Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu August: Gwiritsani ntchito bulosha lakuti Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? Mabuloshaŵa akatha pa mpingopo, mungagwiritse ntchito bulosha lina lililonse. Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo kwa anthu amene asonyeza chidwi. September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja kapena Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. October: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji kwa anthu amene asonyeza chidwi ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. November: Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Mukapeza eninyumba amene ali nalo kale buku ndi bulosha limeneli, agaŵireni bulosha lina lililonse.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa September 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Akatha kuŵerengerako, mukalengeze kumpingo mutamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Kuŵerengera mabuku ndi magazini onse amene ali m’sitoko kumene kumachitika pachaka kuchitike pa August 31, 2003 kapena pakangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Kuŵerengera kumeneku n’kofanana ndi kuŵerengera mabuku kumene mtumiki wa mabuku amachita mwezi uliwonse, ndipo ziŵerengero zonse zilembedwe pafomu ya Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chiŵerengero chonse cha magazini amene alipo mungachipeze kwa mtumiki wa magazini. Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chonde tumizani pepala loyamba ku ofesi ya nthambi pasanafike pa September 6. Sungani pepala lachiŵiri m’faelo yanu. Pepala lachitatulo mungaligwiritse ntchito ngati poŵonkhetsera. Mlembi adzayang’anire kuŵerengeraku. Iye ndi woyang’anira wotsogolera adzasaine fomuyi.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Kalendala ya Mboni za Yehova ya 2004, Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2004, ndi mabuku a 2004 Yearbook of Jehovah’s Witnesses pa oda yawo ya mabuku yotsatira. Ma Yearbook adzakhala m’Chingelezi basi. Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku kadzapezeka m’Chicheŵa, m’Chingelezi, ndi m’Chitumbuka pamene Kalendala idzapezeka m’Chicheŵa ndi m’Chingelezi.
◼ Tinasangalala kwambiri kulandira posachedwapa Nsanja ya Olonda ya zilembo zazikulu. Komabe, mipingo ina ikuoneka kuti ikuoda magazini ambiri otereŵa kuposa mmene ziyenera kukhalira. Tikufuna tikumbutse mipingo kuti Nsanja ya Olonda ya zilembo zazikuluyi si yoti iloŵe m’malo mwa Nsanja ya Olonda imene timalandira nthaŵi zonse ndiponso anaikonzera makamaka anthu amene amavutika kuona. Nthaŵi zonse, zingakhale bwino kuti ofalitsa ndi anthu ena onse amene alibe vuto la maso azilandira magazini ya nthaŵi zonse, osati ya zilembo zazikulu, chifukwa m’magazini imeneyi mumakhalanso nkhani zina zolimbitsa chikhulupiriro kuwonjezera pa nkhani zophunzira. Ndiponso, zithunzi, zimene nthaŵi zambiri zimaphunzitsa, sizipezeka m’magazini ya zilembo zazikulu.