Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira May 12
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 25: Makolo Thandizani Ana Anu Kupita Patsogolo. Nkhani yofotokoza mfundo zazikulu za m’buku la Sukulu ya Utumiki, masamba 9-12 ndi 21-38. Limbikitsani makolo kuti azigwiritsira ntchito zina mwa mfundo zimenezi pa phunziro lawo labanja, n’cholinga chothandiza ana awo kuti apite patsogolo mu utumiki. Sonyezani mfundo zimene angazigwiritsire ntchito pothandiza ana aang’ono kukhala ndi luso lofunika mu utumiki.
Mph. 15: “Anatiikiza Uthenga Wabwino.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzeranitu zoti wofalitsa mmodzi kapena aŵiri adzafotokoze mwachidule zimene anachita kuti asinthe zina ndi zina m’moyo wawo n’cholinga chowonjezera zimene amachita mu ntchito yolalikira.
Nyimbo Na. 46 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 19
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kambiranani “Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse M’mayiko Ena a ku Ulaya.” Tchulani zoti ndalama zomangira Nyumba za Ufumu m’mayiko ena osauka komanso kwathu kuno zimachokera ku zopereka za ku Thumba la Nyumba za Ufumu.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 15: “Lemekezani Yehova mwa Kulalikira Mwamwayi.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Pokambirana ndime 3, funsani omvetsera zimene anganene kuti ayambe kukambirana za m’Baibulo ndi anthu m’malo aŵa: (1) muli pamzere kuchipatala, (2) m’basi kapena m’minibasi, (3) kwa munthu woyandikana naye nyumba amene akugwira ntchito m’munda wake wa pakhomo, (4) kwa munthu wogwira naye ntchito muli kuntchitoko, (5) ndi kwa munthu amene muli naye m’kalasi imodzi ku sukulu. Konzeranitu zoti wofalitsa wina adzafotokoze zimene zinam’chitikiradi zosonyeza zimene anachita kuti athe kulalikira mwamwayi.
Nyimbo Na. 135 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 26
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kuti apereke malipoti a utumiki a May. Mwakugwiritsira ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya May 15 ndi Galamukani! ya May 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, afotokoze za magazini imodzi, ngakhale kuti agaŵira magazini onse aŵiri. Tchulani za chopereka kwa mwininyumba.
Mph 15: “Kaonekedwe Kabwino Koyenera Akristu.” Nkhani yoti ikambidwe ndi Woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Mph. 20: “Mawu a Mulungu Ndi Choonadi.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsirani ntchito mafunso amene alembedwawo. Funsani omvetsera kuti anene mmene anathandizidwira kuti aphunzire choonadi pamene ofalitsa anayankha mafunso awo pogwiritsira ntchito Baibulo. Pokambirana ndime 5, wofalitsa wodziŵa bwino kulalikira achite chitsanzo chosonyeza mmene angagwiritsire ntchito Baibulo pa ulendo woyamba, ndipo agwiritsire ntchito mfundo zina zimene zili mu nkhani yakuti “Lunjikani Nawo Bwino Mawu a Mulungu.”—km-CN 12/01 tsa. 1 ndime 3-4.
Nyimbo Na. 188 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 2
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Mwakugwiritsira ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya May 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, afotokoze za magazini imodzi, ngakhale kuti agaŵira magazini onse aŵiri. Pamapeto pa chitsanzo chimodzi, apereke thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? kwa mwininyumba amene sanalandire magazini. Pendani mfundo imodzi kapena ziŵiri zimene zili mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002 zosonyeza mmene tingagaŵire bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso.
Mph. 18: Mulungu Amafuna Ukwati Wolemekezeka. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. M’mayiko ambiri, n’zofala mwamuna ndi mkazi kukhala nyumba imodzi popanda kulembetsa ukwati ku boma. Ena amanena kuti kuchita zimenezi kumathandiza. Fotokozani zimene Baibulo limanena, ndipo tsindikani kuti Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati. (rs-CN tsa. 383-384) Kukhalira limodzi popanda ukwati ndi dama. (fy-CN tsa. 17) Mosiyana ndi zimene ena amakhulupirira, kafukufuku wasonyeza kuti kukhalira limodzi musanakwatirane nthaŵi zambiri kumapangitsa kuti ukwati wanu usadzakhalitse. Akristu amalemekeza Yehova mwa kumvera mfundo zake. Akamatero, amapindulanso paokha.—Yes. 48:17, 18.
Mph. 15: Kodi Mukupindula Motani? Kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi woyang’anira sukulu. Kuyambira mu January, tinayamba njira yatsopano yochitira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Fotokozani mwachidule zina mwa zinthu zatsopano m’sukuluyi. Tchulanipo zinthu zina zabwino zimene zachitika chiyambireni njira yatsopanoyi. Kodi anthu ambiri alembetsa m’sukuluyi? Kodi mpingo wonse ukusonyeza kuti uli ndi chidwi kwambiri ndi sukuluyi? Kodi anthu a m’sukuluyi akupindula bwanji ndi njira yatsopano yoperekera malangizo? Funsani omvetsera kuti afotokozepo mmene iwo paokha apindulira chiyambireni njira yatsopanoyi, komanso mmene akuganizira kuti iwathandizira m’tsogolo muno.
Nyimbo Na. 225 ndi pemphero lomaliza.