Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/02 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira June 10
  • Mlungu Woyambira June 17
  • Mlungu Woyambira June 24
  • Mlungu Woyambira July 1
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 6/02 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira June 10

Nyimbo Na. 58

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Ŵerengani nkhani yonse ndi malemba amene aperekedwawo. Ndiyeno phatikizanipo ndemanga zina, mwa kufutukula mfundo zina za m’Bokosi la Mafunso la mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 1998.

Mph. 20: “Kufesa Mowoloŵa Manja Kumabweretsa Madalitso Ochuluka.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1992, masamba 15-16, ndime 14-17.

Nyimbo Na. 220 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 17

Nyimbo Na. 136

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 4, sonyezani zitsanzo ziŵiri za ulaliki za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya June 15 ndi Galamukani! ya July 8. Ngati Galamukani! ya July 8 palibe, gwiritsani ntchito Galamukani! ya June 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana naye, akuti “Sindili wokondwera ndi chipembedzo.”—Onani buku la Kukambitsirana, pamasamba 16, 17.

Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Khutirani ndi Zimene Muli Nazo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani Malemba amene pachokera malangizoŵa, ndipo ngati nthaŵi ilipo ŵerengani komanso kambiranani ambiri mwa malemba amene aperekedwawo.

Nyimbo Na. 197 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 24

Nyimbo Na. 52

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwamuna ndi mkazi amene amayendera limodzi mu utumiki asonyeze momwe tingagwiritsire ntchito mfundo za patsamba 4 kugaŵira magazini ya July 1 ndi ya July 8. Ngati Galamukani! ya July 8 palibe, gwiritsani ntchito Galamukani! ya June 8. Mkaziyo achite chitsanzo chogaŵira Nsanja ya Olonda, ndipo mwamunayo achite chitsanzo chogaŵira Galamukani!

Mph. 15: Ofalitsa pampingopo asimbe kapena achite chitsanzo cha zimene zinachitikadi (1) pamene anali kulalikira kwa anthu amitundu yosiyanasiyana kapena anthu a zinenero zina kapena (2) pamene anali kulalikira mwa njira ina osati kunyumba ndi nyumba ndi ulaliki wa mumsewu. Pokonzekera Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wa maŵa, limbikitsani onse kusankha ndi kukonzekera ulaliki woti adzagwiritse ntchito pogaŵira limodzi la mabulosha amene tigaŵire mu July ndi August.—Onani bokosi lakuti “Zofalitsa Zina,” mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002.

Mph. 20: “Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 2.” Ikambidwe ndi mkulu waluso. Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

Nyimbo Na. 95 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 1

Nyimbo Na. 83

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a June. Pemphani ofalitsa kutchula bulosha limene akonzekera kugaŵira mu July ndiponso ulaliki umene adzagwiritse ntchito.

Mph. 15: Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! Nkhani komanso kukambirana ndi omvetsera. Tchulani zinthu za m’buloshali zimene zimapangitsa kuti likhale chida champhamvu chophunzitsira za Yehova kwa ana ndiponso anthu ena amene sanaphunzire kwenikweni kapena amene sadziŵa kwambiri kuŵerenga. Kambiranani zitsanzo zosonyeza kuti limafotokozera zinthu mosavuta ndiponso mogwira mtima. (Onani phunziro 2, 8, ndiponso 12.) Sonyezani momwe tingagwiritsire ntchito zithunzi kuti timufike pamtima wophunzira wathu. Tchulani momwe tingagwiritsire ntchito bwino bulosha limeneli. Makolo ayenera kuphunzira buloshali ndi ana awo ang’onoang’ono. Limbikitsani onse kugaŵira buloshali mu utumiki pamene pali poyenera.

Mph. 15: “Kodi ‘Mukufuna’ Kuthandiza Anthu Ena?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Limbikitsani anthu onse mu mpingo kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuthandiza anthu ena.

Nyimbo Na. 156 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena