Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu February: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati mwapeza munthu wachidwi paulendo wobwereza, mulembetsereni magazini. Gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba.
◼ Polalikira m’magawo osagaŵiridwa, ofalitsa angagaŵire bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso. Angagaŵire buku lina lililonse ngati mwininyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi. Onse ayenera kutenga mathirakiti amitundumitundu okasiya panyumba zimene sanapeze anthu kapena kupatsa anthu amene sanalandire buku. Ayenera kuyesetsa kubwerera kwa anthu amene anachita chidwi, makamaka ngati magawo ameneŵa ali pafupi ndi mipingo.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa March 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki apende ntchito ya apainiya okhazikika onse. Ngati wina zikum’vuta kukwanitsa maola, akulu akonze zom’thandiza. Kuti mupeze mfundo za mmene mungam’thandizire, onani makalata apachaka a Sosaite a S-201. Onaninso ndime 12-20 m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1986.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya nyengo ya Chikumbutso cha 2002 idzakambidwa Lamlungu, pa April 14. Mutu wa nkhaniyi udzakhala wakuti “Kumbukirani ‘Tsiku Loopsa’!” Autilaini yake itumizidwa. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera kapena msonkhano mlungu umenewu idzakhala ndi nkhani yapaderayi mlungu winawo. Mpingo uliwonse usakambe nkhani yapaderayi pasanafike pa April 14, 2002.