Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu January: Buku la Mankind’s Search for God, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, ndi Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. February: Buku latsopano la Yandikirani kwa Yehova. March: Buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Oyang’anira madera adzayamba kukamba nkhani ya onse yatsopano yakuti “Kulanditsidwa ku Dziko la Mdima.” Adzayamba tsiku lililonse kuyambira February mpaka March 2.
◼ Mipingo ipange makonzedwe abwino odzachita Chikumbutso chaka chino Lachitatu, pa April 16, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, musayendetse zizindikiro za Chikumbutso kufikira dzuŵa litaloŵa. Funsani odziŵa za nyengo kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yoloŵera dzuŵa m’dera lanu. Ngati mipingo ingapo imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mpingo umodzi kapena yoposerapo ingapeze malo ena odzagwiritsira ntchito tsikuli madzulo. Tikupereka malingaliro akuti, ngati kungatheke mapulogalamu akatha pazipita mphindi zosachepera 40 ena asanayambe, kuti onse apindule mokwanira. M’pofunika kuganizira za kuchuluka kwa magalimoto ndiponso koimikako magalimotowa, komanso za kukatenga ndi kukasiya anthu. Bungwe la akulu liyenera kupanga makonzedwe okomera mpingowo.
◼ Mipingo iyenera kuitanitsa timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso cha chaka cha mawa ikamatumiza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) yotsatira. Timapepalati tili m’Chichewa, m’Chingelezi, ndi m’Chitumbuka. M’chinenero chilichonse poitanitsa, kuchuluka kwake kukhale kwa m’ma 100, monga ma 100, 200, 300, choncho basi. Chonde khalani osamala poitanitsa zimenezi chifukwa si zogaŵa mwachisawawa ayi koma ndi za anthu achidwi okha.