Bokosi la Mafunso
◼ Kodi n’koyenera kuwombera m’manja chilengezo cha kubwezeretsedwa?
Chifukwa cha kukoma mtima kwake kwachikondi, Yehova Mulungu wapereka njira ya Malemba yakuti ochita zoipa olapa apezenso chiyanjo chake ndi kubwezeretsedwa mu mpingo wachikristu. (Sal. 51:12, 17) Zimenezi zikachitika, timalimbikitsidwa kuwatsimikizira chikondi chathu anthu olapa moona mtima ameneŵa.—2 Akor. 2:6-8.
Ngakhale kuti timasangalala kwambiri pamene wachibale wathu kapena mnzathu wabwezeretsedwa, tiyenera kukhala chete pamene akulengeza mu mpingo za kubwezeretsedwa kwake. Nsanja ya Olonda ya October 1, 1998 patsamba 17 inanena nkhaniyi motere: “Komabe, tikumbukire kuti ambiri mumpingo sakudziŵa zimene zinachotsetsa munthuyo kapena zimene zachititsa kuti abwezeretsedwe. Ndiponso, pangakhale ena amene anakhudzidwa mtima kwambiri kapena kukhumudwa mwina kwanthaŵi yaitali chifukwa cha tchimo la munthu wolapayo. Chifukwa chozindikira zinthu ngati zimenezo, tidzapeŵa mawu akuti tam’landira polengeza kubwezeretsedwa kwake. Tidzasiyira nkhani imeneyo kwa munthu aliyense payekha kuti adzilankhulire yekha pokambirana naye wobwezeretsedwayo.”
Ngakhale timakondwa kwambiri kuona kuti wina wabwerera m’choonadi, kuwombera m’manja panthaŵi imene iye akubwezeretsedwa n’kosayenera.