Mutu 20
Kumaumanga Moyo Wabanja Wacimwemwe
1. Kodi ncifukwa ninji palibe malo abwino koposa Baibulo a kupezako cilangizo cabwino conena za moyo wa banja?
KUONJEZERA pa kumapereka coonadi pa nkhani zonena za ciphunzitso, Baibulo limapereka uphungu womvekera bwino kwambiri ponena za moyo wa banja. Ilo limatisonyeza ife m’mene tingazigonjetsere zothetsa nzeru za tsiku ndi siku za moyo. Palibe malo ena amene tingapezeko uphungu wabwino, cifukwa cakuti Yehova, Muyambitsi wa Baibulo, alinso Amene anauyambitsa ukwati nalinganiza za moyo wa banja.—Genesis 2:18, 22.
2. (a) Kodi ndi motani mmene Yesu Kristu ananenera za umodzi umene unayenera kukhalapo pakati pa mwamuna ndi mkazi wace? (b) Kodi ici cimafunikira kuti iwo akulitse ciani?
2 Pamene Mulungu anagwirizanitsa mwamuna ndi mkazi oyambawo pamodzi monga mwamuna ndi mkazi, iye anaugogomezera umodzi umene unayenera kukhala pakati pao. Yesu Kristu anacinena ici pamene iye anati: “Kodi simunawerenga kuti iye amene adalenga munthu paciyambi, adawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, cifukwa ci ici mwamuna adzasiya atate wace ndi amace, nadzaphatikizana ndi mkazi wace, ndipo wiriwo adzakhala thupi limodzi? Cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi.” (Mateyu 19:4-6) Iwo anayenera kukhala omacitana mpikisano. Ndiponso iwo sanangokhala kokha atsamwali amene anali kukhalira limodzi m’nyumba imodzi. Ai, iwo anayenera kukhala “thupi limodzi.” Cotero, okwatirana anayenera kukhala ndi cikondi cacikuru kaamba ka wina ndi mnzace, ndi kufunafuna kukhalira limodzi mu umodzi.
MALO A MWAMUNA NDI MKAZI
3. (a) Kodi ndi motani mmene Aefeso 5:23 amaulongosolera mkhalidwe wa mwamuna? (b) Kodi cimeneci cimatanthauzanji?
3 Kuti anthu okwatiriana akhaledi acimwemwe, ponse pawiri mwamuna ndi mkazi ayenera kuwazindikira malo ao. Malo amenewa sanangoikidwa ndi miyambo ya pamalopo. Iwo alongosoledwa m’Mau a Mulungu Baibulo, ndipo ali ogwirizana ndi mikhalidwe imene Mulungu aniika mwa mwamuna ndi mkazi pa nthawi ya kulenga. Podziwa za mmene anampangira munthu, ndi cifuno cimene anali naco, Yehova analemba m’Mau ace kuti “mwamuna nidye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia.” (Aefeso 5:23) Ici cimatanthauza kuti mwamuna ayenera kutsogolera panyumba, akumawapanga malinganizidwe a mayendedwe a banjalo ndi kumalisenza thayo la kumazipanga zosankha zotsirizira. Koma ici sicimamuyeneretsa iye kukhala wolamulira waukali ndi wankharwe wa banja lace.—Akolose 3:19.
4. Kodi ndi citsanzo cabwino ca ndani cimene amuna Acikristu anayenera kuciphunzira, limodzi ndi mapindu otani?
4 Ngakhale kuli kwakuti amuna ambiri aucita umutu mu njira yopanda cikondi, amuna Acikristu anayenera kupewa cimeneci. Iwo ayenera kufufuza mosamalitsa za mmene Yesu Kristu waucitira umutu wace pa mpingo Wacikristu, ndipo ayenera kutsanzira citsanzo cace. Pa Aefeso 5:25 amuna akupatsidwa uphungu wakuti: “Kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwace.” Pakutero, sadzakhala akumafunsira zocuruka kwa akazi ao, koma adzakatsogolera kayendedwe ka banja mu njira imene iri yomtonthoza maganizo munthu aliyense amene alimo.—Mateyu 11:28-30.
5. (a) Kodi ndi motani mmene mkazi Wacikristu anayenera kumuonera mwamuna wace? (b) Ngati mkazi ali ndi maganizo akuthwa koposa mwamuna wace, kodi ndi motani mmene angaugwiritsirire nchito mkhalidwe umenewu munjira yopindulitsa? (c) Kodi ndi mathayo otani a akazi okwatiwa amene alongosoledwa pa Tito 2:4, 5?
5 Mkaziyo, ku mbali yace, “aziopa mwamuna wace.” (Aefeso 5:33) Popeza kuti iye ndiye amene walamulidwa ndi Mulungu kuti azitsogolera, mkaziyo angathandizire kwambiri kudzetsa cimwemwe ca banja mwa kumagonjera mofunitsitsa kwa mutu wacewo. (Akolose 3:18) Ngati mkaziyo ali wocenjera kwambiri koposa mwamuna wace, monga momwe zimacitikira nthawi zina, pamenepo angaugwiritsire nchito mkhalidwe uwu kumcirikizira mwamuna wace mu nchito yace monga mutu, koposa kumapikisana naye kapena kumaziluluza zimene mwamunayo amazicita. (Miyambo 12:4) Pali zambiri zakuti mkaziyo azicite m’banja lace. Baibulo moyenerera limawalimbikitsa akazi okwatiwa kuti “akonde amuna ao, akonde ana ao, akhale odziletsa, odekha, ocita m’nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti Mau a Mulungu angacitidwe mwano.” (Tito 2:4-5) Mkazi ndi mai amene amakwaniritsa nchito zimenezi adzakhala ndi cikondi cokhalitsa ndi kulemekezeka m’banja lace.—Miyambo 31:10, 11, 26-28.
6 (a) Kodi nciani cimene amuna ena amalephera kucilingalira ponena za akazi ao, motero kumaputira zothetsa nzeru? (b) Cotero kodi nciani cimene 1 Petro 3:7 amawalangiza amuna kuti azicicita?
6 M’mabanja ambiri zothetsa nzeru zimabuka pamene mwamuna amalephera kuuzindikira mtima wacikazi, ndi mkhalidwe wa maganizo wa mkazi wace. Iye afunikira kuzindikira kuti iye amaziona zinthu mwa njira yina. Malingaliro ace amabvomereza mwanjira yina. Nyonga yace siri yofanana ndi ya mwamunayo. Cifukwa ca cimeneco cilangizo couziridwa ca amuna ndico cakuti: “Khalani nao monga mwa cidziwitso, ndi kucitira mkazi ulemu, monga cotengera cocepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wacisomo ca moyo.” (1 Petro 3:7) Pamene mwamuna acita ici, iye amathandizira kudzetsa mzimu wa kuzindikira ndi cisungiko m’banjamo.
7. (a) Kodi ndi motani mmene kugwiritsira nchito zimene zalembedwa pa Ahebri 13:4 kumathandizira kupereka cisungiko m’banjamo? (b) Kodi Mkristu ayenera kumagonana ndi ndani yekha, ndipo cifukwa ninji?
7 Kuli kofala pakati pa anthu audziko kaamba ka kuponderezedwa kwa cisungiko ca banjalo mwa kumagonana ndi ena osakhala okwatirana nawo. Koma awo amene amakhala mogwirizana ndi Mau a Mulungu amacinjirizidwa pa ululu ndi cisoni zimene zimadzetsedwa ndi khalidwe loterolo. M’mau amene ali osabvuta kuwazindikira Baibulo limacenjeza kuti: “Ukwati ucitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi acigololo adzawaweruza Mulungu.” (Ahebri 13:4) Cisembwere sicikuloledwa. Awo amene afuna kukhala atumiki a Mulungu ayenera kukhala ndi miyoyo yopanda ucisi. (1 Atesalonika 4:3-8) Iwo ayenera kumagonana ndi awo okha amene ali okwatirana nawowo, ndipo ali ololedwa pamaso pa Mulungu kutero. (Miyambo 5:15-21) Ciyenera kukhala cikhumbo ca mtima wonse ca mwamuna ndi mkazi ca kumathandizana kuti apewe ciyeso ca kulakwa. Iwo angacicite ici mwa kumasonyeza kulingalira kopanda dyera kwa wina ndi mnzace.—1 Akorinto 7:3-5.
8. (a) Kuti ukwati ukhale bwino, kodi cinthu cofunika kopambana ndi ciani pa banjapo? (b) Cotero kodi ndi ciani cimene ciyenera kukhala mbali ya njira ya moyo ya banjalo?
8 Komabe, ngati cigwirizano ca banja cingagwire nchito mogwirizana ndi maprinsipulo aumulungu amene tawakambitsiranawo, payeneranso kukhala cigogomezero ca nthawi yonse pa zinthu zauzimu. Kulambira Yehova Mulungu kuyenera kukhala cinthu coyamba m’banjamo. Sikuyenera kukankhiridwa pambali moziyanja zoyesayesa za kupeza Cuma cakuthupi cocuruka kapena kuti pakhale nthawi yocuruka ya kufunafuna zosangalatsa thupi. (Luka 8:11, 14, 15) Pemphero la banja limodzi ndi kusonkhana kwa kawirikawiri kwa banjalo kaamba ka phunziro la Baibulo ziyenera kukhala mbali ya moyo wa banja lirilonse. Kodi mumalinganiza kaamba ka ici m’banja mwanu?
KUMAWALERA ANA MU NJIRA YAUMULUNGU
9. Kodi ndi motani mmene zothetsa nzeru za kulera ana mwacipambano zingathetsedwere?
9 Pamene ana amabadwa, ciri cikhumbo ca makolo acikondi cakuona kuti miyoyo ya ana amenewo ikhale yabwino. Koma nchitoyo simakhala yofewa. Pamakhala zothetsa nzeru zambiri zimene zimabuka m’kupita kwa nthawi. Izi zingathetsedwe mwacipambano kokha mwa kugwiritsira nchito uphungu wa m’Mau a Mulungu.—Miyambo 22:6; Deuteronomo 11:18-21.
10. (a) Kuonjezera pa cakudya, zobvala ndi malo ogona kodi ndi cianinso cimene ana amacifunikira kwambirimbiri? (b) Kodi ndi liti pamene zimenezi ziyenera kuperekedwa?
10 Nthawi yocuruka limodzi ndi yosesayesa kawirikawiri zimakhala zofunika kuona kuti pali cakudya coyenera, zobvala zabwino ndi nyumba yosangalatsa ya kukhalamo. Koma Baibulo mobwerezabwereza limasonyeza kuti thayo la makolo mwa njira iriyonse silimathera pamenepo. Kulinso kofunika kuwaphatikizamo ana mokhazikika mu programu ya banjalo ya cilangizo m’Mau a Mulungu. (Salmo 78:5-7 [77:5-7Dy]) Osangoti kokha pa nthawi ya kuphunzira, komanso pa nthawi zina makolo ayenera kumalankhula ndi ana ao ponena za Yehova ndi njira zace. (Deuteronomo 6:6, 7) Pamene ici cacitidwa, ana amaphunzira kuganiza za Mulungu mogwirizana ndi macitacita onse a moyo.
11. Kodi ndani amene ali ndi thayo lalikuru la kuona kuti ana akupatsidwa cilangizo m’Mau a Mulungu, ndipo kodi ndi motani mmene Baibulo limasonyezera ici?
11 Kuli kwamaziko kwa bamboyo, monga mutu wa banjalo, kuti Malemba amaliika thayo pa iyeyo la kuona kuti cilangizo ici cikuperekedwa. Pamene iye awapanga makonzedwe a izi ndipo iye mwiniyo atsogolera m’kucipereka ici, banja lonselo limagwirizanitsidwa pamodzi. Pa nthawi imodzimodziyo, anawo amapatsidwa mtundu wa kaphunzitsidwe kamene amakayenerera kwambiri. Cotero kuli kofunika kumakumbukira zimene zalembedwa pa Aefeso 6:4: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi cilangizo ca Ambuye.”—Onaninso Miyambo 4:1.
12. Kodi ncifukwa ninji kumvera makolo sikuyenera kululuzidwa?
12 Mbali yina ya “cilangizo ca Ambuye” cimene ciyenera kuphunzitsidwaco cimaphatikizapo thayo la mwanayo la kukhala womvera kwa makolo ace. Ici siciri cinthu cimene ciyenera kuonedwa mopepuka, popeza kuti ziyembekezo za mwanayo kaamba ka moyo wamuyaya zikulowetsedwamo. (Aefeso 6:1-3) Mulungu ndiye amene amafuna kuti ana aziwamvera makolo ao. Kumasonyeza nzeru ku mbali ya makolo ngati iwo modekha ndi mosalekeza aligogomezera phunziro ili m’maganizo ndi mumtima mwa ana ao.—Akolose 3:20, 23.
13. Kodi ndi motani mmene bukhu la Baibulo la Miyambo limakugogomezerera kufunika kwace kwa kuwaongolera ana pamene iwo alakwa kanthu mwadala?
13 Padzakhala nthawi pamene icico cimafunikira zambiri koposa ndi kumangomuuza mwanayo za cimene ciri coyenera. Pamene iye acicita mwadala cimene akudziwa kuti ciri colakwa, kacitidwe kamphamvu kamafunika kuti mwanayo akuone kuopsa kwace kwa nkhaniyo pa iye. Mwanzeru Baibulo limanena kuti: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.” (Miyambo 22:15) Cifukwa ca kupanda ungwiro kwa colowa ana amabadwa ndi mkhalidwe wa kufuna kucita coipa, cotero iwo amafunikira ciongolero. Kholo lacikondi silidzanyalanyaza kucita ici. Monga momwe Miyambo 13:24 imanenera: “Wolekerera mwana wace wosammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.”
14. Kodi ndi motani mmene ciongolero cingaperekedwere pa banja Lacikristu, limodzi ndi zoturukapo zabwino zotani?
14 Cilangizo cimene cikuperekedwa m’cikondi ciri ndi ubwino wosatha wa mwanayo. Ico sicimacitikira m’kukalipa kwaciwawa cifukwa ca mkwiyo kapena mwa kukuwa kwakukuru koopseza. Imeneyo sindiyo njira Yacikristu. (Aefeso 4:31, 32) Payenera kukhalapo kutsimikizira, komanso kulingalira bwino kwa maganizo kuyenera kukhalapo. Makolo eniwo ayenera kumasonyeza citsanzo cabwino, osangoti kokha kumabvala cisonyezero wamba ca cilungamo—ana amaziona mwamsanga zimenezo—koma payenera kukhalapo kuona mtima, kunena zoona. Ndipo ngati atero anawo adzathandizidwa kuzindikira kuti maprinsipulo olungama a Mulungu akulamulira panyumbapo, osati zamasewera kapena zacibwana. Anawo sadzakhala akumaopa kuti iwo adzalangidwa mosalungama. Koma m’malo mwace iwo adzacigwirizanitsa cilango ndi kuswa kwa malamulo oyenera a khalidwe labwino.
15. (a) Kodi ndi ciani cimene ana ayenera kuphunzitsidwa ponena za: Kunama? (b) Kodi ndi motani mmene makolo angawaphunzitsire ana ao kotero kuti angacite cimene ciri coyenera ngakhale kukhale kwakuti makolo ao palibe?
15 Pakati pa maprinsipulo olungama ocokera m’Baibulo amene afunikira kuwakambitsirana mosamalitsa m’banja ndiwo aja onena za malamulo aumulungu a cikhalidwe ca mtima. Ana afunikira kuphunzitsidwa, mwacitsanzo, kuti “yense wakukonda bodza ndi kulicita” ali wonyansa kwa Yehova. (Cibvumbulutso 22:15; Miyambo 6:16-19) Kubanso, m’mipangidwe yace yonse yosiyanasiyana kuyenera kuonedwa monga kuuswa mkhalidwe wa cikhalidwe cabwino ca Mulungu. (Aefeso 4:28; Aroma 13:9, 10) Anyamata amenewa afunikira kucenjezedwa, mu njira imene iwo angazindikire, kuti asamacita cisembwere ca kugonana kapena ciriconse cimene cingatsogolere ku ico. (Aefeso 5:5; Miyambo 5:3-14) Kambitsiranani limodzi monga banja zothetsa nzeru zosiyanasiyana zimene zimabuka panyumba, pa sukulu ndiponso posewera. Akambitsiraneni limodzi malemba amene amasonyeza mtundu wa khalidwe limene liri lokondweretsa Mulungu. Mu njira iyi ana adzaphunzira kuligwiritsira nchito Baibulo m’miyoyo yao. Ilo lidzakhala cinjirizo, kotero kuti ngakhale pamene anawo ali kwina kumene kulibe makolo ao cilangizo cimene acilandiraco cidzapitirizabe kuwatsogolera iwo.—Miyambo 6:20-23.
16. (a) Kodi nciani cimene Baibulo limanena ponena za ciyambukiro ca atsamwali oipa? (b) Cotero kodi ndi motani mmene makolo angasonyezere nzeru ponena za kasankhidwe ka atsamwali a ana ao?
16 Kusamala kuyeneranso kuperekedwa pa kusankha mabwenzi. Mabwenzi a munthu amauyambukira kwa kukurukuru moyo wa munthuyo. Atsamwali abwino ali ndi ciyambukiro cabwino, koma “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Kawirikawiri Baibulo limacisonyeza ceniceni ici. (Genesis 34:1, 2; Numeri 25:1, 2) Ana sangakuzindikire kuopsa kwace kwa ici, koma makolo anayenera kudziwa. Cotero ciri cisonyezero ca nzeru ku mbali yao kumapenyetsetsa mwacikondi za amene ali atsamwali a ana ao. Atsamwali amenewa amaphatikizapo, osangoti kokha awo amene anawo amasewera nawo, komanso aja amene iwo amawerenga za iwo ndi aja amene amawaona pa akanema ndi pa wailesi ya kanema.—Afilipi 4:8.
17. Kodi ndi cina cianinso cimene cidzathandizira kuupangitsa moyo wa banja kukhaladi wokhutiritsa?
17 Komabe, kuti moyo wa banja ukhale wokhutiritsadi, zambiri zikufunika koposa kungopewa zinthu zobvulaza zokha. Payeneranso kukhalapo kusangalala ndi kumacita zinthu zoyenera limodzi monga banja. Cisangalalo ceniceni ca moyo wa banja cimatayika pamene aliyense wa m’banjamo angocita zace zimene afuna osawalabadira enawo. Koma pamene kukhalapo kusangalala ndi kumacita zinthu zoyenera limodzi monga banja. Cisangalalo ceniceni ca moyo wa banja cimatayika pamene aliyense wa m’banjamo angocita zace zimene afuna osawalabadira enawo. Koma pamene kukhalako kukambitsirana kolimbikitsa kwa banja lonse, pamene malinganidzidwe apangidwira limodzi ndipo onse agwirira nchito limodzi kuwakwaniritsa iwo, banjalo limagwirizanitsidwa pamodzi mu umodzi. (Miyambo 15:22) Ici sicimakhala cobvuta pamene m’banjamo muli cikondi. Ndipo cikondi siciri cinthu cosoweka pakati pa anthu amene amamdziwa Mulungu nakhala ndi mzimu wace.—1 Yohane 4:7, 8; Agalatiya 5:22, 23.
KUZITHETSA ZOBVUTA ZA BANJA
18. Kodi ndi motani mmene uphungu wa pa Akolose 3:12-14 umatithandizira ife kuzithetsa zobvuta zirizonse za banja zimene zingabuke?
18 Ngakhale m’mabanja amene amakhala acimwemwe kwa nthawi yambiri, zobvuta zingabuke pa nthawi zina. Izi kawirikawiri ziri cifukwa ca kupanda ungwiro kwaumunthu, kapena zitsenderezo za dziko mu limene tikukhalamo. Kodi nciani cimene cingacitidwe pamene kuombana kukhalapo pakati pa mamemba a banja? Mathetsedwe ace sali obvuta kuwapeza ngati tingakumbukire kuti tonsefe ndife opanda ungwiro. Sikunangokhala kokha kunja kwa pabanjapo komanso m’kati mwa banjalo mmene tifunika kuugwiritsiramo nchito uphungu wouziridwa wakuti: “Bvalani . . . mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.”—Akolose 3:12-14; onaninso Miyambo 10:12; 19:11.
19. Pamene mkangano ubuka pakati pa ana, kodi ciani cimene mmodzi wa makolowo angacicite cimene cidzakhaladi copindulitsa kwambiri?
19 Pamene cothetsa nzeruco cionekera kukhala cobvuta kwambiri, pali mastepe amene angatsatiridwe kaamba ka kuilinganiza njira kaamba ka cikhululukiro cacikondi. Mwacitsanzo, pamene mkangano ubuka pakati pa ana, mmodzi wa makolowo angakhale pansi limodzi ndi anawo, aimve cobvutaco, ndipo pamenepo kupereka cisonkhezero cakuti pakhale kupepesana koyenererako ndiponso cikhululukiro cofunikaco. Pa nthawi zoterozo malemba onga ngati aja amene tangowawerenga kumene aja angakambitsiridwe mopindulitsa.
20. Pamene bvuto lina libuka pakati pa mwamuna ndi mkazi wace, kodi ndi ciani cimene sicidzathandizira kuithetsera nkhaniyo, koma nciani cimene cidzathandizira?
20 Ngati bvutolo liri pakati pa mwamunayo ndi mkazi wace, ndithudi kuli bwino kusayamba kumanena za ilo pamaso pa ana. Ndiponso mkhalidwewo sudzaongokera pakumawawanditsa madandaulo kwa mabwenzi anu ndi anthu okhala pafupi nanu. Ngakhale kukhale kwakuti munthu wakhumudwa kwambiri, kulalata mokuwa sikudzaongolera zinthu. (Miyambo 29:22) Ndipo m’ng’aluwo udzaonjezeka kukula ngati awiriwo atha masiku ambiri osalankhulana. Cinthu Cacikristu ca kuicita ndico ca kucikambitsiranana cothetsa nzeruco limodzi, mwa citsimikiziro cakuti mubwezeretse mtendere. Ngakhale ngati winayo ndiye amene ali wolakwa, kupangitseni kugwirizananso kukhala kosabvuta mwa kukoma mtima kwanu. Ngati mwalakwa muli inuyo, pemphani cikhululukiro modzicepetsa. Musacikankhire ico patsogolo; cithetseni cothetsa nzeruco pasanapite nthawi yaitali. “Dzuwa lisalowe muli cikwiyire.”—Aefeso 4:26; onaninso Mateyu 18:21-35.
21. (a) Kodi cisudzulo ciri njira ya kuthetsera mabvuto a banja? (b) Kodi Baibulo limanena kuti maziko okha a cisudzulo cimene cimammasula munthu kukwatiranso ndi ciani?
21 Ngakhale kuli kwakuti cisudzulo ciri cofala kwambiri m’dziko, Baibulo silimaciyamikira ico kukhala njira ya kuthetsera zothetsa nzeru. Ukwati uli cinthu ca moyo wonse, ndipo suyenera kuonedwa mopepuka. (Aroma 7:2) Mau a Mulungu amawalola maziko amodzi okha pa amene Mkristu angacipezere cisudzulo cimene cingammasule iye kukwatiranso. Kodi cimeneco ndi ciani? Ico ciri cigololo. Mu cocitika ici, kuli kwa wosacimwayo kuti asankhe ngati angafunefune cisudzulo kapena ai. (Mateyu 5:32) Komabe, kacitidwe ka kufunafuna cisudzulo sikanayenera kutsatiridwa kokha cifukwa ca cikaikiro; payenera kukhalapo umboni woonekera bwino.
22. Ngati munthu anacicita cisudzulo mwansontho asanawaphunzire malamulo a Mulungu ndipo wayamba kumakhalira limodzi ndi winanso, kodi nciani cimene angacicite ngati afuna kumatumikira Yehova?
22 Kale, asanaphunzire zofunika zolungama za Mulungu, anthu ena angakhale ansontho kufuna kupeza cisudzulo, ndipo tsopano ayambanso kumakhala limodzi ndi wina. Kodi angatani? Iwo sangathe kubwereranso m’mbuyo ndi kukayambiranso. Koma, ngati iwo afuna kukhala ndi phande mu utumiki wa Yehova Mulungu, ndipo akukhala ndi wina, iwo ayenera kutsimikizira kuti ukwati wao watsopano linowo walembetsedwa mwa lamulo la boma. Iwo afunikira kupita kwa Mulungu m’pemphero ndikufunafuna cikhululukiro cace kaamba ka kacitidwe kao kakale. Pamenpo iwo ayenera kugwira nchito molimbika pa kumakhala mogwirizana ndi zofuna za Mulungu ponena za ukwati kuyambira pa nthawi yino kunkabe mtsogolo.
23. (a) Kodi Baibulo limsonkhezera kusiyana ndi wokwatirana naye wosakhulupirira pamene zobvuta zibuka? (b) Kodi ndi motani mmene wokhulupirirayo angauongolerere mkhalidwe wa pa banjapo, limodzi ndi coturukapo cotani?
23 Bwanji ngati wokwatirana naye wanuyo wakana kuphunzira Mau a Mulungu limodzi nanu? Ndipo bwanji ngati simuli okhoza kukambitsirana zothetsa nzeru limodzi pa maziko a maprinsipulo a Baibulo? Baibulo limakulimbikitsanibe inu kukhalira limodzi ndi kusakuona kulekana kukhala njira yosabvuta ya kuzithetsera zothetsa nzeruzo. Citani zimene inuyo mungathe kuzicita kuti muuongolere mkhalidwewo panyumba panu mwa kumagwiritsira nchito zimene Baibulo limanena ponena za kakhalidwe kanu. Mu nthawi yace, cifukwa ca khalidwe lanu Lacikristu, inu mungampindule wokwatirana nanuyo. (1 Akorinto 7:10-16; 1 Petro 3:1, 2) Ndipo ndi dalitso lotani nanga limene mudzakhala nalo ngati kudekha kwanu kwacikondiko kwapatsidwa mfupo mwa njira iyi!
24. Potsirizira pace, kodi ndi motani mmene mungalimangire banja lacimwemwe?
24 Pali zambiri zimene zingacitidwe m’banja lirilonse pa kumaumanga moyo wabanja wacimwemwe. Ugwiritsireni nchito uphungu wa Baibulo, ndipo padzakhala zoturukapo zabwino! Aliyense m’banjamo mwacikondi afunefune zabwino za ena, motero kumazilimbikitsa zomangira za banja. (Akolose 3:14) Koposa zonse, khalani ndi phande mogwirizana mu kulambira koona, kotero kuti nonsenu limodzi mudzasangalala ndi dalitso lalikuru la Yehova Mulungu, Uyo amene angacionjezere cimwemwe canu mwa kukupatsani moyo wosatha.—Miyambo 3:11-18.
[Chithunzi patsamba 176]
Kusonkhana kawirikawiri kaamba ka kuphunzira Baibulo kuyenera kukhala mbali ya moyo wa banja lirilonse