Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/00 tsamba 3-6
  • Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2001

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2001
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Timitu
  • Malangizo
  • NDANDANDA
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 10/00 tsamba 3-6

Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2001

Malangizo

Mu 2001, otsatiraŵa ndiwo adzakhale makonzedwe pochititsa Sukulu ya Utumiki Wateokalase.

MABUKU OPHUNZIRA: Revised Nyanja (Union) Version [bi53], Nsanja ya Olonda [w-CN], Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN], adzakhala magwero a nkhani zimene zidzagaŵiridwa.

Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje achidule. Palibe chifukwa choperekera chithunzithunzi cha zimene zili pa pulogalamu. Pamene woyang’anira sukulu aitanira wokamba nkhani iliyonse, iye ndiye adzatchula nkhani imene idzakambidwa. Ndiyeno n’kupitiriza motere:

NKHANI NA. 1: Mphindi 15. Imeneyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira, ndipo idzatengedwa mu Nsanja ya Olonda kapena mu buku la Munthu Wamkulu Woposa Wonse Amene Anakhalako. Ngati yatengedwa mu Nsanja ya Olonda, iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 15 yopanda mafunso obwereramo; ngati yatengedwa mu buku la Munthu Wamkulu ikambidwe ngati nkhani yachilangizo ya mphindi 10 mpaka 12, kenako mphindi 3 mpaka 5 za mafunso obwereramo, kugwiritsa ntchito mafunso osindikizidwa m’bukulo. Cholinga chake sichiyenera kukhala cha kungokamba nkhaniyo koma kusamalira kwambiri za phindu lenileni la chidziŵitso chimene chikufotokozedwa, mukumagogomeza mfundo zomwe zidzakhala zothandiza kwambiri mpingowo. Gwiritsani ntchito mutu wosonyezedwa.

Abale opatsidwa nkhani imeneyi ayenera kukhala osamala kusunga nthaŵi. Uphungu wamseri ungaperekedwe ngati kuli kofunika kapena ngati wapemphedwa ndi wokamba nkhaniyo.

MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 6. Nkhaniyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira amene adzagwiritsa ntchito mfundozo pa zofunika za kumaloko. Mutu wa nkhani n’ngwosafunikira kwenikweni. Siyenera kukhala chidule wamba cha kuŵerenga kwa mlunguwo. Choyamba perekani chithunzi chachidule cha machaputala onse a mlunguwo pa masekondi 30 mpaka 60. Komabe, cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvetsera kuzindikira chifukwa chake ndi mmene chidziŵitsocho chilili chaphindu kwa ife. Ndiyeno woyang’anira sukulu adzauza ophunzirawo kupita ku makalasi awo osiyanasiyana.

NKHANI NA. 2: Mphindi 5. Iyi ndi nkhani ya kuŵerenga Baibulo kwa mbali yogaŵiridwa kochitidwa ndi mbale. Nkhaniyi idzakambidwa m’sukulu yaikulu limodzinso ndi m’timagulu tinato. Kaŵirikaŵiri mbali zoŵerenga zimakhala zazifupi mololeza wophunzira kukamba mawu oyamba ndi omaliza achidule opereka chidziŵitso pankhaniyo. Zingaphatikizepo mbiri yakale, tanthauzo la ulosi kapena la chiphunzitso, ndi mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zake zachikhalidwe. Mavesi onse ogaŵiridwa ayenera kuŵerengedwa mosalekeza. Komabe, pamene mavesiwo saali ondondozana, wophunzira angatchule vesi lopitirizira kuŵerengako.

NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhaniyi idzapatsidwa kwa mlongo. Mutu wa nkhaniyi udzatengedwa m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Chochitikacho chingakhale umboni wamwamwayi, ulendo wobwereza, kapena phunziro la Baibulo la panyumba, ndipo otenga mbaliwo angakhale pansi kapena kuimirira. Woyang’anira sukulu adzafuna makamaka kuona mmene wophunzirayo adzafotokozera mutu wogaŵiridwawo ndi kuthandiza mwininyumba kusinkhasinkha malemba. Wophunzira wopatsidwa nkhani imeneyi ayenera kudziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi, koma mukhoza kugwiritsa ntchito wothandiza winanso. Chimene chiyenera kusamalidwa kwambiri, si mkhalidwe wa chochitikacho, koma kugwiritsa ntchito Baibulo kogwira mtima.

NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Mutu wa nkhani imeneyi udzatengedwa m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Mbale kapena mlongo angagaŵiridwe Nkhani Na. 4. Pamene ipatsidwa kwa mbale, nthaŵi zonse iyenera kukambidwa monga nkhani zina zonse. Pamene ipatsidwa kwa mlongo, iyenera kuperekedwa mofanana ndi Nkhani Na. 3.

NDANDANDA YOŴERENGA BAIBULO: Aliyense mumpingo akulimbikitsidwa kutsatira ndandanda ya mlungu ndi mlungu ya kuŵerenga Baibulo, imene imafuna kuŵerenga tsamba limodzi patsiku.

CHIDZIŴITSO: Za chidziŵitso china ndi malangizo onena za uphungu, kusunga nthaŵi, kubwereramo kolemba, ndi kukonzekera nkhani, onani patsamba 3 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1996.

NDANDANDA

Jan. 1 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 13-16

Nyimbo Na. 62

Na. 1: Kukhululukira Ena Kutsegula Njira ya Chipulumutso (w99-CN 1/1 mas. 30-1)

Na. 2: 2 Mafumu 14:1-14

Na. 3: Kutaya Mimba—N’chifukwa Chiyani Kuli Koletsedwa? (rs-CN tsa. 210 ndime 6 mpaka tsa. 211 ndime 8)

Na. 4: Kuyankha Munthu Amene Anganene Kuti: ‘Ndili ndi Kuyenera kwa Kupanga Chosankha Pankhani Zimene Zimakhudza Thupi Langa’ (rs-CN tsa. 212 ndime 1)

Jan. 8 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 17-20

Nyimbo Na. 116

Na. 1: Uphungu Umene Uli Wosavuta Kuulandira (w99-CN 1/15 mas. 21-4)

Na. 2: 2 Mafumu 18:1-16

Na. 3: Adamu ndi Hava—Anthu Enieni a M’mbiri? (rs-CN mas. 25-6)

Na. 4: Kuyankha Munthu Amene Anganene Kuti: ‘Uchimo wa Adamu Unali Chifuniro cha Mulungu, Kakonzedwe ka Mulungu’ (rs-CN tsa. 27 ndime 1-2)

Jan. 15 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 21-25

Nyimbo Na. 61

Na. 1: Kuzindikira Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako (gt-CN mawu oyamba ndime 1-15)

Na. 2: 2 Mafumu 21:1-16

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kulambira Makolo kuli Kwachabe? (rs-CN mas. 188-9 ndime 3)

Na. 4: Chifukwa Chimene Kulambira Makolo Sikukondweretsera Yehova Mulungu (rs-CN 189 ndime 4 mpaka tsa. 190 ndime 3)

Jan. 22 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 1-5

Nyimbo Na. 16

Na. 1: Chimene Chinapangitsa Yesu Kukhala Munthu Wamkulu Woposa Onse (gt-CN mawu oyamba ndime 16 mpaka ndime 23)

Na. 2: 1 Mbiri 1:1-27

Na. 3: Kodi Ndani Amene Ali Okana Kristu (rs-CN mas. 414-15 ndime 7)

Na. 4: Kuzindikira Ampatuko (rs-CN tsa. 299 ndime 5 mpaka tsa. 301 ndime 2)

Jan. 29 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 6-10

Nyimbo Na. 73

Na. 1: Mmene Tingasonyezere Kudzichepetsa Kwenikweni (w99-CN 2/1 mas. 6-7)

Na. 2: 1 Mbiri 9:1-21

Na. 3: Kodi Tiyenera Kuwaona Motani Ampatuko? (rs-CN tsa. 301 ndime 3 mpaka tsa. 302 ndime 3)

Na. 4: Kristu Sanamange Tchalitchi pa Petro (rs-CN mas. 196-8 ndime 2)

Feb. 5 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 11-16

Nyimbo Na. 65

Na. 1: Khalani Munthu Wolimbikitsa Kwambiri (w99-CN 2/15 mas. 26-9)

Na. 2: 1 Mbiri 11:1-19

Na. 3: Kodi N’chiyani Chinali Mfungulo Zimene Petro Anagwiritsa Ntchito? (rs-CN tsa. 198 ndime 3 mpaka tsa. 200 ndime 4)

Na. 4: “Oloŵa M’malo mwa Atumwi” Si Akristu Oona (rs-CN tsa. 200 ndime 5 mpaka tsa. 203 ndime 1)

Feb. 12 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 17-23

Nyimbo Na. 122

Na. 1: Valani Kudzichepetsa (w99-CN 3/1 mas. 30-1)

Na. 2: 1 Mbiri 18:1-17

Na. 3: Kodi Armagedo Idzamenyedwera Kuti? (rs-CN mas. 37-9 ndime 3)

Na. 4: Kodi Ndani Komanso N’chiyani Chimene Chidzawonongedwa pa Armagedo? (rs-CN tsa. 39 ndime 4 mpaka tsa. 40 ndime 2)

Feb. 19 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mbiri 24-29

Nyimbo Na. 119

Na. 1: Gabrieli Aonekera kwa Zakariya ndi Mariya (gt-CN mutu 1)

Na. 2: 1 Mbiri 29:1-13

Na. 3: Kodi Ndani Adzapulumuka Armagedo? (rs-CN tsa. 40 ndime 3-8)

Na. 4: Armagedo—Sidzaswa Chikondi cha Mulungu (rs-CN tsa. 41 ndime 1-3)

Feb. 26 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 1-5

Nyimbo Na. 168

Na. 1: Yesu Alemekezedwa Asanabadwe (gt-CN mutu 2)

Na. 2: 2 Mbiri 1:1-17

Na. 3: Palibe Kukhala Wopanda Mbali pa Armagedo (rs-CN tsa. 41 ndime 4-7)

Na. 4: Kodi ndi Chisonkhezero Chayani Chimene Chikukankhira Amitundu ku Armagedo? (rs-CN tsa. 41 ndime 8 mpaka tsa. 42 ndime 1)

Mar. 5 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 6-9

Nyimbo Na. 103

Na. 1: Musagonjetsedwe ndi Nkhaŵa (w99-CN 3/15 mas. 21-3)

Na. 2: 2 Mbiri 8:1-16

Na. 3: Kuzindikira Babulo wa m’Chivumbulutso (rs-CN tsa. 47 ndime 3 mpaka tsa. 48 ndime 1)

Na. 4: Kodi Babulo Wakale Anadziŵika ndi Chiyani? (rs-CN tsa. 48 ndime 2 mpaka tsa. 50 ndime 2)

Mar. 12 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 10-15

Nyimbo Na. 59

Na. 1: Kodi Ndani Amene Amaumba Maganizo Anu? (w99-CN 4/1 mas. 20-2)

Na. 2: 2 Mbiri 10:1-16

Na. 3: Chifukwa Chimene Zipembedzo Zodzinenera Kukhala Zachikristu Zili Mbali ya Babulo Wamkulu (rs-CN tsa. 50 ndime 3 mpaka tsa. 51 ndime 3)

Na. 4: Chifukwa Chake Pakufunika Kutuluka Mofulumira m’Babulo Wamkulu (rs-CN tsa. 51 ndime 4 mpaka tsa. 52 ndime 3)

Mar. 19 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 16-20

Nyimbo Na. 69

Na.1: Tetezani Mtima Wanu ku Mzimu wa Kulambira Baala (w99-CN 4/1 mas. 28-31)

Na. 2: 2 Mbiri 16:1-14

Na. 3: Chimene Ubatizo Uli, Ndiponso Chifukwa Chimene Okhulupirira Amabatizidwira (rs-CN tsa. 364 ndime 1-4)

Na. 4: Ubatizo Wachikristu—Wosawaza Madzi, Si wa Makanda (rs-CN tsa. 364 ndime 5 mpaka tsa. 365 ndime 3)

Mar. 26 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 21-25

Nyimbo Na. 212

Na. 1: Musalephere Kusonyeza Kuyamikira (w99-CN 4/15 mas. 15-17)

Na. 2: 2 Mbiri 22:1-12

Na. 3: Ubatizo Wam’madzi Sumachititsa Kukhululukidwa Machimo (rs-CN tsa. 365 ndime 4 mpaka tsa. 366 ndime 1)

Na. 4: Kodi Ndani Ali Wobatizidwa ndi Mzimu Woyera? (rs-CN tsa. 366 ndime 2 mpaka tsa. 367 ndime 3)

Apr. 2 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 26-29

Nyimbo Na. 49

Na. 1: Kodi Mulungu Amachita Zinthu ‘Mokhotakhota’? (w99-CN 5/1 mas. 28-9)

Na. 2: 2 Mbiri 28:1-15

Na. 3: Ubatizo wa Moto ndi Wosiyana ndi Ubatizo wa Mzimu Woyera (rs-CN tsa. 367 ndime 4 mpaka tsa. 368 ndime 1)

Na. 4: Zifukwa Zophunzirira Baibulo (rs-CN mas. 52-54 ndime 2)

Apr. 9 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 30-33

Nyimbo Na. 1

Na. 1: Kodi Anthu Angalemekeze Bwanji Yehova Mulungu? (w99-CN 5/15 mas. 21-4)

Na. 2: 2 Mbiri 33:1-13

Na. 3: Umboni Wochokera kwa Yesaya ndi Yeremiya wa Kuuziridwa kwa Baibulo (rs-CN tsa. 54 ndime 3 mpaka tsa. 55 ndime 2)

Na. 4: Kukwaniritsidwa kwa Maulosi a Yesu Kusonyeza Kuuziridwa kwa Baibulo (rs-CN tsa. 55 ndime 3 mpaka tsa. 56)

Apr. 16 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mbiri 34-36

Nyimbo Na. 144

Na. 1: Kubadwa kwa Yohane (gt-CN mutu 3)

Na. 2: 2 Mbiri 36:1-16

Na. 3: Baibulo N’logwirizana ndi Sayansi (rs-CN tsa. 56 ndime1 mpaka tsa. 58 ndime 2)

Na. 4: Kuyankha Otsutsa Baibulo (rs-CN tsa. 58 ndime 3 mpaka tsa. 62 ndime 1)

Apr. 23 Kuŵerenga Baibulo: Ezara 1-6

Nyimbo Na. 24

Na. 1: Yosefe Akwatira Mariya Wapakati (gt-CN mutu 4)

Na. 2: Ezara 4:1-16

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Sakondwerera Masiku Akubadwa? (rs-CN mas. 361-63 ndime 3)

Na. 4: N’chifukwa Chiyani Akristu Amasala Mwazi? (rs-CN mas. 313-15 ndime 1)

Apr. 30 Kubwereramo Kolemba. Kuŵerenga Baibulo: Ezara 7-10

Nyimbo Na. 203

May 7 Kuŵerenga Baibulo: Nehemiya 1-5

Nyimbo Na. 56

Na. 1: Kubadwa kwa Yesu—Kuti Ndipo Liti? (gt-CN mutu 5)

Na. 2: Nehemiya 1:1-11

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Amakana Kuikidwa Mwazi? (rs-CN tsa. 315 ndime 2 mpaka tsa. 316 ndime 3)

Na. 4: *Kuyankha Zonena za Anthu Pankhani ya Kuika Mwazi (rs-CN tsa. 317 ndime 1 mpaka tsa. 319 ndime 1)

May 14 Kuŵerenga Baibulo: Nehemiya 6-9

Nyimbo Na. 155

Na. 1: Mpingo Wachikristu Ndi Gwero la Chitonthozo (w99-CN 5/15 mas. 25-8)

Na. 2: Nehemiya 9:1-15

Na. 3: Kodi Kubadwanso Kumatanthauza Chiyani? (rs-CN tsa. 157 ndime 1 mpaka tsa. 158 ndime 8)

Na. 4: Chipulumutso Sichidalira “Kubadwanso” (rs-CN tsa. 159 ndime 1 mpaka tsa. 160 ndime 1)

May 21 Kuŵerenga Baibulo: Nehemiya 10-13

Nyimbo Na. 14

Na. 1: Mwana wa Lonjezo (gt-CN mutu 6)

Na. 2: Nehemiya 12:27-43

Na. 3: *Kuyankha Malingaliro Okhudzana ndi Kubadwanso (rs-CN tsa.160 ndime 3 mpaka tsa. 161 ndime 2)

Na. 4: Kuululira Machimo Ansembe—N’chifukwa Chiyani Sikuli kwa Malemba? (rs-CN tsa. 218 ndime 2 mpaka tsa. 219 ndime 7)

May 28 Kuŵerenga Baibulo: Estere 1-4

Nyimbo Na. 62

Na. 1: Yesu ndi Openda Nyenyezi (gt-CN mutu 7)

Na. 2: Estere1:1-15

Na. 3: Kuulula Machimo Olakwira Mulungu ndi Munthu (rs-CN tsa. 220 ndime 5 mpaka tsa. 221 ndime 6)

Na. 4: N’chifukwa Chiyani Machimo Aakulu Ayenera Kuululidwa kwa Akulu (rs-CN tsa. 221 ndime 7 mpaka tsa. 222 ndime 2

June 4 Kuŵerenga Baibulo: Estere 5-10

Nyimbo Na. 5

Na. 1: Kuthaŵa Wolamulira Wankhalwe (gt-CN mutu 8)

Na. 2: Estere 5:1-14

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kuli Kwanzeru Kukhulupirira Chilengedwe? (rs-CN mas. 74-6 ndime 1)

Na. 4: Kumvetsa Nkhani ya m’Baibulo ya Chilengedwe (rs-CN tsa. 76 ndime 2 mpaka tsa. 78 ndime 3)

June 11 Kuŵerenga Baibulo: Yobu 1-7

Nyimbo Na. 102

Na. 1: Moyo Wabanja Woyambirira wa Yesu (gt-CN mutu 9)

Na. 2: Yobu 1:6-22

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kulambira Mtanda Sikuli kwa m’Malemba? (rs-CN tsa. 305 ndime 3 mpaka tsa. 306 ndime 4)

Na. 4: N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa? (rs-CN mas. 151 ndime 3 mpaka tsa. 152 ndime 6)

June 18 Kuŵerenga Baibulo: Yobu 8-14

Nyimbo Na. 192

Na. 1: Saulo—Chotengera Chosankhika cha Ambuye (w99-CN 5/15 mas. 29-31)

Na. 2: Yobu 8:1-22

Na. 3: Kodi Akufa Ali Kuti, Ndipo Ali mu Mkhalidwe Wotani? (rs-CN tsa. 152 ndime 7 mpaka tsa. 154 ndime 4)

Na. 4: N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizichita Nawo Miyambo ya Maliro? (rs-CN tsa. 155 ndime 1 mpaka tsa. 156 ndime 1)

June 25 Kuŵerenga Baibulo: Yobu 15-21

Nyimbo Na. 81

Na. 1: Mulungu Sazengereza Nalo Lonjezo Lake (w99-CN 6/1 mas. 4-7)

Na. 2: Yobu 17:1-16

Na. 3: *Kuyankha Malingaliro Olakwika Okhudza Imfa (rs-CN tsa. 156 ndime 2 mpaka tsa.157)

Na. 4: Maloto: Ouziridwa ndi Osauziridwa (rs-CN tsa. 246 ndime 3 mpaka tsa. 247)

July 2 Kuŵerenga Baibulo: Yobu 22-29

Nyimbo Na. 173

Na. 1: Kodi Muyenera Kukulitsa Kaonedwe Kanu ka Zinthu? (w99-CN 6/15 mas. 10-13)

Na. 2: Yobu 27:1-23

Na. 3: Mankhwala—Pamene Amakhala Oletsedwa kwa Akristu (rs-CN mas. 248-9 ndime 2)

Na. 4: Chifukwa Chimene Akristu Amakanira Chamba (rs-CN tsa. 250 ndime 1 mpaka tsa. 251 ndime 1)

July 9 Kuŵerenga Baibulo: Yobu 30-35

Nyimbo Na. 108

Na.1: Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Ulosi wa Baibulo (w99-CN 7/15 mas. 4-8)

Na. 2: Yobu 31:1-22

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Amapewa Fodya? (rs-CN tsa. 251 ndime 2 mpaka tsa. 253 ndime 1)

Na. 4: Kodi Tingagonjetse Motani Zizoloŵezi Zoipa (rs-CN tsa. 253 ndime 2 mpaka tsa. 254 ndime 1)

July 16 Kuŵerenga Baibulo: Yobu 36-42

Nyimbo Na. 61

Na. 1: Ku Yerusalemu Ali ndi Zaka 12 (gt-CN mutu 10)

Na. 2: Yobu 36:1-22

Na. 3: Mayiko Sadzalepheretsa Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansi (rs-CN tsa. 131 ndime 2 mpaka tsa. 132 ndime 2)

Na. 4: Kodi Yehova Adzawononga Dziko Lapansi ndi Moto? (rs-CN tsa. 132 ndime 3 mpaka tsa. 133 ndime 5)

July 23 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 1-10

Nyimbo Na. 5

Na. 1: Yohane Akonza Njira ya Yesu (gt-CN mutu 11)

Na. 2: Salmo 3:1–4:8

Na. 3: A Yerusalemu Watsopano Sadzabwereranso pa Dziko Lapansi Ochimwa Atawonongedwa (rs-CN tsa. 134 ndime 1–2)

Na. 4: Kodi Cholinga cha Mulungu Choyambirira cha Dziko Lapansi Chinasintha? (rs-CN tsa. 135 ndime 1-5)

July 30 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 11-18

Nyimbo Na. 182

Na. 1: Zimene Zikuchitika Pobatizidwa Yesu (gt-CN mutu 12)

Na. 2: Salmo 11:1–13:6

Na. 3: Kodi Tingalimbikitse Motani Odwala? (rs-CN tsa. 79 ndime 1-4)

Na. 4: Kodi Tingalimbikitse Motani Ofedwa? (rs-CN tsa. 80 ndime 1-5)

Aug. 6 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 19-26

Nyimbo Na. 117

Na. 1: Kulankhulana Kwabwino—Kiyi ya Ukwati Wabwino (w99-CN 7/15 mas. 21-3)

Na. 2: Salmo 20:1–21:13

Na. 3: Chilimbikitso kwa Ozunzidwa Chifukwa Chochita Chifuniro cha Mulungu (rs-CN tsa. 80 ndime 6 mpaka tsa. 81 ndime 2)

Na. 4: Kodi Mungawalimbikitse Bwanji Otaya Mtima Chifukwa Chosoŵa Chilungamo? (rs-CN tsa. 81 ndime 3-6)

Aug. 13 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 27-34

Nyimbo Na. 130

Na. 1: Filipo—Mlaliki Wokangalika (w99-CN 7/15 mas. 24-5)

Na. 2: Salmo 28:1–29:11

Na. 3: Pali Chilimbikitso Chotani kwa Opanikizika ndi Mavuto Azachuma? (rs-CN tsa. 81 ndime 7 mpaka tsa. 82 ndime 4)

Na. 4: Chilimbikitso kwa Olefuka Chifukwa cha Zophophonya za Iwo Eni (rs-CN tsa. 82 ndime 5-8)

Aug. 20 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 35-39

Nyimbo Na. 18

Na. 1: Chisonkhezero cha Mabwenzi—Kodi Chingakuthandizeni? (w99-CN 8/1 mas. 22-5)

Na. 2: Salmo 38:1-22

Na. 3: Chisinthiko—Chothetsa Nzeru kwa Asayansi (rs-CN tsa. 99 ndime 1 mpaka tsa. 100 ndime 5)

Na. 4: Chisinthiko, Zokwiriridwa Zakale, ndi Kumvetsetseka Kwake (rs-CN tsa. 101 ndime 1 mpaka tsa. 104 ndime 2)

Aug. 27 Kubwereramo Kolemba. Kuŵerenga Baibulo: Salmo 40-47

Nyimbo Na. 91

Sept. 3 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 48-55

Nyimbo Na. 36

Na. 1: Musalole Mkwiyo Ukupunthwitseni (w99-CN 8/15 mas. 8-9)

Na. 2: Salmo 49:1-20

Na. 3: *Kuyankha Zonena Ochirikiza Chisinthiko (rs-CN tsa. 104 ndime 3 mpaka tsa. 106 ndime 3)

Na. 4: N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Alibe Chikhulupiriro? (rs-CN mas. 67-8 ndime 2)

Sept. 10 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 56-65

Nyimbo Na. 44

Na. 1: Kodi Mdyerekezi Ndiye Amatidwalitsa? (w99-CN 9/1 mas. 4-7)

Na. 2: Salmo 59:1-17

Na. 3: Kodi Ndi motani Mmene Munthu Angapezere Chikhulupiriro? (rs-CN tsa. 68 ndime 3 mpaka tsa. 69 ndime 1)

Na. 4: Chikhulupiriro M’chiyembekezo cha Dongosolo Latsopano Lolungama Chisonyezedwa ndi Ntchito (rs-CN tsa. 69 ndime 3 mpaka tsa. 70 ndime 2)

Sept. 17 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 66-71

Nyimbo Na. 210

Na. 1: Sankhani “Dera Lokoma” (w99-CN 9/1 mas. 30-1)

Na. 2: Salmo 69:1-19

Na. 3: Kodi Aneneri Onyenga Tingawadziŵe Motani? (rs-CN mas. 32-3 ndime 4)

Na. 4: Aneneri Oona Nthaŵi Zonse Sanamvetse Nthaŵi ndi Mmene Zinthu Zoloseredwa Zidzachitikira (rs-CN tsa. 33 ndime 5 mpaka tsa. 34 ndime 1)

Sept. 24 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 72-77

Nyimbo Na. 217

Na. 1: Kodi N’kusungiranji Malonjezo Anu? (w99-CN 9/15 mas. 8-11)

Na. 2: Salmo 73:1-24

Na. 3: Mawu a Mneneri Woona Amachirikiza Kulambira Koona (rs-CN tsa. 34 ndime 2-3)

Na. 4: Aneneri Oona Amadziŵika ndi Zipatso Zawo (rs-CN tsa. 35 ndime 1 mpaka tsa. 36 ndime 2)

Oct. 1 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 78-81

Nyimbo Na. 88

Na. 1: Pezani Nzeru Ndipo Landirani Mwambo (w99-CN 9/15 mas. 12-15)

Na. 2: Salmo 78:1-22

Na. 3: Kuyankha Amene Amatitcha Aneneri Onyenga (rs-CN tsa. 36 ndime 3 mpaka tsa. 37 ndime 2)

Na. 4: Mulungu Saikiratu Nthaŵi Yomwe Munthu Adzafa (rs-CN tsa. 114 ndime 2-4)

Oct. 8 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 82-89

Nyimbo Na. 221

Na. 1: Timoteo—‘Mwana Weniweni m’Chikhulupiriro’ (w99-CN 9/15 mas. 29-31)

Na. 2: Salmo 88:1-18

Na. 3: Si Zinthu Zonse Zimene Zimachitika Zimene Zili Chifuniro cha Mulungu (rs-CN tsa. 115 ndime 1 mpaka tsa. 116 ndime 5)

Na. 4: Mulungu Sadziŵiratu ndi Kulinganiziratu Kanthu Kali Konse (rs-CN tsa. 116 ndime 6 mpaka tsa. 117 ndime 1)

Oct. 15 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 90-98

Nyimbo Na. 134

Na. 1: Olimba Pokana Kuchita Tchimo (w99-CN 10/1 mas. 28-31)

Na. 2: Salmo 90:1-17

Na. 3: Mphamvu ya Mulungu Yodziŵiratu ndi Kulinganiziratu Zinthu (rs-CN tsa. 117 ndime 2-5)

Na. 4: Chifukwa Chake Mulungu Sanagwiritse Ntchito Mphamvu Yodziŵiratu kwa Adamu (rs-CN tsa. 118 ndime 1-3)

Oct. 22 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 99-105

Nyimbo Na. 89

Na. 1: Kuphunzira Njira Yoposa ya Chikondi (w99-CN 10/15 mas. 8-11)

Na. 2: Salmo 103:1-22

Na. 3: Mulungu Sanalinganiziretu za Yakobo, Esau, Kapena Yudasi (rs-CN tsa. 119 ndime 1-3)

Na. 4: Ndi M’lingaliro Lotani Limene Mpingo Wachikristu Unaikidwiratu? (rs-CN tsa. 119 ndime 4 mpaka tsa. 120 ndime 1)

Oct. 29 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 106-109

Nyimbo Na. 214

Na. 1: “Yehova Apatsa Nzeru” (w99-CN 11/15 mas. 24-7)

Na. 2: Salmo 107:1-19

Na. 3: Kodi Baibulo Limanenanji za Kukhulupirira Nyenyezi? (rs-CN tsa. 120 ndime 2 mpaka tsa. 121 ndime 4)

Na. 4: Kodi Zifukwa Zina Zabwino Zokhulupirira Mulungu N’zotani? (rs-CN tsa. 307 ndime 1-8)

Nov. 5 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 110-118

Nyimbo Na. 14

Na. 1: Uthenga wa m’Chivumbulutso—Kodi Ndi Woopsa Kapena Ndi Wotipatsa Chiyembekezo? (w99-CN 12/1 mas. 5-8)

Na. 2: Salmo 112:1–113:9

Na. 3: Zoipa ndi Mavuto Sizitsimikizira Kuti Kulibe Mulungu (rs-CN tsa. 307 ndime 9 mpaka tsa. 308 ndime 1-2)

Na. 4: Mulungu Ndi Munthu Weniweni Wokhala ndi Malingaliro (rs-CN tsa. 309 ndime 1-7)

Nov. 12 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 119

Nyimbo Na. 35

Na. 1: Musalole Kuti Nyonga Yanu Ikhale Chofooka Chanu (w99-CN 12/1 mas. 26-9)

Na. 2: Salmo 119:1-24

Na. 3: Mulungu Analibe Chiyambi (rs-CN tsa. 309 ndime 8 mpaka tsa. 310 ndime 1)

Na. 4: Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu N’kofunika Kuti Tipulumuke (rs-CN tsa. 310 ndime 2-5)

Nov. 19 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 120-137

Nyimbo Na. 113

Na. 1: Kuphunzira Kuchokera Kuziyeso za Yesu (gt-CN mutu 13)

Na. 2: Salmo 120:1–122:9

Na. 3: Kodi Zipembedzo Zonse N’zabwino? (rs-CN tsa. 310 ndime 6 mpaka tsa. 311 ndime 1-2)

Na. 4: Kodi Yesu Ali “Mulungu” Wamtundu Wanji? (rs-CN tsa. 311 ndime 3-4)

Nov. 26 Kuŵerenga Baibulo: Salmo 138-150

Nyimbo Na. 135

Na. 1: Ophunzira Oyamba a Yesu (gt-CN mutu 14)

Na. 2: Salmo 139:1-24

Na. 3: Kuyankha Osakhulupirira Mulungu (rs-CN tsa. 311 ndime 5 mpaka tsa. 313 ndime 1)

Na. 4: Chifukwa Chimene Anthu Alepherera Kukhazikitsa Boma Lolungama (rs-CN tsa. 62 ndime 2 mpaka tsa. 63 ndime 1-4)

Dec. 3 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 1-7

Nyimbo Na. 132

Na. 1: Chozizwitsa Choyamba cha Yesu (gt-CN mutu 15)

Na. 2: Miyambo 4:1-27

Na. 3: Chifukwa Chimene Zoyesayesa za Anthu Zobweretsa Mpumulo Sizingatheke (rs-CN tsa. 63 ndime 5 mpaka tsa. 64 ndime 1-2)

Na. 4: Ufumu wa Mulungu Ndiwo Yankho Lokha pa Zosoŵa za Anthu (rs-CN tsa. 64 ndime 6 mpaka tsa. 65 ndime 3)

Dec. 10 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 8-13

Nyimbo Na. 31

Na. 1: Changu cha Kulambira Yehova (gt-CN mutu 16)

Na. 2: Miyambo 13:1-25

Na. 3: Maulosi a Baibulo Atsimikizira Kukhala Odalirika (rs-CN tsa. 65 ndime 4 mpaka tsa. 66)

Na. 4: Kuchiritsa Kozizwitsa Lerolino Sikuchitidwa mwa Mzimu wa Mulungu (rs-CN tsa. 166 ndime 1-4)

Dec. 17 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 14-19

Nyimbo Na. 35

Na. 1: Kuphunzitsa Nikodemo (gt-CN mutu 17)

Na. 2: Miyambo 16:1-25

Na. 3: Kusiyana kwa Kuchiritsa kwa Yesu ndi Atumwi Ake ndi kwa M’tsiku Lathu (rs-CN tsa. 167 ndime 1-4)

Na. 4: Mmene Akristu Oona Amadziŵikira Lerolino (rs-CN tsa. 167 ndime 5 mpaka tsa. 168 ndime 1-4)

Dec. 24 Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 20-25

Nyimbo Na. 9

Na. 1: Yohane Achepa, Yesu Akula (gt-CN mutu 18)

Na. 2: Miyambo 20:1-30

Na. 3: Chifukwa Chimene Mphatso Zochiritsa Zinaperekedwera M’zaka za Zana Loyamba (rs-CN tsa. 169 ndime 1-4)

Na. 4: Kodi Pali Chiyembekezo Chotani cha Kuchiritsidwa Kwenikweni kwa Anthu Onse? (rs-CN tsa. 169 ndime 5 mpaka tsa. 170 ndime 1-2)

Dec. 31 Kubwereramo Kolemba. Kuŵerenga Baibulo: Miyambo 26-31

Nyimbo Na. 180

Ngati nthaŵi ilola, pendani mayankho amene angakhale othandiza poyankha zimene anthu m’gawolo amanena, kutsutsa, ndi zina zotero.

S-38-CN 10/00

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena