Kuyamikira “Nyumba ya Mulungu”
1 “Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi: Kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’Kachisi wake.”—Sal. 27:4.
2 Mfumu Davide amene anali munthu woyamikira anasangalala kapena anakondwa ndi kachisi wa Yehova. Kodi lerolino mumaona malikulu a kulambira koona mofananamo? Nyumba za Beteli zoposa 110 za nthambi za Watch Tower Society ndi zina mwa zinthu zokhudza kulambira Yehova m’masiku athu ano.
3 Kodi dzina lakuti Beteli limatanthauza chiyani kwenikweni? Kodi ndi motani mmene aliyense wa Mboni za Yehova, kaya amatumikira Mulungu pa Beteli kapena ayi, angayamikirire dongosolo limeneli?
4 Dzina Lomwe Limafuna Anthu Odzipereka: “Beteli” ndi dzina loyenerera kwambiri, pakuti liwu Lachihebri lakuti Behth-Elʹ limatanthauza kuti “Nyumba ya Mulungu.” (Gen. 28:19, NW, mawu am’munsi) Inde, Beteli imafanana ndi nyumba yolinganizidwa bwino, kapena ‘nyumba yomangidwa mwanzeru’ imene imaika Mulungu ndiponso cholinga chake patsogolo.—Miy. 24:3.
5 Herta anayamikira kuti: “Moyo wake ndi wofanana ndi moyo wa pabanja. Timachita zinthu mwadongosolo tsiku ndi tsiku.” Iye wakhala akutumikira pa Nyumba ya Beteli ya ku Germany kwa zaka zoposa 45. Aliyense m’banja lalikulu limeneli ali ndi ntchito yake ndi malo ake, kuti azisangalala ndiponso azikhala motetezeka.
6 Mogwirizana ndi dzina lakuti Beteli, dipatimenti iliyonse ndi ya dongosolo kwambiri. Zimenezi zimalimbikitsa mtendere, zimathandiza kuti tilalikire uthenga wabwino mogwira mtima, ndiponso zimapereka chifukwa chomveka choti mipingo iziyamikirira kwambiri “Nyumba ya Mulungu” imeneyi.—1 Akor. 14:33, 40.
7 Kodi n’chifukwa chiyani nyumba zimenezi zili zofunika? Mwachitsanzo, Utumiki Wathu wa Ufumu uno, unasindikizidwira pa Beteli. Kulalikira uthenga wa Ufumu ndi kugaŵira chakudya chauzimu, zomwe Yesu Kristu anaoneratu kuti zidzachitika, zimapangitsa kuti dongosolo lokhala ndi gulu longa la Beteli likhale lofunika kwambiri. Beteli imachirikizidwa ndi antchito odzipereka ndipo olambira a Yehova onse amayamikira kwambiri nyumbayi.—Mat. 24:14, 45.
8 Kodi mungakonde kudziŵa zambiri za zimene zimachitika pa Beteli, kuyambira Lolemba mpaka Loŵeruka? Ngakhale kuti ambiri mwa antchito anthaŵi zonse oposa 140 amadzuka mofulumirirapo kuti akonzekere zochita za tsikulo, nthaŵi ya 6:30 m’maŵa, m’nyumba zogona zonse mumalira kabelu kosangalatsa kamene kamadzutsa anthu. Kuyambira Lolemba mpaka Loŵeruka, nthaŵi ya 7:00 m’maŵa, banjalo limasonkhana m’chipinda chodyera kuti likambirane lemba la tsiku, kapena kuti kulambira kwa mmaŵa. Pambuyo pake amadya chakudya cha m’maŵa. Tsiku lililonse, amayamba kugwira ntchito 8:00 m’maŵa ndipo amagwira ntchito kwa maola asanu ndi atatu, amapuma panthaŵi ya chakudya chamasana basi. (Loŵeruka, banjali limagwira ntchito mmaŵa wokha basi.) Kaya ndi ku Khichini, Dipatimenti Yotembenuza, Kochapira, m’Maofesi ena, Kokonzera Zinthu, Dipatimenti Yotumiza Mabuku, kapena ku dipatimenti ina iliyonse, kumakhala ntchito yambiri. Nthaŵi ya madzulo ndiponso kumapeto a sabata, ena a m’banja la Beteli amasonkhana ndi mipingo yozungulira Beteli pa misonkhano kapena kuloŵera pamodzi mu ulaliki. M’mipingo imeneyi abale ambiri a pa Beteli ndi akulu kapena atumiki otumikira. Mboni za m’mpingo imeneyi zimayamikiradi thandizo limeneli, onse amagwira ntchito mogwirizana monga thupi limodzi, amalemekezana ndi kumvana.—Akol. 2:19.
9 Kuyamikira Kwambiri Utumiki Wopatulika Wapabeteli: Anthu ambiri amakonda kufunsa anthu a m’mabanja a Beteli kuti “Kodi mumagwira ntchito yanji?” Ntchito n’zosiyanasiyana, koma aliyense amalemekeza ntchito iliyonse. Chifukwa? Chifukwa chakuti ntchito zonse ndi utumiki wopatulika, kaya ndi yogwiritsa ntchito makina osindikizira chakudya chauzimu, kuchapa zovala, kuphikira banjalo chakudya ndi kuyeretsa nyumba zawo zogona, kapena ntchito ya mu ofesi.
10 Mboni za Yehova zimayamikira kwambiri mzimu wodzimana umene abale ndi alongo awo a pa Beteli amasonyeza, omwe amachita ntchito yawo modzipereka ndi mosangalala. Kaya tikutumikira Yehova pa Beteli kapena kwina kulikonse, tonse tili ndi chifukwa chomveka chochitira zimene anachita Mfumu Davide—kuyamikira, kapena kukondwa, ndi “Nyumba ya Mulungu.”
11 Nthaŵi zina pamapezeka mpata woti achinyamata angakatumikire pa Beteli. Nthaŵi zambiri, utumiki umenewu umafunika anyamata amphamvu, komanso nthaŵi zina alongo amafunika. Kodi muli ndi zaka za pakati pa 19 ndi 35? Kodi ndinu wathanzi ndipo mumaganiza bwinobwino? Kodi mumaŵerenga, kulemba ndi kulankhula bwino Chingelezi? Kodi ndinu munthu wauzimu amene mumakonda kwambiri Yehova ndi gulu lake? Kodi mungagwire mokhulupirika ntchito iliyonse imene angakupatseni? Ndiye kuti mungayenerere kuyamba mwayi wapadera wotumikira pa Beteli. Mungadziŵe zambiri mwa kupezeka pa msonkhano wa anthu amene akufuna utumiki wa pabeteli pa msonkhano wachigawo wa chaka chino.
[Bokosi patsamba 6]
Mabulosha Osonyeza Nthambi ya Malaŵi atumizidwa ku mipingo yonse.
Osamalira Banja la Beteli
Mapulogalamu Auzimu
Dipatimenti ya Utumiki
Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala
Dipatimenti Yomasulira Mabuku
Dipatimenti Yokonza Maonekedwe a Mabuku
Dipatimenti Yoyang’anira Makompyuta
Dipatimenti Yokonza Zinthu
Dipatimenti Yomanga Nyumba za Ufumu
Dipatimenti Yotumiza Mabuku