Kupeza Chimwemwe mu Utumiki Wanu Wopatulika
1 Anabwerera “mokondwera.” Nkhani ya Baibulo imafotokoza mmene ophunzira 70 anamvera atabwerera kwa Yesu, atatha kulalikira kwanthaŵi yaitali. Anapeza chimwemwe cha mumtima m’kuchita chifuniro cha Mulungu. (Luka 10:17) N’chiyani chimene chingakuthandizeni kupeza chimwemwe chofananacho mu utumiki wopatulika?
2 Malingaliro Oyenera: Muli ndi mwayi umene Mulungu wakupatsani wodziŵitsa anthu cholinga chachikulu cha Yehova. Mwa kulalika kwanu, mungathandize kumasula munthu ku mikhalidwe yoipa ya dzikoli ndiponso ku nsinga zachipembedzo chonyenga. Mungapatse anthu chiyembekezo cha moyo m’dziko lopanda udani umene ulipo masiku ano. Talingalirani mmene Yehova amasangalalira mukabzala bwino mbewu za choonadi mu mtima wabwino. Khalani ndi malingaliro abwino popempherera mzimu wa Mulungu kubala chipatso cha chimwemwe mwa inu pamene mukuchita utumiki ndi mtima wanu wonse.
3 Maphunziro Oyenerera: Nthaŵi yamalangizo imene Yesu anakhala ndi ophunzira ake 70 ndi yofanana ndi Msonkhano wa Utumiki wamasiku ano. Anawaphunzitsa kuti akachite utumiki wawo mogwira mtima. (Luka 10:1-16) Lerolino Msonkhano wa Utumiki umakuphunzitsani njira zimene mungafikire anthu, mmene mungayambire kukambirana, mmene mungayambire ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Mwa kudzipereka ndi kuwongolera maluso anu akulalikira, mudzaona kuti kudzikayikira konse kapena kudziona kuti ndinu osayenera kudzatha ndipo kudzabisika ndi chidaliro ndiponso chimwemwe.
4 Yang’anani M’tsogolo: Yesu anapeza chimwemwe mu utumiki wake wopatulika ngakhale kuti anapirira mavuto. Chifukwa chiyani? Chifukwa maso ake onse anali pa madalitso ndi maudindo amene anali patsogolo pake. (Aheb. 12:2) Mungachite chimodzimodzi mwa kuika maganizo anu ndi mtima wanu pa dzina la Yehova ndi pa madalitso a m’dziko latsopano la Mulungu. Izi zidzawonjezera chimwemwe ndi tanthauzo mu utumiki wanu.
5 Kuchita utumiki wopatulika kwa Yehova ndi mwayi waukulu kwabasi umene mungakhale nawo lerolino. Chotero, munene kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda.”—Sal. 40:8.