Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 25, 2003. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 7 mpaka August 25, 2003. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi timapeza mapindu otani tikamayang’ana omvetsera pamene tili mu utumiki? [be-CN tsa. 125 ndime 1-2; tsa. 125 bokosi]
2. Kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni ngati mumachita mantha musanalowe mu utumiki? [be-CN tsa. 128 ndime 4-5]
3. Kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni kuti mulankhule mwachibadwa ndiponso mokambirana pamene mukukamba nkhani papulatifomu? [be-CN tsa. 129 ndime 2; tsa. 129 bokosi]
4. Kodi mfundo zopezeka pa Levitiko 16:4, 24, 26, 28; Yohane 13:10 ndi Chivumbulutso 19:8 ziyenera kutikhudza motani pa kaonekedwe kathu, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? [be-CN tsa. 131 ndime 3; tsa. 131 bokosi]
5. Fotokozani munthu amene ndi wodzichepetsa ndiponso ‘wodziletsa.’ (1 Tim. 2:9, 10) [be-CN tsa. 132 ndime 1]
NKHANI NA. 1
6. Ngakhale kuti Akristu ayenera kukhala ololerana, n’chiyani chimene sayenera kulolera pakati pawo? (Akol. 3:13) [w01-CN 7/15 tsa. 22 ndime 7-8]
7. Zoona kapena Zonama: Mbewu ya mpiru ndi yaying’ono kwambiri kuposa mbewu zonse. (Mat. 13:31, 32) Fotokozani. [gt-CN mutu. 43 ndime. 5-6]
8. Kodi n’cholinga chabwino koposa chiti chimene tiyenera kuŵerengera Mawu a Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani kukhala ndi malingaliro amenewo n’kofunika? [be-CN tsa. 24 ndime 1]
9. Kodi munthu wanzeru ‘amakundika zomwe amadziŵa’ motani? (Miy. 10:14) [w01-CN 7/15 tsa. 27 ndime 4-5]
10. N’chifukwa chiyani zizoloŵezi zabwino za Yobu n’zochititsa chidwi? (Yobu 1:1, 8; 2:3) [w01-CN 8/1 tsa. 20 ndime 4]
KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi a m’bungwe lolamulira anakhala bwanji ndi “mtima umodzi” kuti okhulupirira Akunja sanafunikire kudulidwa kuti apulumutsidwe? (Mac. 15:25)
12. N’chifukwa chiyani bungwe lolamulira linauza Paulo kuchita ina ya miyambo ya Chilamulo cha Mose pamene Chilamulocho chinali chitathetsedwa ndi Yehova? (Mac. 21:20-26) [it-1 tsa. 481 ndime 3; it-2 tsa. 1163 ndime 6–tsa. 1164 ndime 1]
13. Kodi ndi milandu iti yabodza imene anaimba mtumwi Paulo imene ikutikumbutsa nkhani zabodza zimene anthu anena zokhudza Mboni za Yehova m’zaka za posachedwapa? (Mac. 24:5, 6) [w01-CN 12/15 tsa. 22 ndime 7–tsa. 23 ndime. 2]
14. Kodi Paulo anatisiira chitsanzo motani monga wolengeza Ufumu ngakhale pamene anali wandende m’nyumba kwa zaka ziŵiri? (Mac. 28:30, 31)
15. Kodi “maulamuliro a akulu” ali mbali ya “choikika ndi Mulungu” m’njira yotani, ndipo zimenezi ziyenera kuwakhudza bwanji Akristu? (Aroma 13:1, 2) [w00-CN 8/1 tsa. 4 ndime. 5]