Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/02 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira February 11
  • Mlungu Woyambira February 18
  • Mlungu Woyambira February 25
  • Mlungu Woyambira March 4
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 2/02 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira February 11

Nyimbo Na. 6

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Pendani Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ndi wa m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo.

Mph. 20: “Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. (Ndime 1 mpaka 13) Ikambidwe ndi woyang’anira wotsogolera. Akambe mwamphamvu zimene tikufuna kuchita m’mwezi wa March ndi miyezi yotsatira. Aliyense agwiritse ntchito kalendala imene ili mu mphatikayo pokonza ndandanda yomwe angakwanitse kuitsatira ya mu utumiki m’mwezi wa March. Alimbikitseni onse amene angathe, kuti achite upainiya wothandiza mwezi umenewu. Pokambirana ndime 7 ndi 8, pemphani anthu omwe anachita upainiya nthaŵi ya Chikumbutso cha chaka chatha kusimba madalitso amene anapeza. Lengezani kuti amene akufuna mafomu ofunsirapo upainiya wothandiza, angatenge mafomuŵa msonkhano uno ukatha.

Mph. 13: Gwiritsani Ntchito Buku la Chidziŵitso Kuyambitsira Maphunziro. Mu March tikufuna kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. Fotokozani mwachidule chokumana nacho cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 1998, patsamba 4, ndime 8. Ngati wina wayambitsa phunziro posachedwapa mwa kugwiritsa ntchito buku la Chidziŵitso, achite chitsanzo cha zomwe zinachitika. Kumbutsani anthu onse za “Mfundo Zimene Mungagwiritse Ntchito Pogaŵira Buku la Chidziŵitso,” mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002. Mogwiritsa ntchito bukuli, sonyezani chitsanzo cha momwe mungagwiritsire ntchito mfundo imodzi ya patsamba 6 mu mphatikayi pa mutu wakuti “Njira Yolunjika.”

Nyimbo Na. 49 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 18

Nyimbo Na. 95

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 12: “Anthu Achimwemwe Kwambiri Padziko Lapansi.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo mwachidule “Masitepe Opezera Chimwemwe,” omwe ali patsamba 6 mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1997.

Mph. 25: “Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. (Ndime 14 mpaka 23) Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Pendani makonzedwe apadera amene akuchitika pampingopo pokonzekera kugwira ntchito yochuluka m’mwezi wa March. Fotokozani ndandanda yonse ya misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda imene yakonzedwa m’mwezi umenewu. Gogomezerani kuti alimbikitse anthu ozirala ndiponso athandize ana ndi ophunzira Baibulo kuti ayenerere kukhala ofalitsa osabatizidwa. Lengezani mayina a anthu amene achite upainiya wothandiza mwezi wa March, ndipo limbikitsani ena kulingalira mozama zochita nawo upainiya.

Nyimbo Na. 143 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 25

Nyimbo Na. 174

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini.” Pemphani ofalitsa kunena momwe mbali ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu imeneyi yawathandizira kukonzekera bwino kugwirizanitsa nkhanizi ndi zinthu zosautsa za masiku oipa ano. Kodi anthu ena anakumana ndi zotani pamene anali kulimbikitsa ndi kuthandiza anthu kupeza mayankho a m’Baibulo a mafunso ovutitsa maganizo? Mwa zitsanzo ziŵiri zachidule, sonyezani momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya February 15 ndi Galamukani! ya March 8.

Mph. 25: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo a Banja Atanthauzo.” Mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilipo, pemphani kholo limodzi kapena aŵiri kusimba zimene achita kuti phunziro lawo la Baibulo la banja likhale lopindulitsa ndi losangalatsa.

Nyimbo Na. 215 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 4

Nyimbo Na. 207

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Sonyezani zitsanzo zachidule ziŵiri za ulaliki wa magazini—m’chitsanzo chimodzi gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda ya March 1 ndipo chinacho gwiritsani ntchito Galamukani! ya March 8. Chimodzi mwa zitsanzozi achite wachinyamata. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a February.

Mph. 14: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 16: “Kodi N’chifukwa Chiyani Tifunika Kupitiriza Kulalikira?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Malizani ndi kufunsa wofalitsa m’modzi kapena aŵiri amene akhala akulalikira kwa zaka zambiri. Apempheni kuti anene zimene zawapangitsa kulimbikirabe kugwira ntchitoyi ndiponso momwe apindulira.

Nyimbo Na. 223 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena