Ndandanda ya Misonkhani ya Utumiki
Mlungu Woyambira July 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Tchulani mabuku ogaŵira mwezi uno. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zachidule zimene mungagwiritse ntchito.
Mph. 15: “Kusonkhana Pamodzi Kuti Titamande Yehova.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene alembedwawo. Limbikitsani onse kuti akapezekepo pachigawo chilichonse, kuyambira Lachisanu m’maŵa mpaka Lamlungu masana. Gogomezerani kufunika kogwiritsa ntchito zimene timaphunzira m’malo mongomvetsera. Limbikitsani mpingo kuti uzikumbukira kuti mu October pa Msonkhano wina wa Utumiki tidzakhala ndi kubwereramo mu mfundo zazikulu za msonkhano wachigawo. Limbikitsani onse kulemba notsi.
Mph. 20: “Kuyamikira Chifundo cha Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime 3, tchulani mfundo zimene munthu angagwiritse ntchito kuti akhale ndi anthu owagaŵira magazini zochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1998, tsamba 8. Funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵiri odziŵa bwino kulalikira kuti afotokoze njira imene aiona kuti imathandiza poyambitsa maphunziro a Baibulo. Limbikitsani onse kuti akhale ndi cholinga choyambitsa ndi kuchititsa phunziro la Baibulo.—om-CN tsa. 91.
Nyimbo Na. 176 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Khalani Chitsanzo pa Ntchito Zabwino.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene alembedwawo. Gogomezerani kufunika kotsatira malangizo okhudza malo ogona omwe aperekedwa kuti tipindule. Fotokozani chifukwa chake khalidwe labwino ndi lofunika kwa aliyense.
Mph. 20: “Makonzedwe Athu Opepukitsidwa a Kagaŵidwe ka Mabuku.” Mkulu woyenerera akambirane nkhaniyi ndi omvetsera. Mukatha kukambirana ndime 4, wofalitsa wodziŵa bwino kulalikira amene wakonzekera bwino asonyeze mwachidule mmene mungagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhaniyi mu utumiki wakumunda. Ofalitsa akambirane ndi mwininyumba pogwiritsa ntchito magazini yatsopano imodzi imene mugaŵire mu utumiki wakumunda pamapeto pa mlungu uno. Akambirane nkhani imodzi imene ili m’magaziniwo. Ngati mwininyumba afunsa kuti: “Mukugulitsa ndalama zingati?” wofalitsayo angayankhe kuti: “Ngati mukaiŵerengadi, palibe mtengo uliwonse. Mukhoza kuona zimene analemba ofalitsa magaziniyi pa tsamba ili zosonyeza kuti magazini ino ndi mbali imodzi ya ntchito yophunzitsa Baibulo padziko lonse lapansi ndipo imayendetsedwa ndi zopereka zaufulu.” [Sonyezani mawu amene ali pa tsamba 5 la Galamukani! ndi pansi pa tsamba 2 kumanja mu Nsanja ya Olonda.] Mwininyumba apereke chopereka ndipo wofalitsa aike ndalamazo mu envelopu ya zopereka. Wofalitsayo ayamikire choperekacho ndipo anene kuti adzabweranso kudzasiya magazini otsatira.
Nyimbo Na. 201 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 28
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wakumunda a July. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya July 15 ndi Galamukani! ya July 8 m’gawo la mpingo wanu. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, mugaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti mufotokoza za magazini imodzi yokha.
Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ngati nkhani yokambirana ndi omvetsera ndi mkulu woyenerera. Fotokozani udindo wa woyang’anira utumiki ndi atumiki otumikira wosamalira mabuku ndi magazini.
Mph. 20: “Kuvala Moyenera Kumasonyeza kuti Tikulemekeza Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu. Gwiritsani ntchito mafunso amene alembedwawo. Ndime zonse ziŵerengedwe mokweza ndi mbale yemwe amaŵerenga bwino.
Nyimbo Na. 36 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 4
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene mungagaŵire Nsanja ya Olonda ya August1 ndi Galamukani! ya July 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, mugaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti mufotokoza za magazini imodzi yokha. M’chitsanzo chimodzi, musonyeze wofalitsayo akulalikira mwamwayi.
Mph. 20: “Ulaliki Wagulu Umasangalatsa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime 3, mutchulepo mfundo zochokera mu Bokosi la Mafunso la mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2001. Mwachidule funsani mafunso woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo. M’funseni zimene wakonza zokhudza utumiki wakumunda m’phunziro la buku lake ndi mmene gululo limapindulira chifukwa cholalikira limodzi.
Mph. 15: “Olumala Komabe Obala Zipatso.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Tchulani mfundo zosonyeza mmene ena angathandizire zotengedwa mu Galamukani! ya September 8, 1990 masamba 29 mpaka 30, pansi pa kamutu kakuti “Kodi Nchiyani Chingachitidwe?”
Nyimbo Na. 49 ndi pemphero lomaliza.