Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati ameneŵa palibe, mungagaŵire aŵa: Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January: Mankind’s Search for God kapena Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Tidzagaŵira buku latsopano lakuti Yandikirani kwa Yehova. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Posachedwapa mpingo uliwonse ulandira mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso cha 2003 m’chinenero cha mpingowo. Ngati m’gawo lanu amalankhula zinenero zina ndipo mukufuna mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso a m’zinenero zimenezo, itanitsani msanga pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso alipo a m’Chicheŵa, Chingelezi ndi Chitumbuka. Chonde mungoitanitsa a zinenero zokhazo zimene zikufunika m’gawo lanu.
◼ Dziŵani kuti Chikumbutso cha 2004 chidzachitika Lamlungu, pa April 4, dzuŵa litaloŵa. Taneneratu zimenezi kuti abale apezeretu maholo ena ngati mipingo ingapo imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo ikufunikadi kupeza malo ena. Akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti mwambowu usadzadodometsedwe ndi zochitika zina pamalowo kuti Chikumbutsocho chidzachitike mwamtendere ndi mwadongosolo. Popeza mwambowu ndi wapadera, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu yemwe alidi woyenerera, osati kungosinthana kapena kuti chaka chilichonse azingokamba mbale mmodzimodzi yemweyo. Ngati pali wodzozedwa amene ndi mkulu komanso angathe kukamba nkhaniyo musankheni ameneyo.
◼ Utumiki Wathu wa Ufumu wa October chaka chino unanena kuti “ofalitsa ndi ana awo okha basi” ndi amene angapeze mabaibulo a Chicheŵa ndi a Chitumbuka kudzera ku mpingo. Komabe, anthu achidwi amene akuphunzira Baibulo ndipo akulimbikira kuti akhale ofalitsa osabatizidwa angalandirenso Baibulo ku mpingo, kuti apitirize kupita patsogolo mwauzimu.
◼ Ofalitsa obatizidwa onse amene adzapezeka pa Msonkhano wa Utumiki wamlungu woyambira January 6 adzalandira makadi a Chidziŵitso kwa Dokotala/Chom’masula ku Mlandu ndiponso Makadi a Ana awo.
◼ Pali kusintha mmene Sukulu ya Utumiki wa Mulungu izichitikira mlungu umene woyang’anira dera akuchezera mpingowo. Kuyambira mu January 2003, nyimbo ndi pemphero loyamba likatha, sukulu izichitika kwa mphindi pafupifupi 25. Pazikhala nkhani yonena za luso la kulankhula kwa mphindi 5, nkhani yolangiza kwa mphindi 10, ndiponso mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo kwa mphindi 10. Sipazikhala nkhani Na. 2, 3, ndi 4. Ikatha sukulu pazibwera Msonkhano wa Utumiki wa mphindi 30. Ikatha nyimbo, woyang’anira dera azikamba nkhani yake kwa mphindi 30, kenako pazibwera nyimbo ndiponso pemphero lomaliza.