Phunzitsani Ena Kuti Apindule
1 Yehova amafuna kuti anthu onse apindule. (Yes. 48:17) Amadziŵa zimene zimatipatsa chimwemwe chenicheni. Cholinga chake chachikulu ndi chakuti anthu apewe mavuto ndipo asangalale ndi moyo mwa kumvera malamulo ake. Tikupindula kwambiri ife eni pokhala ndi moyo mogwirizana ndi njira ya Mulungu. (Sal. 34:8) Ndi motani mmene tingaphunzitsire ena kuchita zofananazo?
2 Kodi Anthu Akusoŵa Chiyani? Kumene mumakhalako n’chiyani chimadetsa nkhaŵa eninyumba? Kodi si chitetezo cha nyumba zawo, chomwe chingalimbitse mabanja awo, tsogolo la ana awo, ndi nkhani zina zofananazo? Pamene ali ndi mavuto, kodi amafuna kuti thandizo? Angadzidalire, angadalire mapologalamu opereka malangizo a mmene munthu angadzithandizire yekha, kapena chitsogozo cha anthu ena. Akamachita zimenezi, ambiri amadabwa ndi kusinthasintha komanso kusagwira ntchito kwa malingaliro onena za mmene angapindulire. Tiyenera kuwapatsa zifukwa zokhutiritsa zakuti Mawu a Mulungu ali ndi chitsogozo chabwino kwambiri. (Sal. 119:98) Tingachite zimenezi mwa kuwasonyeza mmene angasinthire miyoyo yawo, ngakhale tsopano lino ngati ayesetsa kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito zimene limanena.— 2 Tim. 3:16, 17.
3 Moyo wa Banja Wabwino: Ndi anthu ochepa amene amazindikira mmene uphungu wouziridwa wa pa Aefeso 5:22–6:4 umagwiriradi ntchito pothetsa mavuto a m’banja. Izi zinali choncho ndi anthu ena okwatirana amene anafuna kupatukana atakhala m’banja kwa zaka khumi. Komano, mkazi anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo anaphunzitsidwa malamulo a m’Malemba okhudza moyo wa m’banja. Mosakhalitsa mwamuna anaona kusintha kumene mkazi wake anapanga chifukwa chogwiritsa ntchito malamulo a Baibulo, ndipo nayenso anayamba nawo phunzirolo. Pambuyo pake mwamunayo anati: “Tsopano tapeza maziko a chimwemwe chenicheni m’moyo wa banja.”
4 Cholinga Chenicheni m’Moyo: Pamene wachinyamata wina wokonda mankhwala osokoneza bongo anakafuna thandizo kwa Mboni, anaphunzitsidwa kuti Yehova amasamala za iye. Iye anati: ‘Ndinaphunzira kuti Mlengi ali ndi cholinga ndi anthu ndiponso amapereka moyo wosatha kwa awo amene iye amakonda. Simungadziŵe mmene ndinasangalalira ndi zimenezi. Lerolino ndili ndi thanzi labwino, maganizo anga ali pamtendere, komanso ndili ndi unansi wolimba ndi Mulungu.’
5 Aliyense akhoza kupindula ndi thandizo labwino lopezeka m’Mawu a Mulungu. Mwa kuwagwiritsa ntchito monga chitsogozo chathu, timatsimikiza kuti njira ya Yehova imapambana njira ya dziko. (Sal. 116:12) Ndi mwayi wathu kuti tipereke uthenga umenewu kwa ena, kuwaphunzitsa kuti apindule iwo eni. Tikatero, tidzakhala ndi zotsatirapo zabwino zochuluka.