Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/01 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira January 8
  • Mlungu Woyambira January 15
  • Mlungu Woyambira January 22
  • Mlungu Woyambira January 29
  • Mlungu Woyambira February 5
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 1/01 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira January 8

Nyimbo Na. 29

Mph. 7: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 13: ‘Muwalitse Kuunika Kwanu.’a Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1997, tsamba 15, ndime 12-13. Limbikitsani onse kupezerapo mwayi pampata uliwonse kuchitira umboni.

Mph. 25: Makonzedwe Achikondi a Thanzi Lathu. Nkhani yokambidwa ndi mkulu woyeneretsedwa, yochokera m’kalata ya December 1, 2000 ndi pa autilaini ya Sosaite. Gogomezerani kuti chitetezo chalamulo chabwino kwambiri pokana kuikidwa magazi ndicho kusaina khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu. Ofalitsa obatizidwa alandira khadili pamapeto pa msonkhano uno, koma LISALEMBEDWE lero. Mpingo uyenera kukhala ndi makadi okwanira kuti ugaŵire. Makadiŵa adzasainidwa, kuikira umboni ndi kulembapo deti pamapeto pa Phunziro la Buku la Mpingo lotsatira ndipo afuna thandizo wochititsa phunziro la buku adzawathandiza. Amene adzasaine monga mboni ayenera kuonadi mwinikhadilo akusaina. Ochititsa phunziro la buku atsimikizire kuti onse m’gulu lawo athandizidwa zimene akufuna polemba khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu. Makadi a Ana alipo ndipo makolo angatenge pamapeto pa msonkhano uno. Ofalitsa osabatizidwa angalembe makadi awoawo oti azigwiritsa ntchito iwo ndi ana awo, mwa kukopera mawu a pakhadili ndi kuwasintha kuti agwirizane ndi mikhalidwe yawo komanso zikhulupiriro zawo.

Nyimbo Na. 1 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 15

Nyimbo Na. 51

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: Kodi Mukusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku? Nkhani ndi kufunsa. Pendani Nsanja ya Olonda ya December 15, 1996, masamba 17-18, ndime 12-14, imene ikufotokoza ubwino wokambirana lemba latsiku monga banja. Funsani am’banja, omwe akukumbukira zimene anakambirana posachedwapa palemba la tsiku zomwe zinawathandiza kwambiri ndipo apereke chifukwa chake. Nenani motsindika kuti izi ziyenera kukhala pa pulogalamu yanthaŵi zonse ya phunziro la banja yokonzedwa n’cholinga cholimbitsa mabanja athu ndiponso kusonkhezera banja kukhala lachangu mu utumiki.

Nyimbo Na. 67 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 22

Nyimbo Na. 90

Mph. 7: Zilengezo za pampingo.

Mph. 18: Mmene Tingakonzere Mawu Oyamba. Nkhani ndi zitsanzo. Pendani mfundo zazikulu za m’buku la Kukambitsirana, tsamba 9. Sonyezani mmene tingasankhire mawu oyamba ogwirizana bwino kwambiri ndi khalidwe lathu, umunthu wathu ndi gawo lathu. Pendani zitsanzo za mawu oyamba amene angagwiritsidwe ntchito ndi bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri mogwiritsa ntchito mawuwo. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 1997, tsamba 8.) Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito moyenera malingaliro a m’buku la Kukambitsirana ndi Utumiki Wathu wa Ufumu mu utumiki wawo wakumunda.

Mph. 20: “Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe M’choonadi. Mbali Yachisanu: Mwa Kuchitira Zinthu Pamodzi.” Nkhani ya mkulu ya mafunso ndi mayankho. Funsani mafunso pandime zosiyanasiyana kwa anthu osiyanasiyana mwa omvetsera: ndime 2 mpaka 4 kwa anthu opanda ana; 5 mpaka 6 kwa makolo; 7 kwa achinyamata. Ŵerengani ndime zonse.

Nyimbo Na. 96 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 29

Nyimbo Na. 139

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a January. Tchulani mabuku ogaŵira mu February, ndiponso mabuku amene mpingo uli nawo.

Mph. 15: “Mvetserani Bwinobwino.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Pendani mfundo za mu Buku Lolangiza la Sukulu, masamba 27-8, ndime 15-17. Tingayese bwino kwambiri kumvetsera kwathu mwa kuona kuchuluka kwa zimene timakumbukira. Pemphani omvetsera kutchula zina mwa mfundo zazikulu zomwe zakambidwa lero m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase.

Mph. 20: “Makolo—Khomerezani Zizoloŵezi Zabwino mwa Ana Anu.” Nkhani ndi kufunsa makolo amene ana awo akuchita bwino mwauzimu. Makolowo anene zimene achita kuti ana awo ayambe utumiki wakumunda. Ngati nthaŵi ilola, phatikizanipo malingaliro a m’buku la Chimwemwe cha Banja, masamba 55-9.

Nyimbo Na. 149 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 5

Nyimbo Na. 168

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Kupatulika kwa Makonzedwe a Banja. Nkhani yochokera mu buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Pendani ndi omvetsera mfundo zazikulu pa mutu uliwonse, kudzutsa chidwi cha kuphunzira bukuli pampingo. Limbikitsani mabanja kutenga nawo mbali m’makambirano a mlungu ndi mlungu pa phunziro la buku. Onse afunika kupezekapo nthaŵi zonse, kukhala ofunitsitsa kuphunzira zambiri za Mlengi wathu Wamkulu.

Mph. 20: Mungapeze Zosangulutsa Zabwino. Banja likambirane malangizo a mu Galamukani! ya June 8, 1997. Bambo akuda nkhaŵa n’zosangulutsa zimene banja limachita. Akatha kukambirana mwachidule nkhani yakuti “Kodi Nchiyani Chachitikira Zosangulutsa?” (masamba 18-21), akambe mitundu ya zosangulutsa imene ingakhale yabwino ndi yopindulitsa. Pendani nkhani m’buku la Uminisitala Wathu, masamba 131-2, pakamutu kakuti “Kusangulutsa,” ndi masamba 135-6, pakamutu kakuti “Chitani Zonse Kuulemerero wa Mulungu.” Nenani motsindika udindo wa makolo wotsogolera ndiponso kufunika kwakuti m’banjamo agwirizane kuti banja lonse lipindule.

Nyimbo Na. 190 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena