Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/03 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira February 10
  • Mlungu Woyambira February 17
  • Mlungu Woyambira February 24
  • Mlungu Woyambira March 3
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 2/03 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira February 10

Nyimbo Na. 4

Mph. 10:  Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Mwachidule kambiranani nkhani yakuti “Makonzedwe Atsopano Okhudza Malaibulale a m’Nyumba za Ufumu.” Tchulani amene adzakhala woyang’anira laibulale ya m’Nyumba ya Ufumu.

Mph. 35: “Lalikirani ndi Kuchitira Umboni Mokwanira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Limbikitsani onse amene angathe kuti achite upainiya wothandiza mwezi wa March ndi April. Pemphani amene anachita upainiya panyengo ya Chikumbutso ulendo watha kuti alankhulepo. Kodi anachita zotani kuti apeze mpata wochitira upainiya? Kodi n’chiyani chimene anayesetsa kuchita ndi kusintha kuti athe kutero? Kodi n’chiyani chinawasangalatsa ndipo anapeza madalitso otani? Pendani ndandanda ya chitsanzo m’bokosi limene lili patsamba 4. Lengezani kuti mafomu ofunsira upainiya wothandiza alipo ndipo angawatenge msonkhanowu ukatha.

Nyimbo Na. 30 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 17

Nyimbo Na. 48

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kambiranani za buku logaŵira mwezi wa March. Tchulani mfundo imodzi kapena ziŵiri za mmene tingagaŵire buku la Chidziŵitso. Gwiritsani ntchito mfundo za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002. Tsindikani kuti cholinga chathu ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba.

Mph. 15: “Kodi Mungalole Kuti Nyumba Yanu Igwiritsidwe Ntchito?” Ikambidwe ndi woyang’anira phunziro la buku. Phatikizanipo ndemanga za m’Mabokosi a Mafunso a mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2001 ndi wa February 1990. Tchulani kuti mumpingomo muli magulu angati a phunziro la buku ndi avareji ya opezekapo. Wofalitsa mmodzi kapena aŵiri asimbe mmene apindulira iwowo ndi mabanja awo chifukwa chakuti phunziro la buku limachitikira m’nyumba yawo. Aliyense amene akufuna kuti nyumba yake izigwiritsidwa ntchito auze woyang’anira wotsogolera.

Mph. 20: “Kodi Choyamba N’chiyani M’moyo Wanu?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzani pasadakhale zoti wofalitsa mmodzi kapena aŵiri adzafotokoze kuti atha bwanji kusintha zinthu pamoyo wawo kuti achite zambiri mu utumiki.

Nyimbo Na. 57 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 24

Nyimbo Na. 74

Mph. 12 : Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa February. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri za mmene tingafalitsire Nsanja ya Olonda ya February 15 ndi Galamukani! ya February 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana.

Mph. 15: “Thandizo la Panthaŵi Yake.” Ikambidwe ndi mkulu. Tsindikani kuti ntchito yapadera imene ikuchitika yothandiza anthu amene anasiya kuloŵa m’munda ikusonyeza kuti Yehova amakonda anthu ake ndipo amawasamala.

Mph. 18: “Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera” Nkhani. Lengezani tsiku la msonkhano wadera ukubwerawu. Limbikitsani onse kudzapezekapo ndiponso kudzamvetsera mwatcheru pulogalamuyi. Limbikitsani ofalitsa osabatizidwa kuganizira za ubatizo. Chikhale cholinga chanu kuitanira ophunzira Baibulo ku msonkhanowu.

Nyimbo Na. 56 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 3

Nyimbo Na. 14

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri za mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya February 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Khalani Anzeru Pamene Mapeto Akuyandikira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3 mpaka 4, pemphani ofalitsa kuti atchule zolinga zauzimu zimene akuyesetsa kuzikwaniritsa panopa.

Nyimbo Na. 127 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena