Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/02 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 5/02 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza munthu wachidwi paulendo wobwereza, muikeni pandandanda ya anthu amene mumakawagaŵira magazini. Gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi, gaŵirani bulosha loyenera limene mpingo uli nalo. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha a masamba 32 aŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso ‘Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? mungawagaŵire pamene kuli koyenera kutero.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa June 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Mipingo yambiri yakhala ikuitanitsa zinthu za paoda yapadera monga makaseti awailesi, madisiki, makaseti a vidiyo ndi Mabaibulo achikuto chofeŵa a New World Translation. Ngakhale kuti zinthu zimenezi n’zofunikadi kukhala nazo ndiponso kuti n’zothandiza kwambiri, si zofunika kwambiri moti mungalephere kuphunzira popanda zida zimenezi, pokhapokha ngati muli ndi vuto lalikulu monga kusamvetsetsa kapena kusaona bwino. Choncho, musanaitanitse zinthu zapaderazi, muyenera kulingalira mofatsa chopereka choyenera cha zinthu zimenezi mwa kuona mitengo yongoyerekezera imene ili m’munsimu ya ndalama zimene zingafunike kuti apange zinthu zimenezi. Mitengo imeneyi si mitengo yake ayi, koma zongotithandiza kuzindikira ndalama zimene zimafunika popanga zinthu zimenezi. Mongokumbutsana, anthu amene ali ndi wailesi ya kaseti, wailesi ya CD kapena amene ali ndi vidiyo, ndi okhawo amene angaitanitse makaseti awailesi, madisiki, kapena kaseti ya vidiyo. ZINTHU ZAODA YAPADERA—MTENGO WONGOYEREKEZERA: Baibulo lachikuto chofeŵa la New World Translation ndi K280 limodzi; Baibulo laling’ono kwambiri lachikuto chofeŵa la New World Translation ndi K220 limodzi; Makaseti awailesi ndi K86 imodzi; Moika Makaseti Mopanda Kanthu ndi K137 imodzi; Makaseti a vidiyo ndi K168 imodzi; Madisiki ndi K35 imodzi.

◼ Cheke cha ntchito ya padziko lonse ndi cha ku Thumba la Ndalama za Nyumba ya Ufumu chimene anthu amaika m’mabokosi a zopereka pa Nyumba ya Ufumu ndi m’misonkhano, kapena chimene amatumiza okha ku ofesi ya nthambi azichilemba kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.” Adiresi ya ofesi ya nthambi ndi Watch Tower Bible and Tract Society, Box 30749, Lilongwe 3.

◼ Ngati galimoto ya mabuku ya Sosaite sinabweretse Utumiki Wathu wa Ufumu wa mpingo wa mwezi wotsatira, woyang’anira wotsogolera azidziŵitsa Dipatimenti Yotumiza Mabuku ku nthambi. Mwachitsanzo, ngati galimoto ya mabuku sinabweretse Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 2002 pa mtokoma wanu wa May, dziŵitsani ofesi ya nthambi mofulumira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena