Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/98 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 10/98 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kumene tapeza anthu ochita chidwi, tingagaŵire masabusikripishoni paulendo wobwereza. November: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. January: Lililonse la mabuku a masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo lofalitsidwa isanafike 1985. Mipingo imene ilibe mabuku ameneŵa ingagaŵire buku lakuti Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.

◼ Mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu uno ndi “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki.” Iyenera kusungidwa kuti izidzagwiritsiridwa ntchito chaka chonse cha 1999.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1999 paoda yawo ya mabuku ya October. Timabukuti tidzakhalako m’Chicheŵa ndi m’Chingelezi. Mpaka pamene timabukuti tidzakhalapo ndi kutumizidwa, tidzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu ya mipingo. Timabuku ta Kusanthula Malemba ndi zinthu za oda yapadera.

◼ Mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1998 yachicheŵa m’ndime 9, pamasamba 9 ndi 10, muli mbali zolakwika chifukwa cha kuphophonya panthaŵi ya kusindikiza. Chonde, sinthani masentensi otsatirawa amene akukhudzidwa.

Funso lakuti: “Kodi anali ndi mzimu wosafa umene tsopano unatumizidwa ku helo wamoto chifukwa cha tchimo lawo?” likhale lakuti: “Kodi anali ndi mbali ina yosafa imene tsopano inatumizidwa ku helo wamoto chifukwa cha tchimo lawo?” Ndiyeno sinthani masentensi atatu otsatira lemba la “Genesis 2:7” kuti akhale otere: “Munthu sanapatsidwe chinthu china chamoyo; iye anakhala wamoyo, munthu wamoyo. (1 Akorinto 15:45, NW) Eya, si Adamu yekha amene anali “wamoyo” koma, monga momwe Chihebri chikusonyezera, chinenero chimene Genesis analembedweramo, nazonso nyama wamba zinali “zamoyo”! (Genesis 1:24) Adamu ndi Hava atamwalira, sanakhalenso amoyo.” Funso 9 likhale lakuti: “(a) Kodi choonadi nchiti ponena za munthu? (b) Kodi nchiyani chimachitikira munthu akafa?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena