Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe M’choonadi: Mbali Yachiŵiri—Mwa Kukhala Ofalitsa Ufumu
1 M’mbali yoyamba ya nkhani zino, tinapatsidwa zotsatira za kalembera wosonyeza kuti ana ambiri zedi amene makolo awo ali m’choonadi sanakhalebe ofalitsa. Ambiri a ana ameneŵa ndi a m’mabanja aakulu ndi atumiki otumikira. Komanso, ambiri mwa mabanja ameneŵa sachita maphunziro a banja mokhazikika. M’nkhani ino tidzaona mmene tingayambitsire ana athu kutenga mbali mu utumiki wakumunda ndiponso nthaŵi imene tiyenera kuwayambitsa kuchita zimenezi.
2 Kukonzekeretsa Ana Utumiki Wakumunda: Palibe chifukwa chochedwera kuyambitsa ana kuchita utumiki mpaka atafika zaka zapakati pa 13 ndi 19. Akhoza kuyamba akadali aang’ono malinga ngati akuyenerera. Musawaletse kuyamba ngati ali ndi chidziŵitso ndiponso chikhumbo chotumikira Yehova. Mwina chikhumbocho chikhoza kutha n’kuyamba kukhala ndi zikhumbo zina za Satana ndiponso za dziko lino. Akulu ayenera kugwirizana popenda ana aang’ono ngati akuyenerera kukhala ofalitsa. Safunika kulepheretsedwa kuti sakuyenera kokha chifukwa chakuti ali ndi zaka zochepa.—Sal. 148:12, 13; Mat. 21:16.
3 N’kutheka kuti makolo ena sadziŵa bwinobwino zoyenera kuchita kuti ana awo ayambe utumiki. M’buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, patsamba 99 pamutu wakuti “Kuthandiza Anthu Achichepere,” pali zoyenera kuchita. Ngati ana awowo akufunitsitsa kuyamba kupereka lipoti la utumiki, kholo liyenera kulankhula ndi woyang’anira wotsogolera yemwe adzakonza zoti akulu aŵiri akumane ndi mwanayo pamodzi ndi kholo lakelo. Akulu, pokambirana nkhaniyi ndi kholo la mwanayo, adzaona ngati mwanayo ali wokonzeka kuyamba kupereka lipoti. Mwa zinthu zofunika kupenda ndi mfundo za patsamba 97 mpaka 99 pa kamutu kakuti “Kufitsa Zofunika.” Makolo afunika kukambirana kaye ndi mwana wawoyo mafunso ofunika opezeka m’masamba ameneŵa. Wophunzira Baibulo watsopano safunikira chidziŵitso chakuya cha choonadi kuti ayambe utumiki, chonchonso ana sayenera kuletsedwa ngati akudziŵa choonadi chimene munthu amaphunzira koyambirira, ngati ali amakhalidwe abwino, ndiponso akufuna kutumikira Yehova.
4 Kuwonjezera pa kukulitsa chikhumbo cha ana kuti atenge mbali mwachangu mu utumiki wachikristu, makolo angapezere ana zida zofunika kukhala nazo. Mwachitsanzo, kodi mwanayo ali ndi Baibulo lakelake? Baibulo n’lofunika osati mu utumiki mokha komanso pamisonkhano. Chifukwa chosoŵa ndalama, makolo angalephere kupezera ana awo mabaibulo. Koma n’chinthu chabwino kwambiri kwa ana chimene chingawalimbikitse ndi kuwathandiza kukula mwauzimu. N’kwabwinonso makolo kugulira ana awo zikwama za muutumiki wakumunda. Izinso zidzalimbikitsa ana kutenga mbali m’ntchito yolalikira. Koma, ana afunika kuphunzitsidwa kufunika kosamala bwino Baibulo ndi chikwama chawo cha muulaliki.
5 Pakambidwa zambiri ponena zokonzekera utumiki wakumunda mwa kuchitira limodzi zitsanzo za ulaliki monga banja. Izi zimalimbikitsa ana athu, komanso zimawathandiza kudziŵa zokanena kwa eninyumba. Monga momwe ana angakonzekere bwino nkhani ya wophunzira, choncho akhoza kukonzekeranso ulaliki pa mutu wina kapena pankhani ya m’magazini. Ena a m’banjamo akhoza kukhala ngati eninyumba, n’kumayankha zimene anthu ambiri m’gawolo amanena. Banja lidzasangalala kuchitira limodzi zimenezi. Makolo angathandize kwambiri kuti zimenezi zikhale zosangalatsa.
6 Pali dongosolo labwino kuti ana aang’ono ameneŵa atenge nawo mbali mu utumiki wachikristu: ndife ololedwa kuwatenga muutumiki ngakhale ngati titayenda anthu atatu. Ngati onse akuchitira umboni, onse angachitire lipoti maola. Mwachitsanzo, ngati munthu wamkulu akuyenda ndi ana aŵiri, onse atatu angapereke lipoti. Zingateronso ngati anthu akuluakulu aŵiri akuyenda ndi mwana m’modzi. Izi zidzathandiza ana kuyamba utumiki mosavuta ndi kumauchita mokhazikika, makamaka ngati ali amsinkhu wosati n’kuyenda okha. Mabanja akuluakulu afunika kupezerapo mwayi pamakonzedwe ameneŵa mwamsanga.
7 Inde, ana anu atha kuyamba utumiki pakalipano. Ngati ali ndi chidziŵitso chokwanira cha choonadi kwakuti atha kufotokoza zimene amakhulupirira ndipo ali n’chikhumbo chotumikira Yehova, bwanji osauza woyang’anira wotsogolera kuti auze akulu aŵiri kudzawapenda ndi kuona ngati akuyenera kukhala ofalitsa?
8 Koma, tingachite chiyani kuti ana athu apite patsogolo m’choonadi? Kiyi yake ndi phunziro la Baibulo labanja. Mbali yotsatira m’nkhaniyi idzalongosola kufunika kwa maphunziro a banja okhazikika ndiponso mmene maphunziroŵa angakhalire ogwira mtima kwambiri.