Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi paulendo wobwereza, aikeni pa anthu amene mumakawagaŵira magazini. Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji, n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha amasamba 32 awa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo N’chiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani!” Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi iyo Ilikodi? mungagaŵire pamene kuli koyenera kutero.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa June 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo pambuyo pa lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Potithandiza kukonzekera komanso kuti tikaimbe nawo kwambiri pa Misonkhano Yachigawo ya chaka chino yakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu,” Sosaite yasankha nyimbo zotsatirazi zimene zikagwire ntchito: 8, 18, 29, 34, 37, 39, 52, 74, 100, 115, 158, 189, 195, 204, 205, 208, 209, 212. Tonse tikonzekeretu nyimbozi kuti tikaimbire Yehova zitamando ndi mtima wonse komanso mwachimwemwe.
◼ Kuyambira mlungu wa July 30, 2001, tiziphunzira buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1 pa Phunziro la Buku la Mpingo.