Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mungagaŵire masabusikiripishoni kwa amene akuwafuna. Khalani ndi bolosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu ochita chidwi, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba.
◼ Kuyambira mlungu wa March 22, 1999, buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako lidzaphunziridwa pa Phunziro la Buku la Mpingo. Kope lino la Utumiki Wathu wa Ufumu lili ndi ndandanda yonse ya maphunziro a m’bukuli. Mukhoza kuchititsa fotokope ndandandayi ndi kuiika m’buku lanu kuti musamavutike kuona. Malangizo a mmene tingaphunzirire mawu oyamba a bukuli ali mu ndime 5 ya nkhani yakuti “Kuphunzira Buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako” patsamba 1 la Utumiki Wathu Waufumu wa May 1993.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki aone ntchito ya apainiya okhazikika onse. Ngati ena akuvutika kukwanitsa maola ofunikawo, akulu akonze zowapatsa chithandizo. Onaninso makalata a pachaka a Sosaite a S-201 a deti la October 1 kuti mupezemo malingaliro ochitira zimenezi. Onaninso ndime 12-20 za mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa October 1986.
◼ Mabuku Amene Alipo:
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako—Chichewa, Chingelezi