Kodi Mumayamikira Makonzedwe Opepukitsidwa a Kagaŵidwe ka Mabuku?
1 Ntchito ya Ufumu ikukuladi mofulumira padziko lonse lapansi. (Yes. 60:22) Makonzedwe opepukitsidwa a kagaŵidwe ka mabuku popanda mtengo weniweni tsopano atha chaka ndi miyezi inayi akugwira ntchito. Ndipo taona kuchuluka kwa mabuku ndi magazini amene timagaŵira mu utumiki wathu wakumunda m’Malaŵi muno. Choncho, tikuwafikira anthu onga nkhosa ofuna kuphunzira za Yehova Mulungu ndiponso zinthu zabwino kwambiri zimene wasungira anthu.
2 Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2000, unanena kuti: ‘Sitikakamizika, komanso si cholinga chathu, kupereka mabuku mwachisawawa kwa munthu aliyense amene angalandire. Monga mmene timagwiritsira ntchito mwanzeru zinthu zathu, wofalitsa aliyense ali ndi udindo kuonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito mwanzeru mabuku amene Sosaite ikumupatsa kudzera ku mpingo wake popanda kumulipiritsa. Pamene Sosaite ikupereka mabuku kwa ofalitsa mosalipiritsa, mwachionekere sizikutanthauza kuti, siiwononga ndalama popanga ndi powatumiza. Onse ayenera kuzindikira makamaka kufunika kwa mabuku athu pothandiza anthu oona mtima ofuna kudziŵa Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Kristu molondola.—Yoh. 17:3.’
3 Komabe, kuyambira kale ntchito yathu imathandizidwa ndi zopereka zaufulu. Makonzedwe opepukitsidwa akagaŵidwe ka mabuku ameneŵa amasonyeza kuti sitilalikira uthenga wabwino kuti tipeze ndalama. “Sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nawo mawu a Mulungu; koma monga mwa Mulungu,” tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—2 Akor. 2:17; Mat. 24:14.
4 Komabe zikuoneka kuti, ofalitsa ena akufunika kuwakumbutsa udindo wa mutu wa banja potenga mabuku ndi magazini abanja lake. Wofalitsa kapena munthu wachidwi akafuna kutenga mabuku kapena magazini pa Nyumba ya Ufumu, angatenge popanda ‘kulipira’ zinthu zimene watengazo. Magazini amene mwatenga ndiponso amene mukagaŵire m’munda asamakhale ochuluka mopambanitsa. Bambo, yemwe ndi mutu wa banja ali ndi udindo wotengera mkazi wake ndi ana ake zimene akufuna. Mayi achite zimenezi ngati bambo palibe.
5 Komabe, makolo ena amalekera ana awo kukatenga okha mabuku ndi magazini pa Nyumba ya Ufumu. Inde ndi bwino kuti ana odziŵa kuŵerenga azikhala ndi mabuku komanso magazini awoawo, koma ndi bwinonso kuti bambo azikawatengera anawo zinthu zimenezi. Tikatero tidzasonyeza mtima wabwino kwa ena ofuna kutenga mwadongosolo—1 Akor. 14:40.
6 Mukukumbukira kuti ndalama zimene mosapeŵeka zimawonongedwa popanga komanso potumiza mabuku ndi magazini zimalipiridwa ndi zopereka zaufulu za atumiki odzipatulira a Yehova zothandizira ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse ndiponso yopanga ophunzira a Yesu. Ngakhale kuti nthaŵi zonse takhala tikupereka zopereka modzifunira, makonzedwe ameneŵa akum’patsa mpata munthu aliyense kuchita zimene akufuna malinga ndi chikumbumtima chake pothandiza gulu la Yehova lotsogozedwa ndi mzimu. Tonse tili ndi udindo waukulu ndiponso mwayi wolemekeza Yehova ndi chuma chathu. (Miy. 3:9) Mmene timachitira ndi malangizo a mzimu wa Yehova popereka zopereka zathu kudzasonyeza kuti timazindikira kwambiri kuti Yehova amatikhulupirira.—1 Akor. 4:1, 2.
7 Ntchito ya Zopereka Zathu: Chotero, n’koyenera kuti tifotokozenso mwachidule ndiponso momveka bwino mmene zopereka zaufulu zimathandizira ntchito yathu yophunzitsa Baibulo ya padziko lonse. Ndalama zonse zimene timalandira amalipirira zinthu zowonongeka mu ntchito yolalikira Ufumu m’nthaŵi yamakono ino. Kuphatikiza pa kusindikiza mabuku ogaŵira padziko lonse, Sosaite imakonzetsa maofesi anthambi, nyumba za Beteli, sukulu za amishonale ndi zophunzitsa utumiki, kusamalira amishonale, oyang’anira oyendayenda, malo otumizira mabuku, ndi ntchito zina zofunika pokwaniritsa ntchito imene Yesu anapatsa atumwi ake.—Mat. 24:14; 28:19, 20.
8 Kuwonjezeka kwakukulu kwa gulu la Yehova kwapangitsa ena kufunsa zimene angachite kuti athandize. Ambiri sangathe kuthandiza kumanga nthambi zatsopano ndiponso Nyumba za Ufumu kapena kupita ku mayiko akutali kukathandiza kulalikira kumeneko. Koma kuti athandize nawo m’zochitika zosangalatsazi kumlingo umene angathe, ofalitsa ambiri ndi mabanja awo anazoloŵera kupatula kangachepe nthaŵi zonse kothandizira ntchito ya padziko lonse. (Yerekezani ndi 1 Akorinto 16:1, 2.) Mwa njira imeneyi, ntchito zonse za Sosaite zimalipiridwa, kuphatikizapo kutumiza mabuku. Tisaone zopereka zaufulu za ntchito yapadziko lonse monga zolipilira mtengo wa mabuku okha.
9 Pokalalikira eninyumba kapena anthu ena, tikonzekere kukambirana nawo nkhani za Baibulo. Mawu oyamba osangalatsa komanso osiyanasiyana, ndiponso mitu ya Baibulo yabwino yambiri ili mu Kukambitsirana za m’Malemba. Malinga ndi mmene munthuyo akuchitira ndi uthenga wa Ufumu, wofalitsa angaone mmene angachitire pankhani yogaŵira mabuku. Ngati akuoneka kuti alibe chidwi chokwanira choti n’kum’patsa buku kapena zofalitsa zina, mungaone mmene mungathetsere kukambiranako mwanzeru, ndi kupita ku nyumba ina. Mwina mungasiye thirakiti ngati munthuyo alonjeza kuti aliŵerenga. Onetsetsani ngati ali ndi chidwi kuti mudzapitekonso. Mungachitenso zimenezi ngati mulibe nthaŵi yokwanira yoti n’kukambirana mwachifatse, mwina chifukwa chakuti munthuyo watanganidwa kapena simunam’fikire nthaŵi yabwino.
10 Makonzedwe opepukitsidwa a kagaŵidwe ka mabuku akutithandiza kuika patsogolo cholinga chathu cholalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndiponso kupanga ophunzira a Yesu Kristu. Mosiyaniranatu ndi magulu “opemphetsa ndalama,” Mboni za Yehova zimasangalala kuona kuti mabuku akuperekedwa kwa anthu onse mosawauza mtengo. Sitipempha m’pang’ono pomwe zopereka zolipirira ntchito yapadziko lonse kwa anthu amene alibe chidwi ndi uthenga wathu. Zopereka zonse zimagwiritsidwa ntchito kulipirira ntchito yophunzitsa Baibulo ya padziko lonse imeneyi, chifukwa ogwira ntchito m’gululi ndi odzifunira ndipo salandira malipiro kapena chiwongola dzanja. Nkhani ya zopereka zothandizira ntchito yapadziko lonse timakamba ndi anthu okhawo amene amafunsa kapena kuchita chidwi ndi ntchito yathu.
11 Pofutukula utumiki wathu mwachangu, tikumagwiritsa ntchito mwanzeru mabuku a Sosaite amtengo wapataliwa, Yehova adzapitiriza kudalitsa. Anthu amitima yabwino kulikonse amayamikira kalongosoledwe kathu komveka ka utumiki wathu ndipo amasangalala kusonyeza kuthandiza kwawo mwa zopereka zawo zaufulu. Ngakhale zili choncho tikumbukire kuti ndalama zowonongedwa popanga ndiponso potumiza mabuku ndi magazini kwenikweni zimapezeka mwa zopereka za atumiki a Yehova zothandizira ntchito ya padziko lonse yolalikira ndi kupanga ophunzira. Inde, monga atumiki odzipatulira a Yehova, kodi mumayamikira makonzedwe opepukitsidwa akagaŵidwe ka mabuku?