Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/01 tsamba 2-3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 1/01 tsamba 2-3

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu January: Lililonse la masamba 192 lofalitsidwa mu 1986 kapena chakachi chisanafike limene mpingo ungakhale nalo. February: Bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Paulendo wobwereza tikapeza achidwi, tiwaike pa mndandanda wa anthu amene timagaŵira magazini. Gaŵirani buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha ndi bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.

◼ Ofalitsa obatizidwa onse amene adzapezeka pa Msonkhano wa Utumiki mlungu woyambira January 8 adzalandira khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu ndi makadi a ana awo.

◼ Kuyambira mu February osapyola March 4, nkhani yatsopano yapoyera ya oyang’anira dera idzakhala yakuti “Tsiku la Chiŵeruzo—Nthaŵi Yoopsa Kapena Yopatsa Chiyembekezo?”

◼ Mipingo iyenera kupanga makonzedwe abwino odzachita Chikumbutso chaka chino Lamlungu, pa April 8, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, zizindikiro za Chikumbutso zisayendetsedwe kufikira dzuŵa litaloŵa. Funsani odziŵa zanyengo kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yoloŵera dzuŵa m’dera lanulo. Popeza tsiku limeneli sikudzakhala misonkhano koma kukumana kopita mu utumiki wakumunda, konzani kudzachita phunziro la Nsanja ya Olonda tsiku lina. Oyang’anira dera ayenera kusintha ndandanda yawo ya misonkhano mlunguwo malinga ndi mikhalidwe yakumaloko. Ngakhale kuti n’kwabwino kuti mpingo uliwonse uchite Chikumbutso pawokha, nthaŵi zina si zitheka. Kumene mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mpingo umodzi kapena yoposerapo ingapeze malo ena odzagwiritsa ntchito madzulo a tsikuli. Tikupereka malingaliro akuti, ngati kungatheke mapulogalamu akatha pazipita mphindi zosachepera 40 ena asanayambe, kuti onse apindule mokwanira ndi nthaŵiyo, kulonjera alendo ndiponso kulimbikitsa achatsopano. Bungwe la akulu liyenera kusankha makonzedwe amene angakhale abwino kwambiri pampingopo.

◼ Nkhani yapoyera yapadera ya nyengo ya Chikumbutso cha 2001 idzakambidwa Lamlungu, pa April 1. Mutu wa nkhani udzakhala wakuti “Kodi Ndani Angapulumutsidwe?” Autilaini yake itumizidwa. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera mlungu umenewu idzakhala ndi nkhani yapaderayi mlungu woyambira April 9. Mpingo uliwonse usakhale ndi nkhani yapaderayi pasanafike pa April 1, 2001.

◼ Vinyo wa Chikumbukutso mudzatha kumupeza pagalimoto la Sosaite mu February ndi March 2001.

(Zapitirizidwa pa tsa. 3, danga 1)

Zilengezo(Zapitirizidwa)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena