Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/02 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira December 9
  • Mlungu Woyambira December 16
  • Mlungu Woyambira December 23
  • Mlungu Woyambira December 30
  • Mlungu Woyambira January 6
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 12/02 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira December 9

Nyimbo Na. 193

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph. 15: “Lalikirani Uthenga wa Ufumu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3, phatikizanipo zimene tingachite kuti tiziŵerenga m’Baibulo mwenimwenimo pokambirana uthenga wabwino ndi anthu ena.—km-CN 12/01 tsa. 1, ndime 3.

Mph. 20: Balani Zipatso mu Ntchito Iliyonse Yabwino. Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi mkulu. Pendani mbiri ya mpingowo ndiponso mmene ukuyendera, komanso zimene zinachititsa kuti mpingowo ukhazikitsidwe. Konzeranitu zoti ena amene analipo panthaŵiyo asimbe zokumana nazo zabwino. Pendani zimene zikusonyeza kuti pali chiyembekezo chakuti anthu awonjezekanso, ndipo limbikitsani onse kuthandiza mwachangu ntchito za mpingo.

Nyimbo Na. 119 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 16

Nyimbo Na. 29

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Aphunzitsi Ndiwo Adzazindikira. (Dan. 12:3, 10) Chitsanzo. Munthu wachidwi afunse kuti: “Kodi ndingatsimikize bwanji kuti mumadziŵa zolondola pa zimene Baibulo limaphunzitsa?” Wofalitsa afotokoze mmene munthu angafufuzire za m’Baibulo mwa kusankha nkhani imodzi ndi kuifufuza. (w96-CN 5/15 tsa. 19-20) Mwa kugwiritsa ntchito chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri za m’buku la Kukambitsirana tsamba 131 mpaka 134, afotokoze mmene mwa kupenda Malemba mosamalitsa, tadziŵira cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi. Wofalitsa afotokoze mmene angagwiritsirenso ntchito njira yomweyi kuti amvetse bwino ziphunzitso zina za m’Baibulo ndipo am’pemphe munthuyo kuphunzira naye Baibulo.

Mph. 20: “Ganizirani Okalamba Omwe Ali Okhulupirika.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1994, patsamba 29. Tchulani za dongosolo la anthu okalamba ndi odwaladwala loti azipereka lipoti la mphindi 15 zilizonse za mu utumiki wa kumunda. Konzani zoti anthu angapo asimbe zimene zinachitika zosonyeza kuti kucheza ndi anthu ameneŵa kumapindulitsa onse.

Nyimbo Na. 154 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 23

Nyimbo Na. 148

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsira ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya December 15 ndi Galamukani! ya December 8. 

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Kodi Mumathandiza Kuti Lipoti Likhale Lolondola?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 2, phatikizanipo ndemanga za m’buku la Utumiki Wathu, tsamba 106 mpaka 108.

Nyimbo Na. 165 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 30

Nyimbo Na. 152

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a December. Ngati chaka chikubwerachi mpingo wanu usinthe nthaŵi ya misonkhano, limbikitsani onse mokoma mtima kuti azipezeka mokhazikika panthaŵi zatsopanozi. Tchulani mabuku ofunika kugaŵira mu January, kambani kwambiri za mabuku amene muli nawo pampingopo.

Mph. 15: Onani Ngati Mungakwanitse Upainiya. Nkhani yolimbikitsa anthu ndiponso kufunsa. M’Malaŵi muno, tsopano tili ndi apainiya okhazikika oposa 3,000 osiyana ntchito zawo ndi moyo wawo. N’chiyani chawalimbikitsa kuchita upainiya? Kukonda Yehova ndi mnansi (Mat. 22:37-39); chifundo kwa anthu ndiponso kufuna kuthandiza ambiri kuti apulumuke (1 Tim. 2:4); kudzimana chifukwa chofuna kuchita zinthu za Ufumu. (1 Akor. 9:23) Tiyenera kukhala ndi mtima wofunitsitsa. Kodi mukukulitsa mtima umenewu? Zimene mungachite ngati mukufuna kuchita upainiya: (1) Lankhulani ndi Yehova za nkhaniyo m’pemphero (Mat. 7:7, 8; Afil. 4:6); (2) kambiranani ndi apainiya ndiponso akulu (Miy. 15:22); (3) lembani ndandanda yongoyerekezera, ndipo onani momwe ikukhudzira zinthu zina zachikristu (Luka 14:28); (4) khalani ndi tsiku limene mukufuna kuyamba upainiya, musachite kudikira kuti zinthu zikukhalireni bwino. (Mlal. 11:4) Funsani mpainiya mmodzi kapena aŵiri momwe amagonjetsera zimene zingawalepheretse kuchita upainiya. Musamakayike.

Mph. 20: “Kukhulupirika Posala Magazi.” Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi mkulu woyenera. Limbikitsani onse kusinkhasinkha mfundo za makhalidwe abwino ndiponso malamulo a Baibulo okhudza chithandizo chopatsa munthu magazi kapena zigawo zina za m’magazi kuti azisankha zochita atadziŵa zonse. Mitu ya mabanja iyenera kuyesetsa kwambiri kuthandiza ana awo kumvetsa zimene Baibulo limanena pankhani ya magazi.

Nyimbo Na. 147 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 6

Nyimbo Na. 67

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsira ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya December 8.

Mph. 15: Zimene Zingatithandize Kumvera Lamulo la Mulungu Pankhani ya Magazi. Ikambidwe ndi mkulu woyenera, agwiritse ntchito autilaini yochokera ku ofesi ya nthambi. Mlembi akhale ndi zinthu zotsatirazi zokwanira kuti agaŵire anthu: Khadi la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chom’masula ku Mlandu ndiponso Khadi la Mwana. Ofalitsa obatizidwa alandira zinthu zimenezi lero tikamaliza msonkhano koma ASAZILEMBERE pano. Makadiŵa adzasainidwa, kuikira umboni ndi kulembapo deti pamapeto pa Phunziro la Buku la Mpingo lotsatira ndipo amene afuna thandizo, woyang’anira phunziro la buku adzawathandiza. Osaina monga mboni ayenera kumuonadi mwinikhadilo akusaina. Ofalitsa osabatizidwa angalembe makadi awoawo oti azigwiritsira ntchito iwo ndi ana awo, akopere mawu a pakhadili ndi kuwasintha kuti agwirizane ndi moyo wawo komanso zikhulupiriro zawo.

Mph. 20: Bokosi la Mafunso. Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi mkulu woyenera.

Nyimbo Na. 79 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena