Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/01 tsamba 5-6
  • Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 5/01 tsamba 5-6

Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu

1 M’nthaŵi zakale anthu a Mulungu ambiri anali odziŵa kulemba ndi kuŵerenga. Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Mose analemba mabuku asanu oyambirira a m’Baibulo. Yemwe analoŵa m’malo mwake, Yoswa, analamulidwa kuŵerenga Malemba “usana ndi usiku” kuti agwire bwino ntchito imene Mulungu anam’patsa. Ndipo Mulungu analamula kuti mafumu achiisrayeli, akaloŵa ufumu, azikopera Chilamulo ndi kumaŵerenga tsiku ndi tsiku.—Yos. 1:8; Deut. 17:18, 19.

2 Yesu m’masunagoge ankasanthula mipukutu yonse youziridwa ya Malemba Achihebri, nthaŵi ina anaŵerenga pagulu ndi kutanthauzira lembalo kuti linali kunena za iyeyo. Atumwi akenso anali odziŵa kulemba ndi kuŵerenga, anagwira mawu ndi kutchula Malemba Achihebri kambirimbiri m’zolemba zawo.—Luka 4:16-21; Mac. 17:11.

3 Anthu a Mulungu Lerolino: Yesu anauza otsatira ake ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, kusunga zinthu zonse zimene [iye] anawalamulira.’ Analoseranso kuti “uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.”—Mat. 24:14; 28:19, 20.

4 Monga Akristu a m’zaka za zana loyamba, Mboni za Yehova lerolino zikugwira ntchito imeneyi mwa kuphunzitsa mwachangu ndiponso kulalikira. Ndipo zafalitsanso uthenga wabwino wa Ufumu kudzera m’mabuku. Anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi alabadira uthengawo ndipo akhala ophunzira a Kristu. Pakati pawo pali amuna ndi akazi amene satha kuŵerenga kapena kulemba. Anthu osaphunzira ameneŵa sali Akristu onyozeka—ambiri atumikira Mulungu mokhulupirika zaka zambiri, apirira zizunzo zachipembedzo, ndipo asonyeza kukonda kwawo Yehova mwa kusungabe malamulo ake.—1 Yoh. 5:3.

5 Ambiri a iwo amalakalaka atadziŵa kuŵerenga ndi kulemba, pozindikira kuti kuphunzira ndicho chinsinsi chochita nawo zambiri m’kulambira kwawo Mulungu. Pa misonkhano, amafuna kutsatira pamene Baibulo ndi zofalitsa zachikristu zikuŵerengedwa, ndipo amafuna kuŵerenga mawu a nyimbo kotero kuti aziimbira limodzi ndi abale ndi alongo awo auzimu. Panyumba, amalakalaka kudzilimbikitsa ndiponso kulimbikitsa mabanja awo mwa kuphunzira Baibulo. Mu utumiki, amalakalaka kuphunzitsa ena choonadi cha Mawu a Mulungu popanda kudalira wina kuwaŵerengera.

6 Kuphunzira Kuŵerenga: Pofuna kuthetsa vutoli, Mboni za Yehova zakonza njira yothandiza kuti anthu ambiri m’mipingo yawo ngakhalenso aliyense payekha adziŵe kuŵerenga. Padziko lonse, zaphunzitsa amuna ndi akazi ambirimbiri. Pakalipano m’Malaŵi muno, Mboni za Yehova zaphunzitsa anthu oposa 600 kuŵerenga ndi kulemba.

7 N’chifukwa chake, Watch Tower Society yatulutsa mabuku apadera ophunzitsa kuŵerenga. Mu 2000 buku latsopano mwa mabuku ameneŵa, lamutu wakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba, linatuluka m’Chicheŵa. Lakhala chida chabwino kwambiri chophunzitsira anthu osiyanasiyana kuŵerenga ndi kulemba.

8 Tikulimbikitsa mipingo yonse kuyambitsa makalasi okhazikika ophunzitsa anthu achikulire kuŵerenga ndi kulemba mogwiritsa ntchito mabuku a Sosaite. N’zothandiza kukhala ndi kope la mayina a anthu amene amabwera nthaŵi zonse m’kalasi ndiponso tsiku limene anayamba kuphunzira. Zimenezi zidzathandiza Sosaite kapena abale oyendayenda ofuna kudziŵa zambiri za makalasi a mu mpingo wanu. Inde, mutha kukonza zophunzitsa munthu aliyense payekha.

9 Abale kapena alongo amene ayeneretsedwa kuti aziphunzitsa akulimbikitsidwa kuŵerenga malangizo opezeka pa masamba a mawu oyamba a buku la Chicheŵa, pamutu wakuti “Zokhudza Mphunzitsi.” Kuti zinthu ziyende bwino, ŵerengani malangizo ameneŵa bwinobwino musanayambe kuphunzitsa.

10 Ndi bwinonso kuti ofalitsa onse, makamaka akulu, aŵerengenso malingaliro othandiza opezeka mu Galamukani! ya March 8, 1994.

11 Mlengi wathu, Yehova Mulungu, mokoma mtima wapatsa anthu luso la kuŵerenga ndi kulemba. Koma maluso ameneŵa sapezeka popanda khama. Mphoto yaikulu koposa yophunzirira kuŵerenga ndi kulemba ndiyo kudziŵa Mawu a Mulungu ndi kumvera langizo la Mulungu lakuti: “Ulingiriremo [“uŵerengemo,” NW] usana ndi usiku.”—Yos. 1:8.

[Bokosi patsamba 4]

Malangizo Pophunzitsa Achikulire Kuŵerenga ndi Kulemba

1. N’kofunika kulimbikitsa wophunzira. Paphunziro loyamba, gogomezerani mapindu a kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba, ndipo limbikitsani wophunzira kukhala ndi zolinga zotheka zotenga nthaŵi yaitali ndiponso yochepa.

2. Kuti wophunzira azilimbikira aziphunzira kangapo mlungu uliwonse. Sikokwanira kuphunzira kamodzi pamlungu. Wophunzira azilemba homuweki asanayambe phunziro lina.

3. Musafune zambiri kapena kuuza wophunzirayo zinthu zochuluka paphunziro limodzi. Zimenezi zingam’chititse ulesi ndiponso atha kusiya kupezeka m’kalasi.

4. Khalani wolimbikitsa ndi wodalirika nthaŵi zonse. Kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba kumakula pang’onopang’ono. Wophunzira ayenera kukhutira kuti akupita patsogolo.

5. Limbikitsani wophunzirayo kugwiritsira ntchito mwamsanga zimene akuphunzira m’moyo wake wa tsiku ndi tsiku.

6. Musathere nthaŵi pankhani zosafunika. Achikulire ndi anthu otanganidwa. Gwiritsani ntchito nthaŵi yophunzira kuphunzitsa zinthu zofunika kwambiri.

7. Nthaŵi zonse lemekezani wophunzira, m’patseni ulemu woyenera. Musam’chititse manyazi kapena kumunyoza.

8. Zindikirani mavuto a aliyense. Wophunzira angalephere kuŵerenga zilembo zazing’ono chifukwa chosoŵa magalasi. Ena samvetsetsa ndipo angamavutike kumva katchulidwe kolondola ka mawu.

9. Wophunzira ayenera kuphunzira kulemba chilembo chimodzichimodzi (mosindikiza) asanayambe kulemba chikhukhuza (kalembedwe kolumikiza zilembo). N’kosavuta kuphunzira kulemba chimodzichimodzi ndipo sizivuta kulemba, ndiponso zilembo zake zimafanana kwambiri ndi zija zosindikizidwa m’mabuku.

10. Kaŵirikaŵiri munthu amayamba kudziŵa kuŵerenga asanadziŵe kulemba. Musachedwe kuyamba maphunziro ena oŵerenga ngati wophunzira akulephera kulemba homuweki. Ndiponso, kumbukirani kuti wophunzira amaphunzira mosavuta zilembo zatsopano komanso kuzikumbukira ngati akuyesa kuzilemba.

11. Ngakhale kuti wophunzira wachikulire angagwire ntchito yovuta yamanja, kulemba ndi bolopeni kapena pensulo kungakhale chinthu chovuta ndi chogwetsa ulesi kwa iye. Musaumirire kuti azilemba zilembo zooneka bwino.

[Bokosi patsamba 6]

Kuŵerenga Mokweza

Pa Chivumbulutso 1:3 timaŵerenga kuti: “Wodala iye amene aŵerenga [mokweza, NW] . . . ” M’gawo lathu lino abale ndi alongo 601 amene aphunzira kuŵerenga m’njira imeneyi anakhulupirira mawuwa. Njirayi ikuthandizanso anthu a Mulungu osiyanasiyana m’mipingo yambiri. Malinga ndi Malipoti a Kuphunzira Kulemba ndi Kuŵerenga okwana 318 amene talandira, mwa ofalitsa 23,178 amene analembetsa ofalitsa pafupifupi 601 tsopano amatha kuŵerenga Chicheŵa. Komabe, abale ndi alongo 6,905 sakuthabe kulemba ndi kuŵerenga. Tikukhulupirira kuti ambiri a ameneŵa ali m’gulu la ofalitsa amene angolembetsa kumene m’makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga m’mipingo yosiyanasiyana.

Kodi mpingo wanu uli ndi makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga? Ngati ulibe yambani lero. Angamachitikire m’chipinda china chapafupi panthaŵi ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Ngati makalasiwo angafune nthaŵi yotalikirapo, mungakonze kuti muziwachita nthaŵi ina kapena kangapo pa mlungu.

Kodi mumadziŵa kuŵerenga ndi kulemba bwino? Bwanji osadzipereka kuti inunso muphunzitseko amene mpaka pano sadziŵa kuŵerenga?—Mac. 20:35.

Kodi simudziŵa kuŵerenga? Ndiyetu lembetsani m’kalasi yophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga imene ili mumpingo wanu ndipo muzipezekapo nthaŵi zonse kuti inunso musangalale ndi kuŵerenga mokweza m’miyezi ikubwerayi.—Hab. 2:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena