Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokrase ya 1999
Malangizo
Mu 1999, otsatiraŵa ndiwo adzakhala makonzedwe pochititsa Sukulu Yautumiki Wateokrase.
MABUKU OPHUNZIRA: Revised Nyanja (Union) Version [bi53], Nsanja ya Olonda [w-CN], Galamukani! [g-CN], Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokrase [sg-CN], Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja [fy-CN], ndi Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN] adzakhala magwero a nkhani zimene zidzagaŵiridwa.
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno kupitiriza motere:
NKHANI NA. 1: Mphindi 15. Imeneyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira, ndipo idzatengedwa mu Nsanja ya Olonda, Galamukani!, kapena mu Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokrase. Ngati yatengedwa mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!, iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 15 yopanda mafunso obwereramo; ngati yatengedwa mu Buku Lolangiza la Sukulu, ikambidwe ngati nkhani yachilangizo ya mphindi 10 mpaka 12, kenako mphindi 3 mpaka 5 za mafunso obwereramo, kugwiritsira ntchito mafunso osindikizidwa m’bukulo. Cholinga chake sichiyenera kukhala cha kungokamba nkhaniyo koma kusamalira kwambiri za phindu lenileni la chidziŵitso chimene chikufotokozedwa, mukumagogomezera mfundo zomwe zidzakhala zothandiza kwambiri mpingowo. Gwiritsirani ntchito mutu wosonyezedwa.
Abale opatsidwa nkhani imeneyi ayenera kukhala osamala kusunga nthaŵi. Ngati apatsidwa uphungu wamseri, pasilipi yawo ya uphungu wakulankhula pangalembedwe mfundo zoyenera.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 6. Nkhaniyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira amene adzagwiritsira ntchito mfundozo pazosoŵa za kumaloko. Siyenera kukhala chidule wamba cha kuŵerenga kwa mlunguwo. Choyamba perekani chithunzi chachidule cha machaputala onse a mlunguwo pa masekondi 30 mpaka 60. Komabe, cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvetsera kuzindikira chifukwa chake komanso mmene chidziŵitsocho chilili chaphindu kwa ife. Ndiyeno woyang’anira sukulu adzauza ophunzirawo kupita kumakalasi awo osiyanasiyana.
NKHANI NA. 2: Mphindi 5. Iyi ndi nkhani ya kuŵerenga Baibulo kwa mbali yogaŵiridwa kochitidwa ndi mbale. Nkhaniyi idzakambidwa m’sukulu yaikulu limodzinso ndi m’timagulu tinato. Kaŵirikaŵiri mbali zoŵerenga zimakhala zazifupi mololeza wophunzira kukamba mawu oyamba ndi omaliza achidule opereka chidziŵitso pankhaniyo. Zingaphatikizepo mbiri yakale, tanthauzo la ulosi kapena la chiphunzitso, ndi mmene mapulinsipulo angagwirire ntchito. Mavesi onse ogaŵiridwa ayenera kuŵerengedwa mosalekeza. Koma pamene mavesi owaŵerenga saali ondondozana, wophunzira angatchule vesi lopitirizira kuŵerengako.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhaniyi idzapatsidwa kwa mlongo. Idzatengedwa m’buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, kapena Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Chochitikacho chingakhale umboni wamwamwayi, ulendo wobwereza, kapena phunziro la Baibulo la panyumba, kapena njira ina iliyonse yochitira utumiki wakumunda. Nthaŵi zina, zingakhale ngati kuti kholo likuphunzitsa mwana wamng’ono. Okambawo angakhale pansi kapena kuimirira. Woyang’anira sukulu adzafuna makamaka kuona mmene wophunzirayo adzathandizira mwini nyumba kusinkhasinkha ndi kumvetsetsa nkhaniyo ndi mmene adzagwiritsira ntchito malemba. Wophunzira wopatsidwa nkhani imeneyi ayenera kudziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi, koma mukhoza kugwiritsira ntchito wothandiza winanso. Wophunzirayo ndiye angasankhe kuti kaya amlole mwini nyumba kuŵerenga ndime zina kapena ayi pamene akuphunzira buku la Chimwemwe cha Banja. Chimene chiyenera kusamalidwa kwambiri, si mkhalidwe wa chochitikacho, koma kugwira mtima kwa mfundo zake.
NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Ngati nkhani imeneyi yatengedwa m’buku la Munthu Wamkulu, idzakhala ya mbale kapena mlongo. Ngati yatengedwa m’buku la Chimwemwe cha Banja, idzakhala ya mbale. Nkhani iliyonse mutu wake ulipo kale pandandanda. Ngati idzakhala ya mbale, ayenera kudzaikamba molingalira omvetsera amene ali m’Nyumba ya Ufumuwo. Pamene ipatsidwa kwa mlongo, iyenera kuperekedwa mofanana ndi Nkhani Na. 3.
*NDANDANDA YOWONJEZERA YA KUŴERENGA BAIBULO: Imeneyo taiika m’mabulaketi, pambuyo pa nambala ya nyimbo ya mlungu uliwonse. Mwa kutsatira ndandanda imeneyi, mukumaŵerenga masamba ngati khumi pamlungu, mungaŵerenge Baibulo lonse m’zaka zitatu. Ndandanda ya kuŵerenga yowonjezera imeneyi siili maziko a nkhani za programu ya sukulu kapena kubwereramo kolemba.
CHIDZIŴITSO: Za chidziŵitso china ndi malangizo onena za uphungu, kusunga nthaŵi, kubwereramo kolemba, ndi kukonzekera nkhani, chonde onani patsamba 3 la Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996.
NDANDANDA
Jan. 4 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 16-18
Nyimbo Na. 23 [*2 Mafumu 16-19]
Na. 1: Mmene Mulungu Anauzirira Baibulo (w97-CN 6/15 mas. 4-8)
Na. 2: Chivumbulutso 16:1-16
Na. 3: Tetezerani Mwana Wanu ku Ngozi (fy-CN mas. 61-3 ndime 24-8)
Na. 4: Kuzindikira Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako (gt-CN mawu oyamba, ndime 1-4)
Jan. 11 Kuŵerenga Baibulo: Chivumbulutso 19-22
Nyimbo Na. 126 [*2 Mafumu 20-25]
Na. 1: sg-CN mas. 5-7 ndime 1-9
Na. 2: Chivumbulutso 22:1-15
Na. 3: Makolo—Perekani Mpata Wolankhulana Mwaufulu (fy-CN mas. 64-6 ndime 1-7)
Na. 4: Kodi Yesu Anakhalakodi? (gt-CN mawu oyamba, ndime 5-11)
Jan. 18 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 1-3
Na. 1: sg-CN mas. 7-8 ndime 10-16
Na. 2: Genesis 1:1-13
Na. 3: Phunzitsani Ana Makhalidwe Abwino ndi Zinthu Zauzimu (fy-CN mas. 67-70 ndime 8-14)
Na. 4: Kodi Yesu Anali Yani Kwenikweni? (gt-CN mawu oyamba ndime 12-15)
Jan. 25 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 4-6
Na. 1: Chenjerani ndi Kukayikira Zolinga za Ena (w97-CN 5/15 mas. 26-9)
Na. 2: Genesis 4:1-16
Na. 3: Chifukwa Chake Chilango ndi Ulemu Zili Zofunika (fy-CN mas. 71-2 ndime 15-18)
Na. 4: Chimene Chinapangitsa Yesu Kukhala Munthu Wamkulu Woposa Onse (gt-CN mawu oyamba ndime 16-19)
Feb. 1 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 7-9
Nyimbo Na. 108 [*1 Mbiri 14-21]
Na. 1: Nkhani ya Baibulo Yonena za Chigumula Njoona (g97-CN 2/8 mas. 18-19)
Na. 2: Genesis 7:1-16
Na. 3: Phunzitsani Ana Mmene Mulungu Amaonera Ntchito ndi Kuseŵera (fy-CN mas. 72-5 ndime 19-25)
Na. 4: Kodi Nchifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira za Yesu Ndipo Tingaphunzire Bwanji? (gt-CN mawu oyamba ndime 20-23)
Feb. 8 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 10-12
Nyimbo Na. 132 [*1 Mbiri 22-29]
Na. 1: Choonadi Ponena za Bodza (g97-CN 3/8 mas. 17-19)
Na. 2: Genesis 12:1-20
Na. 3: Kupanduka kwa Ana ndi Zochititsa Zake (fy-CN mas. 76-9 ndime 1-8)
Na. 4: Gabrieli Aoneka kwa Zakariya ndi kwa Mariya (gt-CN mutu 1)
Feb. 15 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 13-15
Na. 1: Kufooka kwa Anthu Kusonyeza Mphamvu ya Yehova (w97-CN 6/1 mas. 24-7)
Na. 2: Genesis 14:8-20
Na. 3: Yesu Alemekezedwa Asanabadwe (gt-CN mutu 2)
Na. 4: Osalekerera Zinthu Komanso Osaziumitsa Kwambiri (fy-CN mas. 80-1 ndime 10-13)
Feb. 22 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 16-19
Nyimbo Na. 188 [*2 Mbiri 9-17]
Na. 1: Chimene Mapemphero Anu Amavumbula (w97-CN 7/1 mas. 27-30)
Na. 2: Genesis 18:1-15
Na. 3: Kukwaniritsa Zofunika Zazikulu Kungaletse Kupanduka (fy-CN mas. 82-4 ndime 14-18)
Na. 4: Kubadwa kwa Yohane (gt-CN mutu 3)
Mar. 1 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 20-23
Nyimbo Na. 54 [*2 Mbiri 18-24]
Na. 1: Mmene Mungaphunzitsire Chikumbumtima Chanu (w97-CN 8/1 mas. 4-6)
Na. 2: Genesis 23:1-13
Na. 3: Yosefe Akwatira Mariya Wokhala ndi Pakati (gt-CN mutu 4)
Na. 4: Njira Zothandizira Mwana Wolakwa (fy-CN mas. 85-7 ndime 19-23)
Mar. 8 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 24-25
Nyimbo Na. 121 [*2 Mbiri 25-31]
Na. 1: Kodi Choonadi Chimatimasula ku Chiyani? (w97-CN 2/1 mas. 4-7)
Na. 2: Genesis 24:1-4, 10-21
Na. 3: Kubadwa kwa Yesu—Kuti Ndipo Liti? (gt-CN mutu 5)
Na. 4: Kuchita ndi Wopanduka Weniweni (fy-CN mas. 87-9 ndime 24-7)
Mar. 15 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 26-28
Nyimbo Na. 197 [*2 Mbiri 32-36]
Na. 1: Malo a Nyimbo Pakulambira Kwamakono (w97-CN 2/1 mas. 24-8)
Na. 2: Genesis 26:1-14
Na. 3: Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga (fy-CN mas. 90-2 ndime 1-7)
Na. 4: Mwana wa Lonjezo (gt-CN mutu 6)
Mar. 22 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 29-31
Na. 1: Dziko Silidzathera m’Moto (g97-CN 1/8 mas. 30-1)
Na. 2: Genesis 31:1-18
Na. 3: Yesu ndi Openda Nyenyezi (gt-CN mutu 7)
Na. 4: Lingaliro la Mulungu pa Zakugonana (fy-CN mas. 92-4 ndime 8-13)
Mar. 29 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 32-35
Nyimbo Na. 143 [*Ezara 8-Nehemiya 4]
Na. 1: Mulungu Adzachiritsa Anthu Mozizwitsa—Liti? (w97-CN 7/1 mas. 4-7)
Na. 2: Genesis 35:1-15
Na. 3: Thandizani Ana Anu Kusankha Mabwenzi Abwino (fy-CN mas. 95-7 ndime 14-18)
Na. 4: Kuthaŵa Wolamulira Wankhalwe (gt-CN mutu 8)
Apr. 5 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 36-38
Nyimbo Na. 106 [*Nehemiya 5-11]
Na. 1: Chipulumutso—Zimene Chimatanthauza Kwenikweni (w97-CN 8/15 mas. 4-7)
Na. 2: Genesis 38:6-19, 24-26
Na. 3: Moyo Wabanja Woyambirira wa Yesu (gt-CN mutu 9)
Na. 4: Kusankha Zosangalatsa Zabwino Zochitira Limodzi ndi Banja (fy-CN mas. 97-102 ndime 19-27)
Apr. 12 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 39-41
Nyimbo Na. 34 [*Nehemiya 12-Estere 5]
Na. 1: Nkuululiranji Choipa? (w97-CN 8/15 mas. 26-9)
Na. 2: Genesis 40:1-15
Na. 3: Nzeru ya m’Malemba Yothandiza Mabanja a Kholo Limodzi (fy-CN mas. 103-5 ndime 1-8)
Na. 4: Ku Yerusalemu Ali ndi Zaka 12 (gt-CN mutu 10)
Apr. 19 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 42-44
Nyimbo Na. 124 [*Estere 6-Yobu 5]
Na. 1: Chifukwa Chake Tiyenera Kuulamulira Mkwiyo (g97-CN 6/8 mas. 11-13
Na. 2: Genesis 42:1-17
Na. 3: Vuto la Kupeza Ntchito Monga Kholo Limodzi (fy-CN mas. 105-7 ndime 9-12)
Na. 4: Yohane Akonzera Yesu Njira (gt-CN mutu 11)
Apr. 26 Kubwereramo Kolemba. Malizani Chivumbulutso 16-Genesis 44
May 3 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 45-47
Na. 1: Kodi Madyerero a Kututa Amakondweretsa Mulungu? (w97-CN 9/15 mas. 8-9)
Na. 2: Genesis 45:16–46:4
Na. 3: Kupereka Chilango m’Banja la Kholo Limodzi (fy-CN mas. 107-10 ndime 13-17)
Na. 4: Zimene Zikuchitika pa Ubatizo wa Yesu (gt-CN mutu 12)
May 10 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 48-50
Na. 1: sg-CN mas. 9-11 ndime 1-12
Na. 2: Genesis 49:13-28
Na. 3: Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kusungulumwa (fy-CN mas. 110-13 ndime 18-22)
Na. 4: Kutengapo Maphunziro pa Ziyeso za Yesu (gt-CN mutu 13)
May 17 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 1-4
Na. 1: sg-CN mas. 11-13 ndime 13-20)
Na. 2: Eksodo 4:1-17
Na. 3: Ophunzira Oyamba a Yesu (gt-CN mutu 14)
Na. 4: Njira Zothandizira Mabanja a Kholo Limodzi (fy-CN mas. 113-15 ndime 23-7)
May 24 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 5-8
Na. 1: Amphaŵi Komabe Olemera—Zingatheke Bwanji? (w97-CN 9/15 mas. 3-7)
Na. 2: Eksodo 7:1-13
Na. 3: Chozizwitsa Choyamba cha Yesu (gt-CN mutu 15)
Na. 4: Ubwino wa Kudwazika Matenda ndi Maganizo Aumulungu (fy-CN mas. 116-19 ndime 1-9)
May 31 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 9-12
Na. 1: Zimene Kusakhala a Dziko Lapansi Kumatanthauza (g97-CN 9/8 mas. 12-13)
Na. 2: Eksodo 12:21-36
Na. 3: Phindu la Mzimu Wochiritsa (fy-CN mas. 120-1 ndime 10-13)
Na. 4: Changu cha Kulambira Yehova (gt-CN mutu 16)
June 7 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 13-16
Na. 1: Mmene Mungakhalire ndi Chiyembekezo Mutataya Mtima (w97-CN 5/15 mas. 22-5)
Na. 2: Eksodo 15:1-13
Na. 3: Ikani Zinthu m’Malo Ake Ndipo Thandizani Ana Kupirira Matenda m’Banja (fy-CN mas. 122-3 ndime 14-18)
Na. 4: Kuphunzitsa Nikodemo (gt-CN mutu 17)
June 14 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 17-20
Na. 1: Mmene Akristu Amalemekezera Makolo Okalamba (w97-CN 9/1 mas. 4-7)
Na. 2: Eksodo 17:1-13
Na. 3: Yohane Achepa, Yesu Akula (gt-CN mutu 18)
Na. 4: Mmene Tiyenera Kuonera Kuchiritsa ndi Mankhwala (fy-CN mas. 124-7 ndime 19-23)
June 21 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 21-24
Na. 1: Sayansi Yeniyeni ndi Baibulo Zimagwirizana (g97-CN 7/8 mas. 16-7)
Na. 2: Eksodo 21:1-15
Na. 3: Kodi Mkazi Wokhulupirira Angasunge Bwanji Mtendere m’Banja la Zipembedzo Zosiyana? (fy-CN mas. 128-32 ndime 1-9)
Na. 4: Kuphunzitsa Mkazi wa ku Samariya (gt-CN mutu 19 ndime 1-14)
June 28 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 25-28
Na. 1: Dziŵani Yehova, Mulungu wa Umunthu Wake (w97-CN 10/1 mas. 4-8)
Na. 2: Eksodo 25:17-30
Na. 3: Chifukwa Chake Asamariya Ambiri Akhulupirira (gt-CN mutu 19 ndime 15-21)
Na. 4: Kodi Mwamuna Wokhulupirira Angasunge Bwanji Mtendere m’Banja la Zipembedzo Zosiyana? (fy-CN mas. 132-3 ndime 10-11)
July 5 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 29-32
Na. 1: Musalole Mzimu wa Dzikoli Kukuipitsani (w97-CN 10/1 mas. 25-9)
Na. 2: Eksodo 29:1-14
Na. 3: Kuphunzitsa Ana mwa Malemba m’Banja la Zipembedzo Zosiyana (fy-CN mas. 133-4 ndime 12-15)
Na. 4: Chozizwitsa Chachiŵiri Ali ku Kana (gt-CN mutu 20)
July 12 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 33-36
Na. 1: Khalani Wodalirika ndi Kukhalabe Wokhulupirika (w97-CN 5/1 mas. 4-7)
Na. 2: Eksodo 34:17-28
Na. 3: Kukhalabe Pamtendere ndi Makolo a Chipembedzo China (fy-CN mas. 134-6 ndime 16-19)
Na. 4: Yesu Alalikira m’Tauni ya Kwawo (gt-CN mutu 21)
July 19 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 37-40
Na. 1: sg-CN mas. 13-17 ndime 1-10
Na. 2: Eksodo 40:1-16
Na. 3: Vuto la Kukhala Kholo Lopeza (fy-CN mas. 136-9 ndime 20-5)
Na. 4: Ophunzira Anayi Aitanidwa (gt-CN mutu 22)
July 26 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 1-4
Nyimbo Na. 26 [*Salmo 107-118]
Na. 1: sg-CN mas. 17-19 ndime 11-17
Na. 2: Levitiko 2:1-13
Na. 3: Musalole Kufuna Zinthu Zakuthupi Kugaŵa Banja Lanu (fy-CN mas. 140-1 ndime 26-8)
Na. 4: Zozizwitsa Zowonjezereka m’Kapernao (gt-CN mutu 23)
Aug. 2 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 5-7
Na. 1: Mfungulo ya Chimwemwe Chenicheni (w97-CN 10/15 mas. 5-7)
Na. 2: Levitiko 6:1-13
Na. 3: Kuwononga kwa Uchidakwa (fy-CN mas. 142-3 ndime 1-4)
Na. 4: Chifukwa Chake Yesu Anadza Kudziko Lapansi (gt-CN mutu 24)
Aug. 9 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 8-10
Nyimbo Na. 210 [*Salmo 126-143]
Na. 1: Kuzindikira Pulinsipulo Kumasonyeza Uchikulire (w97-CN 10/15 mas. 28-30)
Na. 2: Levitiko 10:12-20
Na. 3: Kuthandiza wa m’Banja Yemwe Ali Chidakwa (fy-CN mas. 143-7 ndime 5-13)
Na. 4: Kuchitira Chifundo Wakhate (gt-CN mutu 25)
Aug. 16 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 11-13
Nyimbo Na. 80 [*Salmo 144-Miyambo 5]
Na. 1: Chenjerani ndi “Aepikureya” (w97-CN 11/1 mas. 23-5)
Na. 2: Levitiko 13:1-17
Na. 3: Chiwawa cha m’Banja ndi Njira Zochipeŵera (fy-CN mas. 147-9 ndime 14-22)
Na. 4: Yesu Akhululukira Machimo Nachiritsanso (gt-CN mutu 26)
Aug. 23 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 14-15
Nyimbo Na. 137 [*Miyambo 6-14]
Na. 1: Ano Ndiwodi Masiku Otsiriza (w97-CN 4/1 mas. 4-8)
Na. 2: Levitiko 14:33-47
Na. 3: Mateyu Aitanidwa Ndipo Achita Phwando (gt-CN mutu 27)
No. 4: Kodi Kupatukana Ndilo Yankho Lake? (fy-CN mas. 150-2 ndime 23-6)
Aug. 30 Kubwereramo Kolemba. Malizani Genesis 45-Levitiko 15
Nyimbo Na. 145 [*Miyambo 15-22]
Sept. 6 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 16-18
Nyimbo Na. 222 [*Miyambo 23-31]
Na. 1: Pamene Mavuto Sadzakhalakonso (w97-CN 2/15 mas. 4-7)
Na. 2: Levitiko 16:20-31
Na. 3: Afunsidwa za Kusala Kudya (gt-CN mutu 28)
Na. 4: Njira ya Malemba Yothetsera Mavuto a m’Banja (fy-CN mas. 153-6 ndime 1-9)
Sept. 13 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 19-21
Nyimbo Na. 122 [*Mlaliki 1-12]
Na. 1: Chifukwa Chake Kudzimana Konyanya Sindiko Njira Yopezera Nzeru (g97-CN 10/8 mas. 12-13)
Na. 2: Levitiko 19:16-18, 26-37
Na. 3: Kuchita Ntchito Zabwino pa Sabata (gt-CN mutu 29)
Na. 4: Kupereka Mangaŵa a Muukwati (fy-CN mas. 156-8 ndime 10-13)
Sept. 20 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 22-24
Nyimbo Na. 8 [*Nyimbo ya Solomo 1-Yesaya 5]
Na. 1: Kodi Kudandaula Konse Nkoipa? (w97-CN 12/1 mas. 29-31)
Na. 2: Levitiko 23:15-25
Na. 3: Yesu Ayankha Omuimba Mlandu (gt-CN mutu 30)
Na. 4: Maziko a Baibulo a Chisudzulo (fy-CN mas. 158-9 ndime 14-16)
Sept. 27 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 25-27
Na. 1: sg-CN mas. 19-21 ndime 1-9
Na. 2: Levitiko 25:13-28
Na. 3: Kodi Nkololedwa Kubudula Ngala pa Sabata? (gt-CN mutu 31)
Na. 4: Zimene Malemba Amanena pa Nkhani ya Kupatukana (fy-CN mas. 159-162 ndime 17-22)
Oct. 4 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 1-3
Na. 1: sg-CN mas. 21-3 ndime 10-20)
Na. 2: Numeri 1:44-54
Na. 3: Kukalambirana (fy-CN mas. 163-5 ndime 1-9)
Na. 4: Kodi Chololeka Nchiyani pa Sabata? (gt-CN mutu 32)
Oct. 11 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 4-6
Na. 1: Yehova Amalamulira Mwachifundo (w97-CN 12/15 mas. 28-9)
Na. 2: Numeri 4:17-33
Na. 3: Kulimbitsa Ukwati (fy-CN mas. 166-7 ndime 10-13)
Na. 4: Kukwaniritsa Ulosi wa Yesaya (gt mutu 33)
Oct. 18 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 7-9
Na. 1: Komwe Chimwemwe Chenicheni Chingapezeke (w97-CN 3/15 tsa. 23)
Na. 2: Numeri 9:1-14
Na. 3: Sangalalani ndi Adzukulu Anu Ndipo Sinthani Pamene Mukukalamba (fy-CN mas. 167-69 ndime 14-19)
Na. 4: Kusankha Atumwi Ake (gt-CN mutu 34)
Oct. 25 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 10-12
Nyimbo Na. 125 [*Yesaya 42-49]
Na. 1: Yehova Amasamala Amene Akuzunzika (w97-CN 4/15 mas. 4-7)
Na. 2: Numeri 10:11-13, 29-36
Na. 3: Mmene Mungachitire Pamene Mwataya Mnzanu wa Muukwati (fy-CN mas. 170-2 ndime 20-5)
Na. 4: Ulaliki Wotchuka Woposa Wonse Umene Unaperekedwapo (gt-CN mutu 35 ndime 1-6)
Nov. 1 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 13-15
Na. 1: Chifukwa Chake Zozizwitsa Zokha Sizimabala Chikhulupiriro (w97-CN 3/15 mas. 4-7)
Na. 2: Numeri 14:13-25
Na. 3: Kodi Ndani Amene Alidi Odala? (gt-CN mutu 35 ndime 7-17)
Na. 4: Njira Zachikristu Zolemekezera Makolo Okalamba (fy-CN mas. 173-5 ndime 1-5)
Nov. 8 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 16-19
Na. 1: Chifukwa Chake Kusauka Sikumalungamitsa Kuba (g97-CN 11/8 mas. 20-21)
Na. 2: Numeri 18:1-14
Na. 3: Sonyezani Chikondi ndi Chifundo (fy-CN mas. 175-8 ndime 6-14)
Na. 4: Muyezo Wapamwamba wa Otsatira Ake (gt-CN mutu 35 ndime 18-27)
Nov. 15 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 20-22
Na. 1: Mmene Baibulo Linadzafikira kwa Ife—Mbali Yoyamba (w97-CN 8/15 mas. 8-11)
Na. 2: Numeri 20:14-26
Na. 3: Nthaŵi Zonse Muziyang’ana kwa Yehova Kuti Akupatseni Nyonga (fy-CN mas. 178-82 ndime 12-21)
Na. 4: Pemphero, ndi Chidaliro mwa Mulungu (gt-CN mutu 35 ndime 28-37)
Nov. 22 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 23-26
Nyimbo Na. 59 [*Yeremiya 7-13]
Na. 1: Mmene Baibulo Linadzafikira kwa Ife—Mbali Yachiŵiri (w97-CN 9/15 mas. 25-9)
Na. 2: Numeri 23:1-12
Na. 3: Khalani ndi Kudzipereka Kwaumulungu ndi Kudziletsa (fy-CN mas. 183-4 ndime 1-5)
Na. 4: Njira ya ku Moyo (gt-CN mutu 35 ndime 38-49)
Nov. 29 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 27-30
Nyimbo Na. 180 [*Yeremiya 14-21]
Na. 1: Mmene Baibulo Linadzafikira kwa Ife—Mbali Yachitatu (w97-CN 10/15 mas. 8-12)
Na. 2: Numeri 27:1-11
Na. 3: Lingaliro Loyenera la Umutu (fy-CN mas. 185-6 ndime 6-9)
Na. 4: Chikhulupiriro Chachikulu cha Kazembe wa Nkhondo (gt-CN mutu 36)
Dec. 6 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 31-32
Nyimbo Na. 170 [*Yeremiya 22-28]
Na. 1: Chiyambi cha Krisimasi Yamakono (w97-CN 12/15 mas. 4-7)
Na. 2: Numeri 31:13-24
Na. 3: Ntchito Yaikulu ya Chikondi m’Banja (fy-CN mas. 186-7 ndime 10-12)
Na. 4: Yesu Achotsa Chisoni cha Mkazi Wamasiye (gt-CN mutu 37)
Dec. 13 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 33-36
Nyimbo Na. 51 [*Yeremiya 29-34]
Na. 1: sg-CN mas. 24-6 ndime 1-11
Na. 2: Numeri 36:1-13
Na. 3: Kodi Yohane Anasoŵa Chikhulupiriro? (gt-CN mutu 38)
Na. 4: Kuchita Chifuniro cha Mulungu Monga Banja (fy-CN mas. 188-9 ndime 13-15)
Dec. 20 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 1-3
Nyimbo 159 [*Yeremiya 35-41]
Na. 1: sg-CN mas. 27-8 ndime 12-20
Na. 2: Deuteronomo 2:1-15
Na. 3: Onyada ndi Odzichepetsa (gt-CN mutu 39)
Na. 4: Banja ndi Tsogolo Lanu (fy-CN mutu 190-1 ndime 16-18)
Dec. 27 Kubwereramo Kolemba. Malizani Levitiko 16-Deuteronomo 3
Nyimbo Na. 192 [*Yeremiya 42-48]