambuyo pakupuma usiku, nthumwi zinadza kumsonkhano pa Loŵeruka mmawa ziri zokonzekera kulandira uphungu wina wolimbikitsa Wamalemba. Iwo sanali ogwiritsidwa mwala. Pambuyo pakukambitsiridwa lemba latsiku, programu inapitiriza ndi nkhani yosiyirana imene inasanja njira zosiyanasiyana zimene Mkristu angachititsire kuunika kwake kuŵala. (Mateyu 5:14-16) Njira imodzi yofunika ndiyo kulalikira, ndipo khalidwe labwino nalonso liri ndi mbali yofunika. Monga momwe wokamba nkhaniyo ananenera, “kulalikira kumauza ena zimene timakhulupirira, koma kugwiritsira ntchito chikondi kumakuchitira chitsanzo.”

Pamenepo chothandizira kulalikira chofunika chinasonyezedwa kwa ofika pa msonkhano​—matrakiti. Popeza chilengezo cha tsiku lapitalo chinali chisanaiŵalike m’maganizo, nthumwizo zinamva zokumana nazo zotsimikizira mmene ziŵiya zazing’ono zimenezi ziriri zamphamvu. Nthumwizo zinalimbikitsidwa kukhala nawo mtokoma wa amenewa nthaŵi zonse, ali okonzekera pa nthaŵi iriyonse.

Kenako chisamaliro chinasumikidwa pa apainiya, olengeza Ufumu a nthaŵi yonse amenewo amene amagwira ntchito zolimba m’kunyamula kuunika. Timayamikira chotani nanga apainiya athu ogwira ntchito zolimba! Ndipo chiŵerengero chawo chikuwonjezereka. Ngakhale m’maiko kumene ufulu wa kulambira wangoperekedwa kumene posachedwapa, ziŵerengero za apainiya zikukula. Apainiya analimbikitsidwa kuyamikira mwaŵi wawo. Awo amene sanayambe kuchita upainiya analimbikitsidwa kupenda mkhalidwe wawo. Mwinamwake nawonso akalinganiza mikhalidwe yawo kuti alole kuunika kwawo kuŵala muutumiki wa nthaŵi yonse.

Kaŵirikaŵiri kukhala wonyamula kuunika kumaphatikizapo kudzimana, ndipo izi zinafotokozedwa m’nkhani yotsatira yakuti “Kutumikira Yehova ndi Mzimu Wodzimana.” Paulo anadandaulira kuti: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu.” (Aroma 12:1) Mzimu wodzimana umasonyezedwa ndi awo amene amapirira chizunzo. Apainiya amadzimana tsiku lirilonse kuti akhalebe muutumiki wa nthaŵi yonse. Ndithudi, Akristu owona onse amadzimana, akumadzitanganitsa muutumiki wa Yehova mmalo mwa kulondola zikhumbo zadyera, zokondetsa zinthu zadziko za dziko lino. Njira yotero imadzetsa dalitso lolemerera lochokera kwa Yehova.

Nkhani imeneyo inatumikira monga mawu oyamba oyenerera pa zimene zinatsatira​—nkhani ya ubatizo. Awo amene anabatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Onyamula Kuunika” sadzaiŵaladi nkhani imeneyi. Ubatizo wawo nthaŵi zonse udzakhala mbali yaikulu ya moyo wawo. Iwo anakumbutsidwa kuti anali kutsatira chitsanzo cha Yesu Kristu, amene anabatizidwa pa msinkhu wa zaka 30. Ndiponso, oyembekezera ubatizo anali okondwera kukumbukira kuti anali “atavula ntchito za mdima” ndipo anali atapanga chosankha cha “kutumikira Yehova.” (Aroma 12:11; 13:12) Mwachisangalalo iwo anaimirira pamaso pa khamu lamsonkhano ndipo anapanga chilengezo chapoyera mofuula asanapite ku ubatizo. (Aroma 10:10) Tikupempherera dalitso la Yehova kukhala ndi onse amene anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Iye mwa kuloŵa ubatizo wa m’madzi pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Onyamula Kuunika.”

Loŵeruka masana inali nthaŵi ya machenjezo osabisa mawu. Amenewa anadza mu mpangidwe wa nkhani zakuti: “Peŵani Misampha ya Umbombo,” “Kodi Pali Amene Akukuwonongerani Makhalidwe Okoma?” Ndi “Peŵani Kupembedza Mafano kwa Mtundu Uliwonse.” Nkhani zitatu zimenezi zinasonyeza maluso ena ogwiritsidwa ntchito ndi Satana kufoketsa Mkristu. Yudase Isikariote anali mtumwi, koma anapereka Yesu chifukwa cha ndalama. Samueli wachichepere anakulira pamalo apakati enieni a kulambirira Yehova, komabe mosapeŵeka iye anali ndi oyanjana nawo ena oipa kwambiri. (1 Samueli 2:12, 18-20) Kulambira mafano kungaphatikizepo zinthu zonga chisembwere ndi kusirira. (Aefeso 5:5; Akolose 3:5) Inde, umbombo, mayanjano oipa, ndi kulambira mafano nzaupandu ndipo ziyenera kupeŵedwa.

Pamenepo programu yamsonkhano inasinthira ku nkhani zina, kunena kwake titero. Nkhani yotsatira inadzutsa mafunso angapo a Baibulo okondweretsa ndipo inawayankha. Mwachitsanzo, kodi mungafotokoze kuti kaya anthu amene sakuvomereza chowonadi ndi kufa chisautso chachikulu chisanakanthe adzaukitsidwa? Kodi Mkristu angachitenji ngati satha kupeza wokwatirana naye woyenera? Kuzamitsa chidziŵitso chawo cha Baibulo, nthumwizo zinalimbikitsidwa kugwiritsira ntchito mokwanira Watch Tower Publications Index, makamaka pa mutu wakuti “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga.”

Kukhalapo kwa Kristu ndi Vumbulutso

Mbali yotsirizira ya programu ya Loŵeruka inasumika pa ulosi mwa nkhani yosiirana yakuti “Kusumika Kuunika pa Kukhalapo kwa Kristu ndi Vumbulutso.” Mbali za “chizindikiro” zotsimikizira kukhalapo kwa Yesu Kristu zinapendedwa. (Mateyu 24:3) M’nkhani yachiŵiri, ntchito zamakono za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” zinakambitsiridwa. (Mateyu 24:45-47) Kunatchulidwa kuti kuyambira 1919 kagulu ka kapolo katsogoza mokhulupirika ntchito yolalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Ndiyeno khamu lalikulu linasonkhanitsidwa lochokera m’mitundu yonse kukhala ndi phande limodzi ndi Akristu odzozedwa m’kusonyeza kuunika kwa Yehova. Wokamba nkhaniyo anamaliza mwakumati: “Onse apitirizetu mwachangu kuchirikiza kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Kuli kokha mwakuchita zimenezi kuti tsiku lina mwamsanga onse onga nkhosa adzakhoza kumva mawu achimwemwe akutiwo: ‘Idzani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga, loŵani ufumu wokonzedwera inu kuchokera pa chikhazikiro cha dziko.’”​—Mateyu 25:34.

Wolankhula womalizira anafotokoza matanthauzo ndi zolinga za kuvumbulitsidwa kwa Yesu Kristu. (1 Akorinto 1:7) Nchochitika chothutsa mtima chotani nanga chimene chivumbulutsocho chidzakhala! Babulo Wamkulu adzawonongedwa. Nkhondo yaikulu pakati pa dziko la Satana ndi Yesu ndi angelo ake idzatsirizira m’chiwonongeko cha dongosolo lino. Potsirizira pake, Satana mwiniyo adzaikidwa kuphompho ndi kuchititsidwa kusagwira ntchito. Koma padzakhala mpumulo kwa anthu a Mulungu, pamene kudzachitika ukwati wa Mwanawankhosa kumwamba ndi kubweretsa dziko lapansi latsopano. Wokamba nkhaniyo anakondweretsa omvetsera ake mwa kutulutsa brosha latsopano lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Lidzakhala chithandizo chabwino kwambiri chotani nanga kwa anthu odzichepetsa amene afunikira kudziŵa za Mlengi wathu wosamala ndi zifuno zake kwa ife!

Mabanja Achikristu

Sande, tsiku lomaliza lamsonkhanowo, tsopano linafika. Komabe, zambiri zinalinkudza. Pambuyo pa kukambitsiridwa kwa lemba latsiku, chisamaliro chinaperekedwa ku banja Lachikristu ndi nkhani yosiirana yakuti “Kusamalirana m’Banja Lachikristu.” Mbali yoyamba inathandiza ofika pamsonkhano kuzindikira chinsinsi chakukhala ndi banja Lachikristu lachipambano: kuika zinthu zauzimu pachiyambi. Mbali yachiŵiri inalimbikitsa mabanja kuchitira zinthu pamodzi, kaya zimenezo zikuphatikizapo kufika pamisonkhano, utumiki wakumunda, phunziro labanja, kapena kusanguluka. Ndipo mbali yachitatu ya nkhani yosiiranayo inakumbutsa nthumwizo za moyo wawo ndi thayo lakusamalira okalamba. “Abale athu ndi olongo okalamba ali chithandizo ku mpingo,” anatero wokamba nkhaniyo. Tiyeni tiyamikire chidziŵitso chawo ndi kutsanzira umphumphu wawo.

Kenako tanthauzo la mawu akutiwo “kulama maganizo” anapendedwa. (1 Petro 4:7) Munthu amene ali wolama m’maganizo ngwokhazikika, ngwolingalira, ngwosankitsa, ngwodzichepetsa, ndipo ngwanzeru. Iye angalekanitse pakati pa cholungama ndi chosalungama, chowona ndi chonama. Ndiponso, iye amayesayesa kusunga thanzi labwino lauzimu.

Nkhani yomaliza paprogramu yammaŵa pa Sande inafotokoza kugonjera kwathu Mulungu ndi Kristu. “Kufunika kwa kukhala m’chigonjero chokhulupirika kwa Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, sikungathe kugogomezeredwa mopambanitsa,” anatero wokamba nkhaniyo. Iye anapitiriza kusonyeza mmene izi zimayambukirira mbali iriyonse ya miyoyo yathu. Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kukhala m’chigonjero? Mikhalidwe inayi: chikondi, mantha aumulungu, chikhulipiriro, ndi kudzichepetsa.

Sande Masana

Ndiyeno, linali Sande masana ndi nthaŵi ya kamthemuthe wa programu yamsonkhanowo. Kwa ochuluka, kunawonekera ngati kuti msonkhanowo unali utangoyamba kumene, ndipo unali kufika kale kumapeto ake.

Nkhani yapoyera inali ndi mutu wakuti: “Tsatirani Kuunika kwa Dziko.” Amene analipo anamva malongosoledwe ochititsa chidwi a ntchito ya kuunika kwakuthupi m’kusungitsa moyo. Pamenepo wokamba nkhaniyo anasonyeza kufunika kokulirapo kwa kuunika kwauzimu. Kuunika kwakuthupi kumatipangitsa kupitirizabe kukhala a moyo kwa zaka makumi angapo, koma kuunika kwauzimu kungathe kutipangitsa kupitirizabe kukhala ndi moyo ku umuyaya wonse. Mbali yaikulu ya nkhaniyo inali kukambitsirana kwa vesi ndi vesi kwa Yohane 1:1-16, pamene Yesu akusonyezedwa kukhala kuunika kwa dziko. Lerolino, m’zaka zomalizira za dongosolo loipa lazinthu lino, kuli kofulumira kwambiri koposa ndi kale lonse kutsatira Yesu m’ntchito imeneyi.

Pambuyo pa chidule cha Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu umenewo, inali nthaŵi ya nkhani yomaliza. Mwachimwemwe, wolankhulayo anasonyeza kuti pali zinthu zambiri za kuziyang’anira m’masiku amtsogolo. Mwachitsanzo, iye analengeza kaseti yatsopano ya drama lakuti Kuchita Chifuniro cha Mulungu Mwachangu. Ndipo sizinali zokhazo. Kunali kudzakhala mpambo watsopano wa makaseti a vidiyo a mutu wakuti The Bible​—A Book Of Fact and Prophecy, yoyamba ya nkhani yakuti The Bible​—Accurate History, Reliable Prophecy.

Potsirizira, wokamba nkhaniyo analengeza kuti kudzakhala misonkhano yachigawo ya masiku anayi mu 1993, kuphatikizapo misonkhano yamitundu yonse yapadera mu Afirika, Asiya, Yuropu, ndi Kumwera kwa Amereka. Ngakhale kuti Msonkhano Wachigawo wakuti “Onyamula Kuunika” unalinkutha, nthumwizo zinali zokhoza kuyamba kuchita makonzedwe a chaka chotsatira.

Pamenepo nthaŵi inafika yakuti nthumwi zamsonkhano zibwerere kwawo. Ndithudi, iwo anali otsimikiza kwambiri kuposa ndi kale lonse kupitirizabe kuunikira kuŵalako m’dziko lamdima lino. Pambuyo pa masiku atatu odzala ndi zinthu zabwino zauzimu, mawu alemba lomalizira ogwidwa mawu m’nkhani yomalizira anali atanthauzo lalikulu akutiwo: “Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;  . . Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino; Pakuti chifundo chake nchosatha.”​—Salmo 118:27, 29.

[Chithunzi patsamba 15]

Programu yamsonkhano m’Chirussia

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Ziŵalo za Bungwe Lolamulira zinalankhula pamisonkhano yambiri

Nthumwi zaku Japan zinali pakati pa osonkhana mu St. Petersburg, Russia

Drama la Baibulo lothutsa mtima linagogomezera kufunika kwa kuchita cholungama pamaso pa Yehova

Onyamula kuunika atsopano anasonyezera kudzipatulira kwawo kwa Yehova mwakubatizidwa

Osonkhanawo anatchera khutu kumvetsera programu ku St. Petersburg

[Chithunzi patsamba 18]

Nthumwi zinasangalala kulandira brosha latsopano lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena