Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Khalani ndi bulosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu okondwerera, komanso yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Tili okondwa kwambiri kuona kuti mipingo yambiri yayamba kuchita zotheka kuti ipeze malo omangapo Nyumba yawo ya Ufumu. Choncho, Makomiti athu anayi Omanga Achigawo m’dziko muno akhala otanganidwa kugwira ntchito, kulemba zinthu zofunika za mipingo yambiri ntchito yomanga isanayambe. Pamene Nyumba za Ufumu zimenezi zatha kumangidwa, zidzadzetsa chitamando chachikulu kwa Yehova, Mulungu wathu wamoyo, ndipo timasangalala ndi zimenezi. Pakalipano akulu ambiri amabwera ku Beteli, kudzafunsa malangizo ndi chithandizo china chonena za mmene angapezere malo, zikalata zake, ndi nkhani zina. Timasangalala kukuthandizani, ngati tingathe kutero. Koma kaamba ka ubwino wawo, tikupempha kuti obwera kudzafunsa thandizo lina lililonse lokhudza Nyumba ya Ufumu ayenera kubwera Lachiŵiri kapena Lachinayi. Masiku ameneŵa ndi amene aikidwa kuti aziyankha mafunso okhudza Nyumba ya Ufumu. Tidzayamikira kwambiri kusamalira kwanu nkhaniyi.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki apende ntchito ya apainiya okhazikika onse. Ngati pali wina yemwe zikum’vuta kukwanitsa maola ofunikawo, akulu apange makonzedwe omuthandiza. Onaninso malingaliro ena m’makalata a Sosaite apachaka a S-201 a October 1. Ndiponso onani ndime 12-20 m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1986.
◼ Kuyambira mlungu wa April 17, 2000, tidzayamba kuphunzira buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja pa Phunziro la Buku la Mpingo.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Buku lalikulu la Imbirani Yehova Zitamando—Chicheŵa
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase—Chicheŵa