Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa May 1 kufikira August 21, 2000. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Yankho la Gideoni pa mawu onyoza a amuna a Efraimu linasonyeza kuleza mtima ndi kudzichepetsa kwake ndipo chotero anathetsa kunyoza kwawo kosayenererako ndi kusungitsa mtendere. (Ower. 8:1-3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu]
2. Kunena zoona Manowa ndi mkazi wake anaona woyankhulira waumwini wokhala ndi thupi la munthu wa Mulungu osati Yehova weniweniyo ngakhale kuti iye ananena kuti “taona Mulungu.” (Ower. 13:22) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 5/15 tsa. 23 ndime 4.]
3. Ulosi wa wobwebweta wamizimu wa ku Endori sunakwaniritsidwe m’pang’ono pomwe. (1 Sam. 28:19) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w79 2/15 tsa. 6.]
4. Nkhani ya Davide ndi Bateseba iyenera kusonyeza makolo kuti khalidwe lawo lingakhudze ana awo kwambiri. (2 Sam. 12:13, 14) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86 3/15 tsa. 31.]
5. Oweruza 21:25 amanena za nthaŵi pamene Yehova anasiya mtundu wa Israyeli opanda chitsogozo chilichonse. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 6/15 tsa. 22 ndime 16.]
6. Zifaniziro za akerubi pa likasa la chipangano zinaimira kukhalapo kwa Yehova monga Mfumu, amene ankanenedwa kuti ‘amakhala pakati pa akerubi.’ (1 Sam. 4:4) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w80 11/1 tsa. 29 ndime 2.]
7. Pamene asilikali a Sauli anadya magazi panthaŵi imene anali pa vuto lalikulu kwambiri ndipo sanalangidwe, zinasonyeza kuti nthaŵi zina pangakhale zifukwa zomveka bwino zomwe munthu angaswere malamulo a Mulungu kwakanthaŵi chabe n’cholinga chopulumutsa moyo wake. (1 Sam. 14:24-35) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 4/15 tsa. 31 ndime 7-9.]
8. Ngakhale kuti ena amagwirizanitsa liwu lakuti “kukopa” ndi kusonkhezera ndiponso machenjera, m’lingaliro labwino liwu limeneli lingagwiritsidwe ntchito kupereka lingaliro la kukhutiritsa maganizo ndi kusintha malingaliro a munthu mwa kukambirana naye mogwira mtima ndi momveka bwino. (2 Tim. 3:14, 15) [w98-CN 5/15 tsa. 21 ndime 4]
9. “Phukusi la amoyo” limasonyeza makonzedwe a Mulungu otetezera ndi opulumutsira, amene akanapindulitsa Davide ngati akanapeŵa milandu yakupha pamaso pa Mulungu. (1 Sam. 25:29) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 6/15 tsa. 14 ndime 3.]
10. Pangano la Ufumu wa Davide, lofotokozedwa pa 2 Samueli 7:16, linachepetsa mzera wa Mbewu kukafika kwa Mesiya ndipo linali chitsimikiziro chakuti wina wa m’banja la Davide akadza kudzalamulira “ku nthaŵi zonse.” [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 2/1 tsa. 14 ndime 21—tsa. 15 ndime 22.]
Yankhani mafunso otsatiraŵa:
11. Kodi Salmo 34:18 amatipatsa chitsimikizo chotani? [w98-CN 4/1 tsa. 31 ndime 2]
12. Kodi pamene Yosefe anatchulidwanso kuti Barnaba, zinasonyeza chiyani? (Mac. 4:36) [w98-CN 4/15 tsa. 20 ndime 3, mawu a m’munsi]
13. Kodi n’chifukwa chiyani nkhani ya m’Baibulo imati Eli anapitirizabe kuchitira ulemu ana ake aamuna koposa Yehova? (1 Sam. 2:12, 22-24, 29) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 9/15 tsa. 13 ndime 14.]
14. Kodi mutu wa nkhani ungasankhidwe motani? [sg-CN tsa. 44 ndime 2]
15. Malinga ndi 1 Samueli 1:1-7 kodi ndi chitsanzo chabwino kwambiri chiti chimene chinasonyezedwa ndi banja la Samueli? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 3/1 tsa. 16 ndime 12.]
16. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘chuma n’chachinyengo’? (Mat. 13:22) [w98-CN 5/15 tsa. 5 ndime 1]
17. Kodi Yonatani wachikulireyo anasonyeza motani kuti akuzindikira wodzozedwa wa Yehova, Davide, ndipo kodi zimachitira chithunzi chiyani lerolino? (1 Sam. 18:1, 3, 4) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 1/1 mas. 24, 26 ndime 4, 13.]
18. Ngakhale kuti anali “wangwiro ndi woongoka,” kodi buku la Yobu limasonyeza motani kuti zimenezi sizitanthauza kuti Yobu anali wosachimwa? (Yobu 1:8) [w98-CN 5/1 tsa. 31 ndime 1]
19. Kodi mawu akuti “yesetsani” amatanthauzanji? (Luka 13:24) [w98-CN 6/15 tsa. 31 ndime 1, 4]
20. Pamene tikugwira ntchito ndi anthu ena, kodi ndi phunziro labwino lotani limene tiyenera kulikumbukira, lolembedwa pa 2 Sam. 12:26-28? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 12/1 tsa. 19 ndime 19.]
Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Pamene mukukonzekera nkhani, muyenera kusiya mfundo zimene sizikuthandizira kwenikweni ․․․․․․․ wa nkhani yanu. [sg-CN tsa. 41 ndime 10]
22. Mwa kuchita ntchito yabwino ya kukonzekera gawo lililonse mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase, timadzilola ․․․․․․․ ndi pulogalamu imeneyi ya maphunziro yomwe Yehova watipatsa. [sg-CN tsa. 43 ndime 18]
23. Dzina la Mulungu, lakuti Yehova, limatanthauza kuti ․․․․․․․ ndipo limasonyeza kuti Yehova angakwaniritse ntchito iliyonse imene ikufunika kuti akwaniritse ․․․․․․․ zake. [w98-CN 5/1 tsa. 5 ndime 3]
24. Pangano lofotokozedwa pa 2 Samueli 7:12, 13 ndi ․․․․․․․ . [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 2/1 tsa. 14.]
25. Fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo limasonyeza kuti munthu wolungamadi ndiye amene samangomvera kokha ․․․․․․․ a Mulungu koma amatsanziranso ․․․․․․․ yake. (Luka 10:29-37) [w98-CN 7/1 tsa. 31 ndime 2]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Munthu amene analemekeza banja lake kwambiri kuposa Mulungu anali (Manowa; Eli; Sauli). (1 Sam. 2:29, 30) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 12/15 tsa. 16 ndime 8.]
27. Nthaŵi ya ulamuliro wa oweruza mu Israyeli inatha pamene (Samueli; Davide; Sauli) anadzozedwa kukhala mfumu ndipo mwamsanga pambuyo pake anagonjetsa ( Aamoni; Amoabu; Afilisti) mothandizidwa ndi Yehova. (1 Sam. 11:6, 11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 12/15 tsa. 9 ndime 2–tsa. 10 ndime 1.]
28. Anali (mtumwi Paulo; atate wake; amayi ndi agogo ake akazi) amene anatsogolera m’kuphunzitsa Timoteo “malembo opatulika” kufikira pakumuona akukhala mmishonale ndi woyang’anira wabwino kwambiri. (2 Tim. 3:14, 15; Afil. 2:19-22) [w98-CN 5/15 tsa. 8 ndime 3–tsa. 9 ndime 5]
29. Pamene tili m’mavuto, Yehova amatiyembekezera kugwiritsa ntchito (nzeru yathu ya kulingalira; mphamvu zathu zakuthupi; chuma chakudziko) ndipo osati kungom’dikirira kuti atikonzere zinthu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onaninso w87-CN 4/15 tsa. 19.]
30. Lamulo la Mulungu pa (kulimbana ndi adani; magazi; kunama) silinganyalanyazidwe panthaŵi yangozi. (1 Sam. 14:31-34) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onaninso w86 9/1 tsa. 25.]
Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Ower. 11:30, 31; 1 Sam. 15:22; 30:24, 25; 2 Maf. 6:15-17; Yak. 5:11
31. Yehova amatitsimikizira kuti adzagwiritsa ntchito magulu ake ankhondo a kumwamba kutchinjiriza anthu ake malinga ndi chifuniro chake. [w98-CN 4/15 tsa. 29 ndime 5]
32. Akulu a mu mpingo ali ndi udindo womamatira ku mapangano awo ngakhale kuti nthaŵi zina mapanganowo angakhale opweteka maganizo ndiponso ovuta kuwakwaniritsa. [w99-CN 9/15 tsa. 10 ndime 3-4]
33. Kukhalabe wokhulupirika panthaŵi ya mayesero kumadzetsa mphoto yaikulu kwambiri yochokera kwa Yehova Mulungu. [w98-CN 5/1 tsa. 31 ndime 4]
34. Chikondi chenicheni pa Mulungu chimafuna kumvera malangizo a Mulungu ndipo osati kum’phera nsembe kokha. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 6/15 tsa. 5 ndime 1.]
35. Yehova amayamikira kwambiri anthu amene amatumikira m’maudindo ochirikiza gulu lake lerolino. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86 9/1 tsa. 28 ndime 4.]