Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/02 tsamba 6
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 5/02 tsamba 6

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupereka mwamsanga malipoti a utumiki wathu wakumunda mwezi uliwonse?

Tonsefe timasangalala tikamva zinthu zabwino zimene zikuchitika chifukwa cha kulalikira uthenga wa Ufumu. (Onani Miyambo 25:25.) Pa Machitidwe 2:41 pamanena kuti pa tsiku la Pentekoste, Petro atatha kukamba nkhani yake yolimbikitsa, ‘anawonjezereka anthu ngati zikwi zitatu.’ Patapita kanthaŵi pang’ono, chiŵerengero chimenechi chinakula kufika “ngati zikwi zisanu.” (Mac. 4:4) Malipoti ameneŵa anasangalatsa kwambiri Akristu a m’zaka za zana loyamba. Lerolinonso timasangalala kumva malipoti abwino. Timasangalala kumva kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse ikuwayendera bwino abale athu.

Popeza kuti kuwonkhetsa malipoti ameneŵa ndi ntchito yaikulu ndiponso yofuna nthaŵi yambiri, n’kofunika kuti ofalitsa Ufumu onse athandize nawo pantchitoyi. Kodi mumakumbukira kupereka mwachangu malipoti anu mwezi uliwonse?

Timasangalala kwambiri ndi malipoti onena za kuchuluka kwa anthu. Komanso, malipoti amathandiza Sosaite kudziŵa mmene ntchito yapadziko lonse ikupitira patsogolo. Amafuna kuona kumene kukufunika thandizo lochuluka kapena mabuku amene akufunika ndiponso kuchuluka kwake. Malipoti a utumiki wakumunda amathandiza akulu mumpingo uliwonse kudziŵa mbali zofunika kuwongolera. Malipoti abwino amatilimbikitsa, ndipo amatithandiza kupenda utumiki wathu ndikuona pofunika kusintha.

Ofalitsa onse afunika kuzindikira kuti ndi udindo wawo kupereka mwachangu malipoti a utumiki wakumunda mwezi uliwonse. Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo ndiwo angakumbutse ofalitsa za udindo umenewu, popeza kuti amakhalanso atcheru kuthandiza anthu amene akulephera kuchita nawo utumiki wakumunda mokhazikika mwezi uliwonse. Angawakumbutse zimenezi mwezi uliwonse paphunziro la buku lomaliza m’mweziwo kapena panthaŵi ina yoyenera. Ngati ena sanapeze mpata wopereka malipoti a utumiki wakumunda ku Nyumba ya Ufumu, wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo angasonkhanitse malipotiwo n’kum’patsa mlembi panthaŵi yake kuti akawaphatikize pa lipoti la mpingo la mwezi ndi mwezi lopita ku Sosaite. Mlembi azionetsetsa kuti pofika pa 6 mwezi wotsatira azikhala atatumiza lipoti la (S-1) ku Sosaite.

Kuyesetsa kwathu kupereka mokhulupirika ndi mwachangu malipoti a ntchito yathu ya utumiki wakumunda kumachepetsa ntchito ya amene ali ndi udindo wotisamalira mwauzimu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena