Bokosi la Mafunso
◼ Ngati mwana wa mbale waudindo mu mpingo wachita dama kapena ndi wa khalidwe loipa, kodi ziyeneretso za bambo ake ayenera kuzipenda liti, ndipo zipendedwe ndi ndani?
Kaya mwanayo ndi wofalitsa wobatizidwa kapena wosabatizidwa, choyamba komiti ya chiweruzo yosankhidwa ndi bungwe la akulu idzasamalira nkhani yake malinga ndi zimene zili mu buku la Olinganizidwa, patsamba 148. Bungwe lonse la akulu limapenda ziyeneretso za bambo nthaŵi imene ali ndi woyang’anira dera. Akulu pampingopo ayenera kuika nkhaniyi pa ajenda kuti akambirane mlungu umenewo pofuna kuthandiza onse limodzi ndi woyang’anira dera yemwe, kudziŵa zimene akakambirane pankhaniyi. Komabe, bwanji ngati mkuluyo akufuna kuchita apilo pokana zimene bungwe la akulu lagamula ndiponso zimene woyang’anira dera wavomereza kuti atule udindo wake? Palibe makonzedwe a komiti ya apilo, ngati mmene zimakhalira pankhani zachiŵeruzo. Mbaleyo angalembe kalata ku ofesi ya Sosaite yosonyeza kuti sakumvetsa chimene anam’tulira pansi udindo, koma nthaŵi zambiri ofesi imalembanso kalata kupempha bungwe la akuluwo kuti afotokoze zina zambiri. Ingalemberenso woyang’anira dera kum’funsa mmene akuonera nkhaniyo. Ngati nkhaniyo ndi yaikulu ndipo pali kusagwirizana maganizo ndi zina zotero, ndi bwino kupeza komiti yapadera kuti ionenso nkhaniyo. Ndiyeno ofesi ya Sosaite idzalingalira bwino mochitira ndi nkhaniyo.
◼ Kodi mumawamvetsa makonzedwe a zopereka zaufulu?
Lerolino ntchito yonse yolalikira ndi kupanga ophunzira imathandizidwa ndi zopereka zaufulu. Mabokosi olembedwa kuti “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse.—Mat. 24:14.” amaikidwa mu Nyumba za Ufumu, momwe anthu amaponya mwadongosolo zopereka zawo mlungu uliwonse, m’milungu iŵiri iliyonse kapena mwezi uliwonse. (1 Akor. 16:2) Tonse tizikumbukira kuti ngakhale timauzanso anthu amene si Mboni kupereka zaufulu, atumiki a Yehova ndiwo gwero lalikulu la thandizo limeneli. Timayamikira kangachepe kalikonse kamene anthu ena amapereka. Tiyenera kuponya m’bokosi zopereka zonse zimene talandira mu utumiki.