Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa September 2 kufikira December 23, 2002. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Zonama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Kusinkhasinkha za mikhalidwe yosangalatsa ya Yehova ndi njira yofunika kwambiri poyandikira kwa iye. (Sal. 143:5) [w00-CN 10/15 tsa. 4 ndime 6]
2. Kulumikizana kwa mitengo iŵiri kotchulidwa pa Ezekieli 37:15-24 kukufanana ndi zochitika za makono chifukwa chakuti mu 1919 odzozedwa okhulupirika anagwirizanitsidwa mu ulamuliro wa Kristu, “mfumu [yawo] imodzi” ndi “mbusa [wawo] mmodzi.” [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 9/15 tsa. 25 ndime 13.]
3. ‘Gogi wa Magogi’ ndi mawu ophiphiritsira onena za maboma a dzikoli. (Ezek. 38:2) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 8/15 tsa. 27 ndime 2.]
4. Ngati zimene tamva zachokera kwa munthu wooneka ngati waudindo wake kapena munthu amene akunena kuti ndi wodziŵa zambiri, palibe chifukwa chokanira zinthu zimenezo, n’kunena kuti n’zabodza. [w00-CN 12/1 tsa. 29 ndime 7-8]
5. Yakobo 4:17 amagwirizana ndi Ezekieli 33:7-9, kusonyeza kuti tidzaimbidwa mlandu chifukwa cha zimene timadziŵa pa zimene Mulungu amafuna kwa ife. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 4/1 tsa. 7 ndime 1.]
6. Danieli anasonyeza kuti anali mneneri woona mwa kufotokoza tanthauzo la fano la m’loto la Mfumu Nebukadinezara atam’longosolera lotolo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani Danieli 2:7-9, 26.]
7. Obadiya 16 ananeneratu za kufafanizidwa kwa Aedomu chifukwa chodana ndi Yuda. (Obad. 12) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 4/15 tsa. 30 bokosi.]
8. “Mlomo woyera [“chinenero choyera,” NW]” wotchulidwa pa Zefaniya 3:9 ukuphatikizapo kumvetsetsa choonadi chokhudza Mulungu ndi zofuna zake. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w01-CN 2/15 tsa. 27 ndime 18.]
9. Yesu anavutika kwambiri m’maganizo m’munda wa Getsemane chifukwa chakuti ankalingalira mmene imfa yake yochititsa manyazi monga chigaŵenga chachabechabe ikhudzire Yehova ndi dzina Lake loyera. (Mat. 26:38; Luka 22:44) [w00-CN 11/15 tsa. 23 ndime 1]
10. ‘Mfilisti’ amene wakhala “ngati mkulu wa fuko m’Yuda,” wofotokozedwa pa Zekariya 9:6, 7, akuimira mwaulosi a nkhosa zina lerolino amene aphunzitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndipo apatsidwa maudindo amene akufunika. (Mat. 24:45) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 7/1 tsa. 23 ndime 14.]
Yankhani mafunso otsatiraŵa:
11. Kodi ntchito yathu yolalikira tingaiyerekezere motani ndi ntchito yaulonda ya Ezekieli? (Ezek. 33:1-11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 1/1 tsa. 28 ndime 13.]
12. Kodi n’chiyani chomwe chinaoneka masiku ano chimene chikufanana ndi masomphenya a Ezekieli okhudza mafupa ouma? (Ezek. 37:5-10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 9/15 tsa. 24 ndime 12.]
13. Pa Hagai 2:9, kodi ndi kachisi uti amene anali ‘nyumba yotsiriza,’ nanga ‘yoyambayo,’ inali kachisi uti, ndipo n’chifukwa chiyani ulemerero wa ‘nyumba yotsiriza’ unali waukulu kuposa ulemerero wa ‘yoyambayo’? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 6/1 tsa. 30.]
14. Kodi mzinda wa m’masomphenya a Ezekieli ukuimira chiyani? (Ezek. 48:15-17) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 3/1 tsa. 18 ndime 22.]
15. Malinga ndi Yesaya 2:2-4, kodi tingafotokoze motani kuti zimene zikuchitika ku Israel masiku ano sizikukwaniritsa ulosi wa Baibulo? [rs-CN tsa. 45 ndime 2]
16. Kodi tingaphunzirenji pa zimene Danieli anachita pa lamulo la mfumu loti kwa masiku 30 munthu aliyense asapemphe kanthu kwa mulungu kapena munthu wina aliyense koma kwa mfumuyo? (Dan. 6:7-10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani dp-CN tsa. 125-6 ndime 25-8.]
17. Kodi otsalira akhala ngati mkango mwa amitundu chifukwa cholengeza uthenga wotani wa Yehova? (Mika 5:8) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w81 7/15 tsa. 23 ndime 10.]
18. Kodi mawu akuti “munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake,” a pa Habakuku 3:14 amatanthauzanji? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w00-CN 2/1 tsa. 22 ndime 15; w81 8/1 tsa. 29 ndime 6-7.]
19. Kodi kugwiritsa ntchito mawu akuti “kapena” pa Zefaniya 2:3 kukusonyeza chiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w01-CN 2/15 tsa. 19 ndime 8.]
20. Malinga ndi Zekariya 8:6, kuyambira 1919, kodi Yehova wachita motani zimene n’kutheka kuti anthu ankaona kuti n’zovuta kwambiri? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 1/1 tsa. 16 ndime 18-19.]
Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Timalankhula ndi Yehova kudzera mu ․․․․․․․․ , lomwe ndi kulankhula mwachindunji ndi Mulungu mom’lambira; ndiyeno, njira yaikulu yomwe iye amalankhulira nafe ndiyo kudzera ․․․․․․․․ . (Sal. 65:2; 2 Tim. 3:16) [w00-CN 10/15 tsa. 5 ndime 1-2]
22. Tingadziŵe kuti Yesu Kristu ndi Mikaeli mwa kufananitsa Yuda 9 ndi 1 Atesalonika 4:16, pamene lamulo la Yesu Kristu loti chiukiriro chiyambe lafotokozedwa kuti ndi “ ․․․․․․․․ ;” komanso, dzina lakuti Mikaeli limatanthauza “ ․․․․․․․․ ,” lomwe mwachiwonekere limasonyeza kuti Yesu ndi amene akutsogolera kuchirikiza ufumu wa Yehova ndi kuwononga adani a Mulungu. [rs-CN tsa. 432 ndime 1-2]
23. “Kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kum’manga Yerusalemu” kunachitika mu ․․․․․․․․ , poyambira masabata 69 a zaka, omwe anatha ndi kuonekera kwa Mesiya mu ․․․․․․․․ . (Dan. 9:25) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani dp-CN tsa. 190 ndime 20–tsa. 191 ndime 22.]
24. Pomasulira mawu olembedwa pakhoma, Danieli anasonyeza kwa ․․․․․․․․ chitsanzo chabwino kwambiri cha chikhulupiriro ndi kulimba mtima. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 12/1 tsa. 20 ndime 19.]
25. “Chigwa cha Yosafati” chikuimira ․․․․․․․․ ‘m’tsiku la Yehova.’ (Yow. 3:2, 14) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 3/15.]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. “Chipangano” chikuimira (pangano la Chilamulo; pangano latsopano; pangano la Abrahamu). (Dan. 9:27) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani kc tsa. 65 ndime 23.]
27. Oitana pa dzina la Yehova “adzapulumutsidwa” (akabatizidwa; akamalalikira za dzina la Yehova nthaŵi zonse; Mulungu akamadzapereka chiweruzo chake pa amitundu). (Yow. 2:32) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 3/15.]
28. Yehova “analeka choipa” m’lingaliro lakuti ( anasintha malingaliro ake olanga Aasuri omwe analapa; anamva chisoni kuti iwo anayenera kulandira chilango chowawa kwambiri; anadandaula chifukwa chakuti khalidwe la zolengedwa zake lafika poipa kwambiri). (Yona 3:10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 4/15.]
29. Mtundu wa dzombe wophiphiritsira wotchulidwa pa Yoweli 1:4-6 ukuimira (mtundu wa Israyeli; Akristu odzozedwa; gulu lankhondo la Roma). (Mac. 2:1, 14-17) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 5/1 tsa. 10 ndime 9.]
30. “Ufumu wa Mwana wa chikondi chake” wotchulidwa pa Akolose 1:13 ndi (Ufumu Waumesiya; ulamuliro wa Kristu pa mpingo wachikristu kuyambira pa Pentekoste 33 C.E. mpaka m’tsogolo; Ulamuliro wa Zaka 1000 wa Kristu). [rs-CN tsa. 381 ndime 2]
Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zomwe zili m’munsizi:
Hos. 6:6; Yow. 2:32; Dan. 3:16-18; 7:13, 14; Aroma 12:2
31. Sitiyenera kulola miyezo yachikhalidwe kapena yakudziko kuwumba malingaliro athu. [w00-CN 11/1 tsa. 21 ndime 5]
32. Chimene chikondweretsa Mulungu, si kuchuluka kwa nsembe zongoperekedwa mwamwambo, koma ndi ntchito za kukoma mtima kochitidwa chifukwa chomudziŵa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani si tsa. 145 ndime 16.]
33. Kudziŵa, kulemekeza, ndi kudalira mwini dzina laumulungu n’kofunika pa chipulumutso. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 3/15 tsa. 30 bokosi.]
34. Mogwirizana ndi chitsanzo chimenechi cha m’Malemba, atumiki a Yehova lerolino sagwadira zizindikiro za dziko. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; yerekezani ndi w88-CN 12/1 tsa. 19 ndime 17.]
35. M’paradaiso, Mulungu adzaika anthu pamalo pamene iye wafuna. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 9/15 tsa. 27 ndime 22.]