Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/00 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 8/00 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu August: Lililonse la mabulosha a masamba 32 amene ali m’mumsiŵa angagwiritsidwe ntchito: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, What Happens to Us When We Die? ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndi Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? angagaŵiridwe poyenera kutero. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi pa ulendo wobwereza, mutha kugaŵira masabusikiripishoni. Kuyambira kumapeto kwa mwezi umenewu, tidzagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36, wa mutu wakuti “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?” November: Tidzapitiriza kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Mipingo imene idzamalize kugaŵira eninyumba onse Uthenga wa Ufumu Na. 36 m’gawo lawo ingagaŵire bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detilo. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukapereka lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kufunsira Makalendala a Mboni za Yehova a 2001 pofunsira mabuku a September. Makalendala adzapezeka m’Chicheŵa, m’Chingelezi ndi m’Chitumbuka.

◼ Mafomu okwanira odzagwiritsidwa ntchito m’chaka cha utumiki cha 2001 atumizidwa ku mpingo uliwonse. Chonde gwiritsani ntchito mafomuŵa moyenera. Ayenera kugwiritsidwa ntchito pachifukwa chimene anapangidwira basi.

◼ Kuŵerengera mabuku amene ali m’sitoko kochita pachaka kuyenera kuchitika pa August 31, 2000 kapena pafupi ndi detilo. Kuŵerengera kumeneku n’kofanana ndi kuŵerengera mabuku kumene woimira za mabuku amachita mwezi uliwonse, ndipo ziŵerengero zonse ziyenera kulembedwa pafomu Yoŵerengera Mabuku (S-18). Chiŵerengero chonse cha magazini amene alipo chingapezeke kwa mtumiki wa magazini mu mpingo uliwonse wa m’gulu la mabuku. Mpingo woimira za mabuku uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chonde tumizani pepala loyamba ku Sosaite pasanafike pa September 6. Sungani pepala lachiŵiri m’faelo yanu. Pepala lachitatulo mungaligwiritse ntchito ngati poŵerengerera. Mlembi wa mumpingo umene muli woimira za mabuku ndiye amene adzayang’anire kuŵerengeraku. Mlembi ndi woyang’anira wotsogolera wa mumpingo umene muli woimira za mabuku asaine fomuyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena