Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira January 13
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 20: Limbikitsani Anthu Kukhala ndi Chidwi Chofuna Makambirano Owonjezereka. Nkhani ndi zitsanzo. Tifunika kuchita zinthu mwaluso ndi mokoma mtima tikakhala mu utumiki wathu. (1 Akor. 9:19-23) Ngati tisiya chithunzi chabwino kwa mwininyumba, zingapangitse kuti wofalitsa wina amene adzabwere adzathe kulalikira bwino. Mwa kum’siyira funso mwininyumbayo pamene tikuchoka, tingam’limbikitse kukhala ndi chidwi chofuna kuti tidzam’yenderenso. Ngati titam’funsa funso lokhudzana ndi nkhani imene imam’sangalatsa, mwina mpaka angafune kuti tipitirize kukambirana kwathu. Zingakhale bwino ngati mutagwiritsira ntchito nkhani zimene zikupezeka mu buku la Kukambitsirana. Funsani mafunso onga aŵa, “Kodi munthu analengedwa ndi Mulungu kuti afe?” (rs-CN tsa. 151), “Kodi planetili dziko lapansi lidzawonongedwa m’nkhondo yanyukliya?” (rs-CN tsa. 131), “Kodi nchiyani chimene chili chifuno cha moyo waumunthu?” (rs-CN tsa. 290), “Kodi munthu angadziŵe motani chimene chili chipembedzo choona?” (rs-CN tsa. 89), ndiponso “Kodi n’chifukwa ninji pali kuipa kochuluka?” (rs-CN tsa. 183) kapena mungasankhe mafunso ena alionse amene angakhale oyenerera kwanuko m’buku la Kukambitsirana. Khalani ndi chitsanzo choonetsa mmene mungamalizire makambirano anu ngati mwininyumba alibe chidwi. Pamene wofalitsayo akuchoka, afunse mwininyumbayo funso ndi kumuuza kuti ali wokonzeka kudzaliyankha akadzabweranso. Khalaninso ndi chitsanzo choonetsa mmene wofalitsa angagwiritsire ntchito buku la Kukambitsirana poyankha ngati mwininyumba angafune yankho. Mbale amene akukamba nkhaniyi pomaliza afotokoze za kufunika kolimbikitsa chidwi mwa kufunsa mafunso omupangitsa mwininyumba kuganiza.
Mph. 17: “Kukwaniritsa Kudzipatulira Kwathu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mutapenda ndime 3, funsani mwachidule wachinyamata wobatizidwa wa zaka za m’ma 20 kapena wa zaka zoyambira 13 mpaka 19. Kodi wakumana ndi mayeso otani kuchokera pa ubatizo wake? Chinam’thandiza n’chiyani kupirira? Kodi wapeza phindu lanji mwa kupatulira moyo wake kwa Yehova?
Nyimbo Na. 22 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 20
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Kodi Mukusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku? Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Limbikitsani onse kugwiritsira ntchito bwino kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2003. Kambiranani ndemanga zimene zili pa mawu oyamba, pamasamba 3 mpaka 4. Perekanipo maganizo a mmene mabanja angamakambirane pamodzi lemba la tsiku. Pofuna kusonyeza ubwino wokambirana lemba tsiku lililonse, kambiranani zitsanzo ziŵiri kapena zitatu za malemba ndi ndemanga zake zimene zidzapendedwe mwezi ukubwerawu. Mwamuna ndi mkazi wake achite chitsanzo chachidule. Akambirane lemba lalero ndi ndemanga zake ali limodzi.
Mph. 22: “Phunzitsani Ena Chinenero Choyera.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mutapenda ndime 6, wofalitsa wodziŵa bwino kulalikira achite chitsanzo kusonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo lochita muli choimirira panyumba ya munthu paulendo wobwereza. Agwiritsire ntchito ulaliki wa mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002, patsamba 4. Akambiranenso ndime imodzi m’bulosha la Mulungu Amafunanji. Wofalitsayo pomaliza kukambiranako, afunse funso la ndime yotsatira ndi kukonza zoti adzaliyankhe ulendo wina. Limbikitsani onse kuona ngati ena mwa anthu amene amawayendera angafune kuphunzira Baibulo mwa njira imeneyi.
yimbo 68 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 27
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda. Mwa kugwiritsira ntchito mfundo za patsamba 4, khalani ndi zitsanzo ziŵiri za mmene tingafalitsire Nsanja ya Olonda ya December 15 ndi Galamukani! ya January 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsira ntchito magazini imodzi pokambirana.
Mph. 20: Kuthandiza Amene Timaphunzira Nawo Baibulo. Nkhani yokambirana ndi omvetsera. Igogomezere kufunika kothandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo m’njira zina kuwonjezera pa kuwaphunzitsa Baibulo. (1 Ates. 2:8) Patulani nthaŵi kuti muwalimbikitse kukhala ndi mtima wofuna kupezeka ndi kuyankha pamisonkhano. Athandizeni kuzindikira kufunika kwa gulu la Yehova ndi ubale wathu wa padziko lonse mwa kuwafotokozera za misonkhano yadera, yapadera, ndi yachigawo. Pang’onopang’ono, asonyezeni mmene angauzire ena zimene akuphunzira. Ophunzira Baibulo amene akwaniritsa ziyeneretso zimene zalembedwa pa masamba 98 ndi 99 a buku la Utumiki Wathu ndipo akufuna kumapita nawo mu ulaliki, afunika kuwathandiza kuti akhale ofalitsa osabatizidwa. Ndi kofunika kupeza nthaŵi tikamachititsa phunziro komanso tikamaliza kuwathandiza ophunzirawo kukhala ndi chikhumbo chofuna kudzipatulira ndi kubatizidwa. Tikhoza kuwaonetsa ophunzirawo zithunzi kapena nkhani za m’nyuzipepala zosonyeza ubatizo pamisonkhano yathu. Chitsanzo: Wofalitsa akusonyeza wophunzira Baibulo mmene angalalikire mwamwayi. Iye asankhe mfundo ina m’buku la Chidziŵitso imene angaigwiritsire ntchito m’munda ndipo anene kuti: “Mungachite bwino kuuzako abale anu kapena anansi anu mfundo imeneyi. Mwina mungawauze kuti mwaphunzira kanthu kena kamene simunali kukadziwa kuchokera m’Baibulo.” Limbikitsani ofalitsa kuthandiza ophunzira Baibulo ndi kuwasamalirabe pambuyo poti abatizidwa.
Mph. 15: Thandizani Ena Kuyandikira kwa Yehova. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. M’mwezi wa February tidzagaŵira buku latsopano. Kambiranani mawu oyamba amene alembera oŵerenga patsamba 3, ndipo fotokozani mbali zina za bukuli. Chilichonse mwa zigawo zake zinayi chikufotokoza limodzi la makhalidwe aakulu a Yehova. Chigawo chilichonse chilinso ndi mutu wosonyeza mmene Yesu anaonetsera khalidwe limenelo ndi winanso wofotokoza mmene ifeyo tingachitire zimenezo. M’bukuli muli zithunzi 17 zokwana tsamba lathunthu zokhudza nkhani za m’Baibulo. Mulinso “Mafunso Owasinkhasinkha” otithandiza kuganizira za mbali zina zofunika za nkhaniyo. Kambiranani bokosi lakuti “Mmene Mungafalitsire Buku la Yandikirani kwa Yehova,” ndipo wofalitsa wodziŵa bwino kulalikira achite chitsanzo pogwiritsira ntchito ulaliki umodzi.
Nyimbo Na. 124 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 3
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Pendani Bokosi la Mafunso. Woyang’anira wotsogolera akambe nkhani imeneyi mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani chifukwa chake kuli kofunikira kuŵerenga zilengezo zochokera ku ofesi ya nthambi momveka bwino ndiponso mwachidule. Mwa kugwiritsira ntchito mfundo za patsamba 4, khalani ndi zitsanzo ziŵiri za mmene tingafalitsire Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya January 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, wofalitsa pomaliza apatse mwininyumba—wina amene walandira magazini, ndi wina amene sanalandire—thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Fotokozani mwachidule mmene tingachitire ulendo wobwereza kwa amene tinawagaŵira magazini ndi kuwasiyiranso thirakiti.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2001, tsa. 4, ndime 10.
Mph. 12: Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo. Funsani mkulu amene watumikira Yehova modzichepetsa komanso mokhulupirika kwa zaka zambiri. (Aheb. 13:7) Kodi anaphunzira bwanji choonadi? Kodi anagonjetsa zopinga ziti kuti apitirize? Ndi zinthu ziti zimene Yehova watipatsa kapenanso chilimbikitso zimene zinam’thandiza kupita patsogolo? Kodi anachita chiyani pokalamira udindo mumpingo? (1 Tim. 3:1) Kodi cham’thandiza n’chiyani kusamalira maudindo ake mumpingo kwinaku akusamaliranso udindo wake kuntchito ndi m’banja? (1 Tim. 5:8) Nanga akuuona bwanji mwayi wake wothandiza ena mumpingo?
Mph. 18: “Ntchito Imene Imafunika Kudzichepetsa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3, pemphani omvetsera anenepo maganizo awo a mmene tingachitire ngati wina m’gawo atinyodola kapena ali wachipongwe, wamakani, kapena waukali. Pokambirana ndime 4, phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1990, tsamba 20, ndime 17.
Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.